Russia Athila Nkhondo Ukraine
M’mamaŵa pa February 24, 2022, dziko la Russia linayamba nkhondo yofuna kulanda dziko la Ukraine. Atsogoleli a maiko anayesetsa kuti nkhondoyo isacitike, koma sizinaphule kanthu. Kodi dziko lonse lingakhudzidwe motani na nkhondo imeneyi? Posacedwapa, kalembela wamkulu wa bungwe la United Nations, António Guterres, anakamba kuti: “N’zocititsa mantha kungoganizila zotsatilapo zake. Padzacitika zoopsa zosaneneka kwa anthuwo, dziko lawo lidzasakazidwa momvetsa cisoni, ndipo citetezo ca maiko a ku Europe komanso dziko lonse lapansi cidzagwedezeka.”
Kodi zocitika zotelezi zitanthauza ciyani malinga n’kunena kwa Baibo?
Yesu Khristu ananenelatu za nthawi pamene “mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Baibo imaonetsa bwino lomwe kuti nkhondo zimene zikucitikazi zikukwanilitsa ulosi wa Yesu. Onani zimenezi poŵelenga nkhani yakuti “Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti ‘Nthawi ya Mapeto’ N’chiyani?”
M’buku la Chivumbulutso, nkhondo akuifotokoza ngati munthu wokwela “hachi yofiila ngati moto,” amene ‘akucotsa mtendele padziko lapansi.’ (Chivumbulutso 6:4) Kuti muone mmene nkhondo zikucitika masiku zikukwanilitsila ulosi umenewu, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?”
Buku la Danieli linanenelatu za cidani ca pakati pa “mfumu ya kumpoto” na “mfumu ya kum’mwela.” (Danieli 11:25-45) Kuti muone cimene tinganenele kuti Russia pamodzi na maiko ogwilizana naye ndiwo mfumu ya kumpoto, tambani vidiyo yakuti Kukwanilitsika kwa Maulosi a pa Danieli Caputala 11. a
Buku la Chivumbulutso limakambanso za “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Nkhondo imeneyo si yapakati pa maiko ngati zimene zikucitikazi ayi. Kuti mumve zambili zokhudza nkhondo yam’tsogolo imeneyo, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo ya Aramagedo N’ciyani?”
N’cifukwa ciyani muyenela kukhala na cidalilo ca tsogolo labwino?
Baibo imakamba kuti Mulungu ‘adzaletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.’ (Salimo 46:9) Ŵelengani nkhani yakuti “Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo” kuti mumve za tsogolo limene Mulungu akutilonjeza.
Yesu anaphunzitsa otsatila ake kuti azipemphelela kubwela kwa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 6:9, 10) Ufumu umenewo ni boma lakumwamba limene lidzakwanilitsa cifunilo ca Mulungu pano padziko lapansi. Ndipo cifunilo ca Mulunguco cimaphatikizapo kubwela kwa mtendele wa padziko lonse. Kuti mudziŵe mmene Ufumu wa Mulungu ungakupindulileni, tambani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
Mu dziko la Ukraine muli Mboni za Yehova zopitilila 129,000. Mofanana na Mboni zinzawo m’dziko lililonse, iwo amatengela citsanzo ca Yesu posakhalila mbali m’nkhani zandale. Ndipo amakanilatu kumenya nawo nkhondo. (Yohane 18:36) Zungulile dziko lapansi, a Mboni za Yehova akupitilizabe kulengeza “uthenga wabwino wa Ufumu,” cifukwa ndiwo wokha udzathetsa mavuto a anthu, kuphatikizapo nkhondo. (Mateyu 24:14) Tidziŵitseni conde, ngati mukufuna kumva zambili za uthenga wa m’Baibo wa tsogolo lowala.
a Kuti muunikilidwe zambili pa ulosi umenewu, ŵelengani nkhani yakuti “‘Mfumu ya Kumpoto’ M’nthawi Yamapeto,” komanso yakuti “Kodi ‘Mfumu ya Kumpoto’ Ndani Masiku Ano?”