Banja la Yehova
Daunilodi:
1. M’dzikoli n’kovuta kupeza
Bwenzi labwinodi—bwenzi lapamtima.
N’nali kufuna-funa angakhaledi
Banja kwa ine—indedi mabwenzi.
2. Napeza banja lacikondi.
Naŵapezadi mabwenzi, ndipo anikonda.
Maloto anga lomba athekadi—nisangalala.
Napeza banja la M’lungu.
(BILIJI)
Napeza ’bale na alongo acikonditu.
Nalipezadi banja logwilizana.
Ndifedi osiyana koma tikondana.
Ndife okondwa kukhala m’banja ili.
3. Cikondi cathu n’colimbadi.
Timasangalaladi na ubale wathu.
Tili pa ubale wopambanadi.
Ndife okondwa kukhala m’banja ili.
(BILIJI)
Ndifedi osiyana, koma tikondana.
Ndife okondwa kukhala m’banja ili.
4. M’lungu afuna tikhale mabwenzi
Mabwenzi enieni—ogwilizanadi.
Tidzakhaladi na moyo wosatha, Tidzakhalabe
M’banjali la Yehova.
M’banja—m’banjali la Yehova,
M’banjali,
M’banjali.