Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yehova Ndi Mulungu Wacikondi

Yehova Ndi Mulungu Wacikondi

“Mulungu ndiye cikondi.”—1 YOHANE 4:8, 16.

NYIMBO: 18, 91

1. Kodi khalidwe lalikulu la Mulungu ndi liti? Nanga kudziŵa zimenezi kukucititsani kumva bwanji ponena za iye?

BAIBULO limatiuza kuti “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) Koma kodi zimenezi zitanthauza ciani? Cikondi ndi khalidwe limodzi mwa makhalidwe abwino ambili a Mulungu, ndipo ndi khalidwe lake lalikulu. Sikuti iye ali cabe ndi cikondi, koma iye ndiye cikondi. Cikondi cimeneci cimam’limbikitsa kucita ciliconse cimene wafuna. Tiyamikila kwambili kuti cikondi cinacititsa kuti Yehova alenge cilengedwe conse ndi zinthu zonse zamoyo.

2. Kodi cikondi ca Mulungu cimatipatsa cidalilo cotani? (Onani cithunzi pamwamba.)

2 Yehova amakonda kwambili cilengedwe cake. Cikondi cake pa ife cimatipatsa cidalilo cakuti colinga cake cokhudza anthu cidzakwanilitsidwa m’njila yabwino kwambili. Zotsatilapo zake n’zakuti anthu amene amamumvela adzakhala ndi cimwemwe ceniceni. Mwacitsanzo, cifukwa ca cikondi, Yehova “wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweluza m’cilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzela mwa munthu amene iye wamuika,” Yesu Kristu. (Machitidwe 17:31) Tili ndi cidalilo cakuti ciweluzo cimeneci cidzacitikadi. Izi zidzacititsa kuti anthu omvela adzakhale ndi moyo wabwino kwamuyaya.

ZIMENE ULAMULILO WA ANTHU WAONETSA

3. Kodi umoyo ukanakhala bwanji Mulungu akanapanda kutikonda?

3 Kodi tsogolo la anthu likanakhala bwanji ngati cikondi silinali khalidwe lalikulu la Mulungu? Anthu akanapitiliza kudzilamulila, komanso kutsogoleledwa ndi mulungu wopanda cikondi ndi woipa, Satana. (2  Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19; ŵelengani Chivumbulutso 12:9, 12.) Ngati Yehova sakanatikonda, tsogolo lathu likanakhala loipa kwambili.

4. N’cifukwa ciani Yehova analola anthu kupandukila ulamulilo wake?

4 Pamene Satana anapandukila ulamulilo wa Mulungu, iye anasonkhezela makolo athu oyamba kuti naonso apanduke. Satana anatsutsa ufulu wa Mulungu wolamulila cilengedwe conse. Iye anakamba kuti ulamulilo wake ndiwo wabwino kuposa wa Mulungu. (Genesis 3:1-5) Yehova anacita zinthu mwanzelu mwa kulola Satana kuti aonetse kwa kanthawi kocepa ngati anali kukamba zoona. Koma zotsatilapo zake zaonetsalatu kuti anthu ndiponso Satana si olamulila abwino.

Yehova sanalenge anthu ndi ufulu wakuti azidzilamulila okha popanda citsogozo cake

5. Kodi mbili ya anthu yaonetsa ciani?

5 Masiku ano, zinthu padzikoli zikuipilaipila. Kwa zaka 100 zapitazo, anthu oposa 100 miliyoni anaphedwa pankhondo. Ponena za “masiku otsiliza,” Baibulo limati: “Anthu oipa ndi onyenga adzaipilaipilabe.” (2 Timoteyo 3:1, 13) Baibulo limakambanso kuti: “Ine ndikudziŵa bwino, inu Yehova, kuti munthu wocokela kufumbi alibe ulamulilo woongolela njila ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo woongolela mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Zimene zakhala zikucitika m’mbili ya anthu zaonetsa kuti mau amenewa ndi oona. Yehova sanalenge anthu ndi ufulu wakuti azidzilamulila okha popanda citsogozo cake.

6. N’cifukwa ciani Mulungu walola kuipa?

6 Yehova waonetsanso kuti ulamulilo wake wokha ndiwo wabwino mwa kulola zoipa kupitilizabe kwa kanthawi. Posacedwapa, Mulungu adzaononga onse oipa. Pambuyo pake, munthu aliyense amene adzapandukila ulamulilo wa Mulungu adzaonongedwa nthawi imeneyo. Zimene zacitika m’mbili ya anthu zidzakhala umboni wakuti anthu opanduka ayenela kuonongedwa mwamsanga. Mulungu sadzalola zoipa kukhalaponso.

KODI MULUNGU WAONETSA BWANJI KUTI AMATIKONDA?

7, 8. Kodi Yehova waonetsa bwanji cikondi cake?

