Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi N’kuphonya Cabe pa Kamvedwe?

Kodi N’kuphonya Cabe pa Kamvedwe?

Kamtsikana kena kanaona utsi wocokela pa fakitale inayake ukukwela m’mwamba ndipo unayamba kuoneka monga mitambo. Iye anayamba kuganiza kuti nchito ya pa fakitaleyo ni kupanga mitambo. Maganizo olakwika amene mwanayo anali nawo ndi nkhani yaing’ono ndiponso yoseketsa. Koma pa zinthu zina, kuphonya m’kamvedwe kungakhudze kwambili umoyo wathu. Mwacitsanzo, ngati sitinamvetsetse mau olembedwa pa botolo la mankhwala, tingakumane na mavuto aakulu.

Kuphonya pa kamvedwe ka zinthu zauzimu n’koopsa ngako. Mwacitsanzo, nthawi ina anthu ena sanamvetsetse zimene Yesu anali kuwaphunzitsa. (Yohane 6:48-68) M’malo mwakuti aphunzile zowonjezeleka, iwo anakana kumvetsela zonse zimene Yesu anali kuwaphunzitsa. Anthu amenewo anataya mwayi waukulu.

Kodi mumakonda kuŵelenga Baibo kuti mupeze malangizo othandiza? Ngati n’conco, mucita bwino. Koma kodi n’zotheka kuphonya kamvedwe pa zinthu zina zimene mumaŵelenga? Anthu ambili zawacitikilapo. Onani mfundo zitatu za m’Baibo zimene anthu ambili samvetsetsa.

  • Anthu ena samvetsetsa lamulo la m’Baibo lakuti: “Opa Mulungu woona.” Iwo amaganiza kuti Mulungu afuna kuti tizicita naye mantha. (Mlaliki 12:13) Koma Mulungu safuna kuti anthu amene amam’lambila azicita naye mantha. Iye amati: “Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.” (Yesaya 41:10) Conco, kuopa Mulungu kumatanthauza kukhala ndi mantha aulemu ndi kumulemekeza kwambili.

  • Kodi dziko lidzashokewa na moto?

    Anthu ena samvetsetsa mau ouzilidwa akuti: “Ciliconse cili ndi nthawi yake, . . . pali nthawi yobadwa ndi nthawi ya kufa.” Iwo amakamba kuti mau amenewa aonetsa kuti Mulungu anaikilatu nthawi imene munthu aliyense adzafa. (Mlaliki 3:1, 2) Komabe, lemba limeneli limakamba cabe za mmene moyo wathu ulili, ndipo limaonetsa kuti palibe angathawe imfa. Mau a Mulungu amakambanso kuti zocita zathu zingacititse kuti tikhale na moyo wautali kapena waufupi. Mwacitsanzo, Baibo imati: “Kuopa Yehova kudzawonjezela masiku.” (Miyambo 10:27; Salimo 90:10; Yesaya 55:3) Kodi kuopa Mulungu kungawonjezele bwanji moyo wa munthu? Mwacitsanzo, kuopa Mulungu kumatilimbikitsa kupewa makhalidwe oipa monga ucakolwa ndi ciwelewele.—1 Akorinto 6:9, 10.

  • Ena amaganiza kuti pamene Baibo ikamba kuti kumwamba ndi dziko lapansi “azisungila moto,” itanthauza kumwamba kweni-kweni ndi dziko lapansi leni-leni. Iwo amakhulupilila kuti Mulungu adzawononga dziko lapansi leni-leni. (2 Petulo 3:7) Koma Mulungu analonjeza kuti sadzalola kuti dziko lapansi liwonongedwe. Baibo imati Mulungu ‘anakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.’ (Salimo 104:5; Yesaya 45:18) Conco, dziko limene lidzawonongedwa si dziko lapansi leni-leni. Koma ndi anthu oipa amene adzawonongedwa kothelatu ngati mmene zinthu zimawonongekela zikashokewa na moto. Koma pamene Baibo ikamba za kumwamba kweni-kweni, imatanthauza mumlengalenga, kumwamba kumene kuli nyenyezi, kapena malo okhala Mulungu. Zinthu zonsezi sizidzawonongedwa.

N’CIFUKWA CIANI NTHAWI ZINA ANTHU SAIMVETSETSA BAIBO?

Monga mmene taonela zitsanzo pamwambapa, anthu ambili samvetsetsa mavesi ena amene amaŵelenga m’Baibo. Koma n’cifukwa ciani Mulungu amalola zimenezi kucitika? Ena angakambe kuti: ‘Mulungu ni wanzelu kwambili ndipo amadziŵa zonse cakuti akanakwanitsa kulemba Baibo m’njila yosavuta kumva kuti aliyense azitha kuimvetsetsa. Nanga n’cifukwa ciani sanacite zimenezo?’ Onani zinthu zitatu zimene zimapangitsa anthu kusamvetsetsa Baibo.

