Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Wokana Kristu Ndani?

Kodi Wokana Kristu Ndani?

Filimu inayake yoopsa yaposacedwapa inali ndi mutu wakuti Wokana Kristu.

Gulu lina la oimba nyimbo linatulutsa cimbale ca nyimbo zochuka cimene anacipatsa dzina lakuti Wokana Kristu.

Katswili wina wa zamaphunzilo wa m’zaka za m’ma 1900, dzina lake Friedrich Nietzsche, anacha imodzi mwa nchito zake kuti Wokana Kristu.

Mafumu ndi olamulila a m’zaka za m’ma 1500 anali kuchula adani ao kuti okana Kristu.

Martin Luther mtsogoleli wa gulu lotsutsa Cikatolika ku German anacha apapa Acikatolika kuti okana Kristu.

KWA nthawi yaitali, anthu akhala akugwilitsila nchito mau akuti “wokana Kristu” pa zinthu zosiyanasiyana monga mafilimu ndiponso kwa anthu olamulila. Koma kodi wokana Kristu ndani? Nanga mau amenewa akutikhudza bwanji masiku ano? Zingakhale zothandiza kuŵelenga Baibulo kuti tidziŵe okana Kristu amenewa, ndipo mauwa amapezekamo nthawi zokwanila 5.

WOKANA KRISTU AONEKELA

Pa anthu amene analemba Baibulo, ndi mtumwi Yohane cabe amene anachula mau akuti “wokana Kristu.” Kodi iye anafotokoza kuti wokana Kristu ndani? Onani mau a m’kalata yake yoyamba yodziŵika ndi dzina lake. Mauwo amati: “Ana inu, ino ndi nthawi yakumapeto, ndipo monga mmene munamvela kuti wokana Kristu akubwela, ngakhale panopa alipo okana Kristu ambili. Cifukwa ca zimenezi timadziŵa kuti ino ndi nthawi yakumapeto. Amenewo anacoka pakati pathu, koma sanali m’gulu lathu . . . Kodi wabodza angakhalenso ndani, kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Kristu? Ameneyu ndiye wokana Kristu, amene amakana Atate ndi Mwana.”—1 Yohane 2:18, 19, 22.

Mtumwi Yohane anatanthauza kuti okana Kristu ndi anthu amene mwadala amafalitsa mabodza acipembedzo onena za Yesu Kristu ndi ziphunzitso zake

Kodi tiphunzilapo ciani pa mau amenewa? Yohane anakamba mau akuti “okana Kristu ambili,” kuonetsa kuti wokana Kristu si munthu mmodzi koma ndi gulu la anthu. Anthu kapena magulu a anthu amene amapanga gulu la okana Kristu amafalitsa mabodza. Iwo amakana kuti Yesu ndi Kristu kapena kuti Mesiya ndipo amasokoneza ubale umene ulipo pakati pa Mulungu ndi Mwana Wake, Yesu Kristu. Anthu amene ali m’gulu la okana Kristu amadzicha kuti ndiwo Kristu kapena omuimila. Koma popeza io “anacoka pakati pathu,” anapatuka pa ziphunzitso zolondola za m’Baibulo. Kuonjezela pamenepo, gululi linalipo pamene Yohane anali kulemba kalata yake mu “nthawi yakumapeto,” pamene atumwi anali kutha.

Ndi ciani cina cimene Yohane analemba cokhudza wokana Kristu? Iye anati: “Kuti tidziŵe ngati mau ali ouzilidwa ndiponso ocokela kwa Mulungu, timadziŵila izi: Mauwo amavomeleza zoti Yesu Kristu anabwela monga munthu. Koma mau alionse ouzilidwa amene amatsutsa zoti Yesu anabwela monga munthu, amenewo si ocokela kwa Mulungu, ndipo ndi ouzilidwa ndi wokana Kristu amene munamva kuti akubwela, ndipo tsopano ali kale m’dziko.” (1 Yohane 4:2, 3) Apa n’zoonekelatu kuti Yohane anatanthauza kuti okana Kristu ndi anthu amene mwadala amafalitsa mabodza acipembedzo onena za Yesu Kristu ndi ziphunzitso zake.