7 Yehova waonetsa cikondi cake cacikulu m’njila zambili. Mwacitsanzo, ganizilani za kukula kwa mlengalenga ndi kukongola kwake. Mu mlengalenga muli milalang’amba mabiliyoni ambili. Ndipo mu mlalang’amba uliwonse muli nyenyezi mabiliyoni ambili ndi mapulaneti. Dzuŵa ndi imodzi mwa nyenyezi zimene zili mu mlalang’amba wathu wa Milky Way. Popanda dzuŵa, padziko lapansi sipakanakhala camoyo ciliconse. Conco, zolengedwa zonse zimaonetsa kuti Yehova ndiye Mlengi wathu, ndiponso zimaonetsa makhalidwe ake monga mphamvu, nzelu, ndi cikondi. Zoonadi, “makhalidwe [a Mulungu] osaoneka ndi maso akuonekela bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso umulungu wake, zikuonekela m’zinthu zimene anapanga.”—Aroma 1:20.

Ciliconse cimene Yehova anapanga padziko lapansi, cimapindulitsa anthu ndi nyama

8 Yehova analenga dziko lapansi kuti mukhale zinthu zamoyo. Ciliconse cimene cili m’dziko lapansi cimapindulitsa anthu ndi nyama. Mulungu anapanga munda wokongola kuti anthu akhalemo, ndipo anawalenga ndi maganizo ndi matupi angwilo kuti akhalepo kwamuyaya. (Ŵelengani Chivumbulutso 4:11.) Kuonjezela apo, “amapeleka cakudya kwa zamoyo zonse pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”—Salimo 136:25.

9. Ngakhale kuti Yehova ndi Mulungu wacikondi, kodi amadana ndi ciani?

9 Popeza kuti Yehova ndi Mulungu wacikondi, iye sakondwela ndi zoipa. Mwacitsanzo, ponena za Yehova, lemba la Salimo 5:4-6 limati: “Inu sindinu Mulungu wokondwela ndi zoipa . . . Mumadana ndi onse ocita zopweteka ena.” Ndiponso Mulungu amadana ndi “munthu wokhetsa magazi ndi wacinyengo.”

MAPETO A ZOIPA ZONSE ALI PAFUPI

10, 11. (a) N’ciani cidzacitikila anthu oipa? (b) Kodi Yehova adzawadalitsa bwanji anthu omvela?

10 Panthawi yake yabwino, Yehova adzacotsapo zoipa zonse m’cilengedwe conse. Adzacita zimenezi cifukwa iye ndi Mulungu wacikondi ndipo amadana ndi zoipa. Mau a Mulungu amatilonjeza kuti: “Ocita zoipa adzaphedwa. Koma oyembekezela Yehova ndi amene adzalandile dziko lapansi. Patsala kanthawi kocepa, woipa sadzakhalakonso.” Adani onse a Yehova “adzazimililika ndi kusanduka utsi.”—Salimo 37:9, 10, 20.

11 Mau a Mulungu amatilonjezanso kuti: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Anthu okhulupilika “adzasangalala ndi mtendele woculuka.” (Salimo 37:11) N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Mulungu wathu wacikondi amacitila atumiki ake okhulupilika zinthu zabwino nthawi zonse. Baibulo limatiuza kuti: “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Limeneli ndi tsogolo labwino kwambili kwa anthu amene amayamikila cikondi ca Mulungu!

12. Kodi munthu “wosalakwa” ndani?

12 Baibulo limatiuza kuti: “Ona munthu wosalakwa ndipo yang’anitsitsa munthu wolungama, pakuti tsogolo la munthu ameneyu ndi lamtendele. Koma anthu onse ocimwa adzafafanizidwa. M’tsogolo, anthu oipa adzaphedwa.” (Salimo 37:37, 38) “Munthu wosalakwa” ndi amene amadziŵa Mulungu ndi Mwana wake ndipo amacita cifunilo ca Mulungu ndi mtima wonse (Ŵelengani Yohane 17:3.) Iye amakhulupilila kuti “dziko likupita limodzi ndi cilakolako cake, koma wocita cifunilo ca Mulungu adzakhala kosatha.” (1 Yohane 2:17) Popeza mapeto a dzikoli ali pafupi, ino ndiyo nthawi ‘yoyembekezela Yehova, ndi kusunga njila zake.’—Salimo 37:34.

NJILA YAIKULU IMENE MULUNGU ANAONETSELA KUTI AMATIKONDA

13. Ndi njila yaikulu iti imene Mulungu anaonetsela kuti amatikonda?

13 Ngakhale kuti ndife opanda ungwilo, n’zotheka kumvela Mulungu. Ndipo n’zothekanso kukhala pa ubwenzi wa ponda apa nane m’pondepo ndi Yehova. Izi zimatheka cifukwa ca nsembe ya dipo ya Yesu, imene ndi njila yaikulu imene Mulungu anaonetsela kuti amatikonda. Yehova anapeleka dipo n’colinga cakuti anthu omvela amasulidwe ku ucimo ndi imfa. (Ŵelengani Aroma 5:12; 6:23.) Yesu ali kumwamba, anali wokhulupilika kwa Mulungu kwa nthawi yaitali. Conco, Yehova anali ndi cidalilo cakuti Mwana wake adzakhalabe wokhulupilika akabwela padziko lapansi. Popeza Yehova ndi Atate wacikondi, iye anawawidwa mtima kwambili ataona mmene anthu anali kuzunzila Mwana wake. Komabe, Yesu anacilikiza ulamulilo wa Mulungu mokhulupilika. Ndipo anaonetsa kuti munthu wangwilo angathe kukhalabe wokhulupilika kwa Mulungu ngakhale panthawi ya mavuto.

