Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KHALANI MASO!

Kutentha Kodetsa Nkhawa Padziko Lonse—Kodi Baibo Ikambapo Ciyani

Kutentha Kodetsa Nkhawa Padziko Lonse—Kodi Baibo Ikambapo Ciyani

 M’mwezi wa July 2022, m’madela osiyana-osiyana padziko lapansi kunatentha koopsa. Nawa malipoti ake:

  •   “Kaciŵili tsopano m’mwezi uno, odziŵa zanyengo m’dziko la China akucenjeza kuti pafupifupi mizinda yake 70 idzatentha koopsa.” Malinga n’kunena kwa CNN Wire news ya pa July 25, 2022.

  •   “Cifukwa ca kutentha kwa nyengo kodabwitsa m’maiko ambili ku Europe, m’nkhalango zoculuka mukubuka moto wolilima koopsa, wofalikila mofulumila, komanso wowononga kwambili.” Malinga n’kunena kwa The Guardian ya July 17, 2022.

  •   “Pa Sondo mizinda yoculuka m’dziko la America inatentha kwambili kuposa na kale lonse.” Malinga n’kunena kwa The new York times ya pa July 24, 2022.

 Kodi zonsezi zikutanthauza ciyani? Kodi tsiku lina zinthu zidzafika poipa moti n’kusathekanso kukhalapo padziko lapansi? Nanga Baibo ikambapo ciyani?

Kodi kutentha kwa nyengo kukukwanilitsa ulosi wa m’Baibo?

 Inde kukutelo. Kutentha kwa nyengo padziko lonse kukugwilizana na zimene Baibo inakambilatu zokhudza nthawi yathu ino. Mwacitsanzo, Yesu ananenelatu kuti kudzaoneka “zoopsa” komanso “zizindikilo zodabwitsa.” (Luka 21:11; Baibulo la Dziko Latsopano). Kutentha kwa nyengo padziko lonse komwe kukukwelela-kwelela kwapatsa anthu oculuka nkhawa yakuti anthu adzafika poliwonongelatu dziko lapansi.

Kodi dziko lapansi lidzafika poti n’zosathekanso anthu kukhalapo?

 Ayi. Mulungu analenga dziko lapansi monga mudzi wacikhalile wa anthu. (Masalimo 115:16; Mlaliki 1:4) Conco, n’zosatheka kuti iye angalole anthu kuliwononga dziko lapansi. M’malo mwake, iye analonjeza kuti “idzafika nthawi yowononga amene akuwononga dziko lapansi.”—Chivumbulutso 11:18.

 Taonani maulosi aŵili okha oonetsa zinanso zimene Mulungu analonjeza:

  •   “Cipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dela lacipululu lidzakondwa ndipo lidzacita maluŵa n’kukhala lokongola ngati duŵa la safironi.” (Yesaya 35:1) N’zosatheka kuti Mulungu akalole dziko lapansi kusandutsidwa cipululu copanda zamoyo. M’malo mwake, adzakonzanso bwino lomwe mbali zonse zowonongedwa za dziko lapansi.

  •   “Inu mwatembenukila dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zoculuka.” (Salimo 65:9) Mulungu akadzalidalitsa dziko lapansi, lidzakhala paladaiso wokongola.

 Kuti mudziŵe zambili za mmene kusintha kwa nyengo kukwanilitsila ulosi wa m’Baibo, ŵelengani nkhani yakuti “Zomwe Baibulo Limanena pa Nkhani ya Kusintha kwa Nyengo Komanso Tsogolo Lathu.”

 Kuti mudziŵe zambili pa lonjezo la m’Baibo la kukonzanso malo a dziko lapansi, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?