“ANENELI ONYENGA” NDI “MUNTHU WOSAMVELA MALAMULO”

Yohane asanalembe za okana Kristu, Yesu anacenjeza otsatila ake kuti: “Cenjelani ndi aneneli onyenga amene amabwela kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwao ali mimbulu yolusa.” (Mateyu 7:15) Nayenso mtumwi Paulo anacenjeza Akristu a ku Tesalonika kuti: “Wina asakunyengeni pa nkhani imeneyi m’njila iliyonse. Pakuti tsikulo [tsiku la Yehova] silidzayamba kufika mpatuko usanacitike, ndiponso asanaonekele munthu wosamvela malamulo, amene ndiye mwana wa cionongeko.”—2 Atesalonika 2:3.

Yesu anacenjeza kuti aneneli onyenga ‘adzabwela atavala ngati nkhosa’

M’nthawi ya atumwi, aneneli onyenga ndi anthu ampatuko anali kale pa nchito yofooketsa mpingo wacikristu. Pamene Paulo anakamba mau akuti “okana Kristu” anatanthauza anthu onse amene amanena mabodza okhudza Yesu Kristu ndi ziphunzitso zake. Iye anaonetsanso maganizo a Yehova kwa anthuwo pamene anati, “mwana wa cionongeko.”

CENJELANI NDI ZOCITA ZA OKANA KRISTU

Nanga bwanji masiku ano? Anthu amene amapanga gulu la okana Kristu amatsutsa Kristu ndi ziphunzitso zake. Mwadala io amafalitsa mabodza n’colinga cofuna kulepheletsa anthu kudziŵa Atate, Yehova Mulungu, ndi Mwana Wake, Yesu Kristu. Tili ndi zifukwa zabwino zokhalila ocenjela ku mabodza otelo a zipembedzo. Tiyeni tione zitsanzo ziŵili zotsatilazi.

Kwa zaka zambili, machalichi akhala akuphunzitsa ciphunzitso ca utatu, kuonetsa kuti Atate ndi Mwana ndi cinthu cimodzi cogwilana. Conco okana Kristu aphimba coonadi conena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Ciphunzitso ca utatu calepheletsa anthu oona mtima kutengela citsanzo ca Yesu Kristu, ndi kuti ayandikile Mulungu, monga mmene Baibulo limatilimbikitsila.—1 Akorinto 11:1; Yakobo 4:8.

Machalichi aonjezela msokonezo umenewu mwa kulimbikitsa anthu kugwilitsila nchito Mabaibulo amene dzina la Mulungu lakuti Yehova lacotsedwamo. Iwo acita zimenezi ngakhale kuti dzina la Mulungu limapezeka nthawi zokwanila 7,000 m’mipukutu yoyambilila ya Baibulo. Kodi zotsatilapo zake zakhala zotani? Zakhala zakuti coonadi conena za Mulungu caphimbidwilatu.

Komabe, kudziŵa dzina la Mulungu lakuti Yehova, kwathandiza anthu ambili a mitima yabwino kuyandikila Mulungu. Mwacitsanzo, Richard akukumbukila zimene anakambilana ndi Mboni za Yehova ziŵili. Iye anati: “Iwo anandionetsa dzina la Mulungu woona m’Baibulo, kuti ndi Yehova. Ndinakhudzidwa kwambili kudziŵa kuti Mulungu ali ndi dzina lake, cinthu cimene cikhalile sindinamvepo.” Conco kuyambila nthawiyo, iye anayamba kukhala ndi umoyo wogwilizana ndi mfundo za m’Baibulo ndi kucita zinthu zokondweletsa Yehova. Iye anaonjezelanso kuti: “Kudziŵa dzina la Mulungu kwandithandiza kukhala naye paubwenzi.”

Kwa zaka zambili, okana Kristu acititsa anthu mamiliyoni ambili kukhala mumdima wa kuuzimu. Koma kuphunzila Mau a Mulungu, Baibulo, kwatithandiza kudziŵa anthu okana Kristu ndipo tamasuka ku cinyengo ndi mabodza a zipembedzo.—Yohane 17:17.