Cifukwa ca cikondi cake, Mulungu anatuma Mwana wake (Onani ndime 13)

14, 15. Kodi imfa ya Yesu inapatsa anthu mwai wotani?

14 Ngakhale kuti Yesu anakumana ndi ziyeso zoopsa, iye anakhalabe wokhulupilika kwa Mulungu, ndipo anacilikiza ulamulilo wa Yehova. Tifunika kuyamikila kuti Yesu anapeleka moyo wake monga dipo limene limatipatsa mwai wodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Mtumwi Paulo anafotokoza cikondi cimene Yehova ndi Yesu anaonetsa kudzela m’dipo. Iye anati: “Pamene tinali ofooka, Kristu anafela anthu osapembedza Mulungu pa nthawi yoikidwilatu. Pakuti n’capatali kuti munthu wina afele munthu wolungama. Zoonadi, mwina wina angalimbe mtima kufela munthu wabwino. Koma Mulungu akuonetsa cikondi cake kwa ife, moti pamene tinali ocimwa, Kristu anatifela.” (Aroma 5:6-8) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu anatisonyeza ife cikondi cake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzela mwa iye. Cikondi cimeneci cikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba macimo athu.”—1 Yohane 4:9, 10.

15 Yesu anakamba kuti “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asaonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ngakhale kuti zimenezi zinali zopweteka kwambili kwa Yehova, iye analola kuti Mwana wake aphedwe monga dipo. Izi zionetsa kuti iye amawakonda kwambili anthu. Ndipo cikondi cimeneci cidzakhalapo kwamuyaya. Paulo analemba kuti: “Ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwela m’tsogolo, mphamvu, msinkhu, kuzama, kapena colengedwa cina cilichonse, sicidzatha kutilekanitsa ndi cikondi ca Mulungu cimene cili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 8:38, 39.

UFUMU WA MULUNGU UKULAMULILA

16. Kodi Ufumu wa Mesiya n’ciani? Nanga ndani amene Yehova wamuika kukhala Wolamulila mu Ufumuwo?

16 Boma la Mulungu, limene ndi Ufumu wa Mesiya, ndi umboni winanso wakuti Yehova amatikonda. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti Yehova waika kale Yesu Kristu kukhala Wolamulila, ndipo iye amakonda anthu komanso ndi woyenelela. (Miyambo 8:31) Mulungu anasankha anthu okwana 144,000 kuti akalamulile pamodzi ndi Yesu kumwamba. Iwo akaukitsidwa, amakumbukilabe umoyo wao wakale akali padziko lapansi. (Chivumbulutso 14:1) Pamene Yesu anali padziko lapansi, nkhani yaikulu imene anali kuphunzitsa inali yonena za Ufumu. Iye anaphunzitsa ophunzila ake kupemphela kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Tikuyembekezela mwacidwi kudzaona pemphelo limeneli likuyankhidwa, pamene Ufumu wa Mulungu udzabweletsa madalitso ambili kwa anthu.

17. Fotokozani kusiyana kumene kulipo pakati pa ulamulilo wa Yesu ndi ulamulilo wa anthu.

17 Pali kusiyana kwakukulu pakati pa ulamulilo wacikondi wa Yesu ndi ulamulilo wa anthu. Ulamulilo wa anthu wacititsa nkhondo zambili zimene zapha anthu mamiliyoni. Koma Wolamulila wathu, Yesu, amatikonda kwambili ndipo amatengela makhalidwe abwino a Mulungu, makamaka cikondi cake. (Chivumbulutso 7:10, 16, 17) Yesu anakamba kuti: “Bwelani kwa ine nonsenu ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzilani kwa ine, cifukwa ndine wofatsa ndi wodzicepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mateyu 11:28-30) Limeneli ndi lonjezo labwino kwambili!

18. (a) N’ciani cakhala cikucitika kuyambila mu 1914? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

18 Baibulo limaonetsa kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila kumwamba mu 1914. Kuyambila nthawi imeneyo, otsalila amene adzalamulila pamodzi ndi Yesu kumwamba, ndiponso a “khamu lalikulu” amene adzapulumuka mapeto a dzikoli ndi kulowa m’dziko latsopano, akhala akusonkhanitsidwa. (Chivumbulutso 7:9, 13, 14) Kodi a khamu lalikulu ndi oculuka motani masiku ano? Kodi Mulungu afuna kuti io azicita ciani? Nkhani yotsatila idzayankha mafunso amenewa.