  1. Baibo inapangidwa m’njila yakuti anthu odzicepetsa ndi ofunitsitsa kuiphunzila azitha kuimvetsetsa. Pokamba ndi Atate ake, Yesu anati: “Atate ndikukutamandani pamaso pa onse, inu Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, cifukwa zinthu izi mwazibisa kwa anzelu ndi ozama m’maphunzilo, koma mwaziulula kwa tiana.” (Luka 10:21) Baibo inalembedwa m’njila yakuti anthu okhawo amene ali na maganizo oyenela azitha kumvetsetsa uthenga wake. Kaŵili-kaŵili anthu a khalidwe lonyada saimvetsetsa Baibo, ndipo khalidwe limeneli n’lofala pakati pa anthu “anzelu ndi ozama m’maphunzilo.” Koma anthu amene amaŵelenga Baibo na maganizo odzicepetsa, ofunitsitsa kuphunzila ngati ‘tuŵana,’ amadalitsidwa mwa kumvetsetsa uthenga wa Mulungu. Conco, tingathe kuona kuti Mulungu anaipanga mwanzelu kwambili Baibo.

  2. Baibo inalembedwela anthu oona mtima amene amadalila thandizo la Mulungu kuti aimvetsetse. Yesu anaonetsa kuti anthu afunika thandizo kuti amvetsetse zimene iye anali kuphunzitsa. Kodi iwo akanalandila bwanji thandizo limenelo? Yesu anafotokoza kuti: “Mthandizi, amene ndi mzimu woyela, amene Atate wanga adzatumiza m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse.” (Yohane 14:26) Conco, Mulungu amapeleka mzimu woyela, mphamvu yake yogwila nchito, kuti uthandize anthu kumvetsetsa zimene amaŵelenga m’Baibo. Komabe, Mulungu sapeleka mzimu wake kwa anthu amene sadalila thandizo lake. Pa cifukwa cimeneci, iwo amalephela kuimvetsetsa. Mzimu woyela umalimbikitsanso Akhiristu odziŵa zambili kuti athandize anthu amene afuna kumvetsetsa Baibo.—Machitidwe 8:26-35.

  3. Pali malemba ena amene anthu sangawamvetsetse mpaka nthawi yoyenelela itakwana. Mwacitsanzo, mneneli Danieli anauzidwa kulemba uthenga wina-wake wokamba za mtsogolo. Mngelo anamuuza kuti: “Danieli, sunga mauwa mwacinsinsi ndipo utseke ndi kumata bukuli kufikila nthawi yamapeto.” Kwa zaka zambili, anthu oculuka aŵelengapo buku la Danieli, koma sanalimvetsetse. Ndipo ngakhale Danieli iye mwini sanamvetsetse zimene analemba. Modzicepetsa, iye anati: “Ndinamva zimene ananenazo, koma sindinadziŵe tanthauzo lake.” M’kupita kwa nthawi, anthu anakwanitsa kumvetsetsa maulosi a Mulungu olembedwa m’buku la Danieli, koma pa nthawi yoyenelela imene Mulungu anasankha. Mngelo anafotokoza kuti: “Pita Danieli, pakuti mawuwa asungidwa mwacinsinsi ndipo atsekedwa ndi kumatidwa kufikila nthawi yamapeto.” Ndani anali kudzamvetsetsa uthenga wa Mulungu? Baibo imati: “Palibe munthu woipa aliyense amene adzamvetsetse mau amenewa, koma anthu ozindikila adzawamvetsetsa.” (Danieli 12:4, 8-10) Conco, Mulungu saulula tanthauzo la mauthenga ena a m’Baibo mpaka nthawi yake yoyenelela itakwana.

Kodi Mboni za Yehova zinaphonyapo kamvedwe ka malemba ena cifukwa cakuti nthawi yoyenela yakuti Mulungu aulule tanthauzo lake inali isanakwane? Inde. Koma pamene Mulungu anawathandiza kumvetsetsa tanthauzo la malembawo, iwo anasintha maganizo olakwikawo. Mwa kucita zimenezi, a Mboni amatsatila citsanzo ca atumwi a Khiristu, amene modzicepetsa anasintha maganizo awo pamene Yesu anawawongolela.—Machitidwe 1:6, 7.

Maganizo olakwika a mwana amene tamuchula kuciyambi kwa nkhani ino, okhudza kumene kumacokela mitambo, ni nkhani yaing’ono. Komabe, zimene Baibo imaphunzitsa ni nkhani yofunika kwambili kwa inu. Popeza kuti uthenga wa m’Baibo ni wofunika kwambili, si bwino kudalila cabe nzelu zathu kuti timvetsetse zimene timaŵelenga m’Baibo. M’malo mwake, tifunika kupempha thandizo. Conco, pemphani thandizo kwa anthu amene amaŵelenga Baibo ndi maganizo odzicepetsa, amene amadalila mzimu wa Mulungu kuti aimvetsetse, komanso amene amakhulupilila kuti tili m’nthawi imene Mulungu afuna kuti anthu amvetsetse Baibo. Musazengeleze kuonana ndi Mboni za Yehova kapena kuŵelenga nkhani za pa webusaiti yawo ya jw.org. Baibo imalonjeza kuti: “Ukaitana kumvetsa zinthu. . . , udzamudziŵadi Mulungu.”—Miyambo 2:3-5.