Kodi Anthu Oyambilila Kulengedwa Anali Kukhaladi M’munda wa Edeni?
Kodi Anthu Oyambilila Kulengedwa Anali Kukhaladi M’munda wa Edeni?
TAYELEKEZANI kuti muli pamalo ena amaluwa na mitengo yambili. Palibe zinthu zosokoneza zilizonse, palibenso pilingu-pilingu wa anthu, phokoso la magalimoto ndiponso nyumba zamipanda. Malo okongolawa ni aakulu, ndipo palibe ciliconse cosokoneza mtendele. Kuwonjezela pamenepo mulibe nkhawa, simukudwala matenda aliwonse kapena kumva kupweteka kulikonse. Mukungosangalala na bata komanso kukongola kwa malowo.
Kulikonse kumene mukuyang’ana mukuona maluwa okongola a mitundu yosiyana-siyana. Mukuonanso mtsinje wa madzi oyela, mitengo yogudila bwino ndiponso udzu wobiliwila. Dzuŵa likuwala koma pali mithunzi yambili. Kukuwomba kamphepo kayaziyazi kamene kakubweletsa kafungo konunkhila bwino ka maluwa na mitengo. Mukumvanso kaphokoso kamasamba a mitengo, phokoso la madzi amene akugwela pamiyala ikulu-ikulu, kulila kwa mbalame ndiponso phokoso la tizilombo touluka. Mukaganizila zimenezi, kodi simukulakalaka mutamakhala malo ngati amenewa?
Padziko lonse anthu amakhulupilila kuti poyamba anthu anali kukhala malo ngati amenewa. Kwa zaka zambili Ayuda, Akhristu ndiponso Asilamu akhala akuphunzitsidwa kuti Mulungu anaika Adamu na Hava m’munda wa Edeni kuti azikhala mmenemo. Malinga na zimene Baibo imanena, iwo anali kukhala mwamtendele ndiponso mosangalala. Anali kukhala mwamtendele na nyama ndiponso na Mulungu, amene mokoma mtima anakonza zoti anthu amenewa akhale na moyo kwamuyaya pamalo abwino amenewa.—Genesis 2:15-24.
Ahindu nawo amanena nkhani zosiyana-siyana zokhudza mmene moyo m’paradaiso unalili. Abuda amakhulupilila kuti atsogoleli awo acipembedzo ochuka, amene amachedwa kuti Buda, amakhalapo zinthu padziko lapansi zikakhala kuti zili bwino kwambili ngati m’paradaiso. Komanso zipembedzo zambili za ku Africa kuno zimaphunzitsa nkhani zimene zimafanana kwambili na nkani ya Adamu na Hava.
Ndipotu mfundo yakuti kalelo kunali paradaiso imapezeka m’zipembedzo zambili ndiponso m’miyambo ya anthu ambili. Munthu wina analemba kuti: “Anthu ambili amakhulupilila kuti kale kwambili kunali paradaiso ndipo ciliconse pa nthawi imeneyo cinali bwino. Iwo amati anthu anali kukhala mwaufulu, mwamtendele, mosangalala ndiponso kunali ciliconse cimene munthu angafune. Kunalibe munthu woopseza mnzake, kunalibe kusamvana, kapena kukangana. . . . Cikhulupililo cimeneci cinacititsa kuti anthu kulikonse azilakalaka paradaiso ndiponso kuti aziyesetsa kupeza njila zopezelanso paradaiso ameneyo.”
Kodi n’kutheka kuti pali cimene cinayambitsa nkhani na ziphunzitso zonsezi? Kodi mwina “anthu kulikonse” amafuna paradaiso cifukwa cakuti poyamba analipodi? Kodi kale kwambili kunalidi munda wa Edeni ndiponso Adamu na Hava?
Anthu ena amatsutsa mfundo yakuti zimenezi ni zoona. Cifukwa ca kupita patsogolo kwa sayansi masiku ano, anthu ambili amaganiza kuti nkhani zimenezi ni nthano zongopeka, ndipo codabwitsa kwambili n’cakuti ena amene amakayikila zimenezi ni atsogoleli acipembedzo. Atsogoleliwa amacititsa anthu kuti asamakhulupilile kuti kunalidi munda wa Edeni. Amanena kuti malo amenewa kunalibe. Iwo amanenanso kuti nkhani imeneyi ni yongoyelekezela ndipo nthano kapenanso fanizo cabe.
Ni zoona kuti Baibo ili na nkhani zina zomwe ni mafanizo cabe, ndipo ochuka mwa mafanizo amenewo anawanena ni Yesu. Komabe Baibo imafotokoza nkhani ya mu Edeni osati ngati fanizo, koma ngati mbili yakale, yoti inacitikadi ndiponso ni yosavuta kumva. Cifukwa ngati zimenezi sizinacitikedi ndiye kuti nkhani zina zonse zimene zili m’Baibo nazonso sizinacitike, conco sitingazikhulupilile. Tiyeni tione cifukwa cake anthu ena amakayikila zakuti kunalidi munda wa Edeni, ndiponso tione ngati zifukwa zawozo zilidi zomveka. Kenako tikambilane cifukwa cake nkhani imeneyi ni yofunika kwa tonsefe.