Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pitilizani Kusinkhasinkha Zinthu za Kuuzimu

Pitilizani Kusinkhasinkha Zinthu za Kuuzimu

“Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Dzipeleke pa zinthu zimenezi kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.”—1 TIMOTEYO 4: 15.

NYIMBO: 57, 52

1, 2. N’ciani cimasiyanitsa anthu ndi nyama?

UBONGO wa munthu ndi wapadela kwambili. Mwacitsanzo, anthu ali ndi luso lophunzila cinenelo. Ndipo cinenelo cimatithandiza kudziŵa kuŵelenga, kulemba, kukamba, ndiponso kumvetsa zimene zikukambidwa. Cimatithandizanso kuti tizipemphela ndi kuimba nyimbo zotamanda Yehova. Zinthu zonsezi zimatipangitsa kukhala osiyana ndi nyama. Asayansi samvetsetsa kuti ubongo wathu umakwanitsa bwanji kucita zinthu zodabwitsa zimenezi.

2 Luso lomvetsa ndi kukamba cinenelo ndi mphatso imene Yehova anatipatsa. (Salimo 139:14; Chivumbulutso 4:11) Iye watipatsanso mphatso ina imene imatisiyanitsa ndi nyama. Anthufe tinalengedwa “m’cifanizilo ca Mulungu.” Tili ndi ufulu wodzisankhila zocita. Conco, tikhoza kusankha kugwilitsila nchito cinenelo potumikila ndi kutamanda Yehova.—Genesis 1:27.

3. Kodi Yehova watipatsa ciani kuti tikhale anzelu?

3 Yehova watipatsa Baibulo kuti atidziŵitse mmene tingam’tumikilile ndi kum’tamanda. Baibulo lonse kapena mbali yake, lipezeka m’zinenelo zoposa 2,800. Ngati tisinkhasinkha zimene Baibulo limakamba, timayamba kuona zinthu mmene Mulungu amazionela. (Salimo 40:5; 92:5; 139:17) Kuona zinthu mmene Yehova amaonela kumaticititsa kukhala anzelu, ndipo kudzatitsogolela ku moyo wosatha.—Ŵelengani 2 Timoteyo 3:14-17.

4. Kodi kusinkhasinkha kumatanthauza ciani? Ndipo tikambilana mafunso ati?

4 Kusinkhasinkha kumatanthauza kuika maganizo pa cinthu cinacake, kuciganizila mozama ndiponso mosamala kwambili. (Salimo 77:12; Miyambo 24:1, 2) Tikasinkhasinkha zimene timaphunzila zokhudza Yehova ndi Yesu, timapindula kwambili. (Yohane 17:3) Nkhani ino, iyankha mafunso otsatilawa: Kodi kaŵelengedwe kathu kayenela kukhala kotani kuti tizisinkhasinkha bwino? Ndi zinthu zotani zimene tingasinkhesinkhe? Nanga n’ciani cingatithandize kusinkhasinkha nthawi zonse ndiponso mosangalala?

MUZIONETSETSA KUTI MWAPINDULA PA ZIMENE MWAPHUNZILA

5, 6. N’ciani cingakuthandizeni kukumbukila ndi kumvetsetsa zimene mwaŵelenga?

5 Kodi munaganizilapo za zinthu zimene timacita mwacibadwa? Zinthu monga kupuma, kuyenda, kapena kuchova njinga, timazicita popanda kuziganizila. N’zacisoni kuti nthawi zina timaŵelenga zinthu popanda kuziganizila. Mwina mukhoza kumaganizila zinthu zina uku mukuŵelenga. Mungacite ciani kuti mupewe zimenezi? Mufunika kuika maganizo anu pa zimene muŵelenga ndi kuganizila tanthauzo lake. Ndiyeno, mukatsiliza kuŵelenga ndime kapena mutu uliwonse m’cofalitsa, imani pang’ono ndi kuganizila zimene mwaŵelengazo. Ganizilani zimene mwaphunzila, ndipo onetsetsani kuti mwazimvetsetsa.

