NKHANI YA PACIKUTO—AMUNA ANAYI OKWELA PA MAHOSI—KODI AMAKUKHUDZANI BWANJI?
Mmene Amuna Anayi Okwela pa Mahosi Amakukhudzilani
Mwadzidzidzi, mahosi akutulukila cothamanga, apo mgugu wa ziboda uli dididi! Baibo imafotokoza momveka bwino masomphenya a mahosi anayi amphamvu ndi okwelapo ake cakuti tikamaŵelenga, timakhala ngati tikuwaona m’maganizo mwathu. Hosi yoyamba ni yoyela, ndipo wokwelapo wake ni mfumu yoikidwa catsopano yaulemelelo. Yotsatila pambuyo ni hosi yofiila monga moto, ndipo wokwelapo wake akucotsa mtendele padziko lonse. Ndiyeno, pakutsatila hosi yacitatu yakuda bii. Wokwelapo wake wanyamula sikelo pamene uthenga wacisoni wokamba za kucepa kwa cakudya ukulengezedwa. Hosi yacinayi ni yotuŵa, ndipo n’cizindikilo ca matenda ndi zinthu zina zakupha. Wokwelapo wake ni Imfa. Ndipo Manda a anthu onse akutsatila pafupi, kutenga miyoyo ya anthu ambili.—Chivumbulutso 6:1-8.
“N’nacita mantha kwambili n’taŵelenga koyamba za amuna anayi okwela pa mahosi. N’naona monga Tsiku la Ciweluzo lafika, ndi kuti siningapulumuke cifukwa n’nali wosakonzeka.”—Crystal.
“N’nacita cidwi maningi na mahosi anayi a mitundu yosiyana-siyana ndi okwelapo ake. N’tamvetsetsa tanthauzo la masomphenya amenewo, n’nadziŵa cifukwa cake okwelapo ake akufotokozedwa mwa njila imeneyi.”—Ed.
Kodi inunso mumamvela monga mmene Crystal anamvelela ataŵelenga za amuna anayi okwela pa mahosi a m’buku la Chivumbulutso? Kapena mumamvela monga mmene Ed anamvelela? Mulimonse mmene mumamvelela, nkhani ya amuna anayi okwela pa mahosi ni imodzi mwa nkhani zodziŵika kwambili za m’buku yotsiliza ya m’Baibo ya Chivumbulutso. Kodi mudziŵa kuti mungapindule mukamvetsetsa tanthauzo la masomphenya amenewa? Nanga mungapindule bwanji? Mulungu analonjeza kuti mudzapeza cimwemwe ceni-ceni ngati muŵelenga, muphunzila, na kuseŵenzetsa zolembedwa m’buku ya ulosi imeneyi.—Chivumbulutso 1:1-3.
Ngakhale kuti ena amacita mantha ndi masomphenya a amuna anayi okwela pa mahosi, sikuti colinga cake ni kukuwopsezani. Anthu ofika m’mamiliyoni apeza kuti masomphenya amenewa amalimbitsa cikhulupililo cawo, na kuwapatsa ciyembekezo ca tsogolo labwino. Na imwe angakuthandizeni cimodzi-modzi. Conde ŵelengani nkhani yotsatila.