Nyimbo 148
Munapeleka Mwana Wanu Wobadwa Yekha
Daunilodi
(Yohane 15:13)
-
Yehova, Atate,
tikuyamikani
Potuma Yesu
kuti atifele.
Timadzipeleka
na mtima umodzi.
Tidziŵitse ena,
cifunilo canu!
(KOLASI)
Mwana wanu Yesu,
munamupeleka.
Tidzakutamandani,
potipatsa mwana wanu.
-
Poona cifundo
na kukoma mtima,
Tifuna kukhala
mabwenzi anu.
Yopambana zonse
ni mphatso ya Yesu.
Anadzipeleka
cifukwa ca ife.
(KOLASI)
Mwana wanu Yesu,
munamupeleka.
Tidzakutamandani,
potipatsa mwana wanu.
KUTSILIZITSA
Yehova, Atate, tikuyamikani.
Cifukwa copeleka mwana wanu Yesu.
(Onaninso Yohane 3:16; 1 Yohane 4:9.)