Kuyankha Mafunso a M’Baibo
Kodi Mulungu angatikhululukile macimo athu?
Baibo imanena kuti tonse ndife ochimwa cifukwa coti tinatengela ucimo kwa kholo lathu Adamu. N’cifukwa cake nthawi zina timacita zinthu zoipa zimene pambuyo pake timakhumudwa nazo. Koma Yesu Khristu, yemwe ni Mwana wa Mulungu, anatifela kuti tizitha kukhululukidwa. Conco, nsembe yake ya dipo ni mphatso yocokela kwa Mulungu.—Ŵelengani Aroma 3:23, 24..
Anthu ena anacitapo macimo akulu-akulu ndipo amakayikila ngati Mulungu angawakhululukile. Koma cosangalatsa n’cakuti Mawu a Mulungu amatitsimikizila kuti: “Magazi a Yesu Mwana wake akutiyeletsa ku uchimo wonse.” (1 Yohane 1:7) Yehova ni wofunitsitsa kukhululukila aliyense, ngakhale atacita chimo lalikulu bwanji, pokhapokha ngati munthuyo walapa kucokela pansi pa mtima.—Ŵelengani Yesaya 1:18.
Kodi tiyenela kucita ciani kuti Mulungu azitikhululukila?
Ngati tikufuna kuti Yehova Mulungu azitikhululukila tifunika kuphunzila zambili za iyeyo zomwe zikuphatikizapo kudziŵa njila zake, malangizo ake komanso zimene amafuna kuti tizicita. (Yohane 17:3) Yehova amakhululukila aliyense amene amalapa macimo ake n’kusiya kucita zoipazo.—Ŵelengani Machitidwe 3:19.
Ndipo n’zotheka anthufe kumacita zinthu zokondweletsa Mulungu. Yehova amatimvetsa tikalakwitsa zinazake cifukwa iye ni wacifundo komanso ni wokoma mtima. Kudziŵa kuti Yehova ni wacifundo kuyenela kutilimbikitsa kufuna kuphunzila zimene tingacite kuti tizimukondweletsa.—Ŵelengani Salimo 103:13, 14.