NKHANI YA PACIKUTO | KODI IMFA NDI MAPETO A ZONSE?
Mphamvu ya Imfa
Imfa si nkhani yosangalatsa. Ndipo anthu ambili samakonda kukambitsilana za imfa. Koma imfa sithawika. Iyo ndi yamphamvu ndipo ululu wake ndi waukulu kwambili.
Palibe cimene tingacite kuti tikonzekele imfa ya makolo, mkazi, mwamuna kapena ya mwana wathu. Mavuto ena angacitike mwadzidzidzi, koma ena angatenge nthawi yaitali. Mulimonse mmene zingakhalile, ululu wa imfa sitingaupewe, ndipo zotsatilapo zake zimakhala zophweteka kwambili.
Antonio, amene atate wake anamwalila pangozi ya galimoto, anati: “Zimakhala ngati winawake wakhoma zitseko zonse za nyumba yanu ndi kutenga makiyi ndipo sungakwanitse kuloŵa m’nyumba. Zinthu zikafika apa umasoŵa cocita. Sungatsimikize kuti zimenezo zacitikadi cifukwa ndi zinthu zopanda cilungamo. Koma popeza zinthu zacitika kale, palibe cimene ungacite.”
A Dorothy naonso amene anataikilidwa wokondedwa wao, ndipo anakhala wamasiye ali ndi zaka 47, anafuna kupeza mayankho pa mafunso okhudza imfa. Pokhala m’phunzitsi wa ana m’cipembedzo cao, io anali kukhulupilila kuti imfa si mapeto a zonse. Komabe, sanali kudziŵa bwino zimene zimacitika munthu akamwalila. Tsiku lina, anafunsa bambo wa chalichi ca Anglican kuti: “Kodi cimacitika n’ciani munthu akamwalila?” Bamboyo anati: “Palibe amene adziŵa zimene zimacitika, tingofunika kuyembekezela.”
Kodi tifunika kukhalabe conco n’kumangoyembekezela? Kodi pali njila ina iliyonse imene tingadziŵile kaya imfa ndi mapeto a zonse?