Kuŵelenga Baibulo mokweza kudzakuthandizani kumvetsetsa ndi kukumbukila kwambili zimene mwaŵelenga

6 Asayansi apeza kuti cimakhala copepuka kukumbukila cinthu ngati tikuciŵelenga mokweza. Mlengi wathu adziŵa zimenezi. Ndiye cifukwa cake anauza Yoswa kuti aziŵelenga buku la cilamulo ndi “kusinkhasinkha,” kutanthauza kuliŵelenga capansipansi. (Ŵelengani Yoswa 1:8.) Kuŵelenga Baibulo mokweza kudzakuthandizani kumvetsetsa ndi kukumbukila kwambili zimene mwaŵelengazo.

7. Ndi nthawi iti yabwino yosinkhasinkha Malemba? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

7 Khama n’lofunika kuti tizisinkhasinkha ndi kuika maganizo pa zimene tiphunzila. Ndiye cifukwa cake tifunika kumasinkhasinkha pamene sindife otopa, tili pamalo acete, ndiponso pamene palibe zinthu zambili zosokoneza. Wamasalimo Davide anali kusinkhasinkha ali pabedi usiku. (Salimo 63:6) Yesu amene anali wangwilo, anasankha malo acete kuti asinkhesinkhe ndi kupemphela.—Luka 6:12.

ZINTHU ZABWINO ZIMENE MUNGASINKHESINKHE

8. (a) Ndi zinthu zotani zimene tingasinkhesinkhe? (b) Yehova amamva bwanji tikamauzako ena za iye?

8 Kuonjezela pa zimene mumaŵelenga m’Baibulo, pali zinthu zina zimene mungasinkhesinkhe. Mwacitsanzo, mukaona cinthu codabwitsa cimene Yehova analenga, dzifunseni kuti, ‘Kodi cimeneci cikundiphunzitsa ciani ponena za Yehova?’ Kuganizila zimenezo kudzakucititsani kumuyamikila Yehova m’pemphelo. Ndipo mukamaceza ndi anthu ena mudzawauzako zimenezo. (Salimo 104:24; Machitidwe 14:17) Yehova amachela khutu, ndipo amasangalala akationa kuti tikusinkhasinkha, kupemphela, ndi kuuzako ena za iye. Baibulo limatitsimikizila kuti: “Buku la cikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake. Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene anali kuganizila za dzina lake.”—Malaki 3:16.

Kodi mumasinkhasinkha mmene mungathandizile ophunzila Baibulo? (Onani ndime 9)

9. (a) Kodi Paulo anauza Timoteyo kuti azisinkhasinkha za ciani? (b) Tingasinkhesinkhe ciani tikamakonzekela utumiki?

9 Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti azisinkhasinkha mmene zokamba zake, khalidwe lake ndi zimene amaphunzitsa zimakhudzila anthu ena. (Ŵelengani 1 Timoteyo 4:12-16.) Inunso mukhodza kusinkhasinkha zinthu zimenezi. Mwacitsanzo, mukamakonzekela kukacititsa phunzilo la Baibulo, muzipeza nthawi yosinkhasinkha. Ganizilani zosoŵa za wophunzila wanu, ndipo pezani funso kapena fanizo limene lidzamuthandiza kupita patsogolo. Mukamakonzekela phunzilo la Baibulo mwa njila imeneyo, cikhulupililo canu cidzalimba. Mudzayamba kuphunzitsa mogwila mtima. Mudzapindulanso ngati musinkhasinkha musanapite mu utumiki. (Ŵelengani Ezara 7:10.) Mwina mungaŵelenge caputala m’buku la Machitidwe kuti mukhale wacangu mu utumiki. Mungasinkhesinkhenso pa malemba ndi zofalitsa zimene mufuna kukagaŵila. (2 Timoteyo 1:6) Ganizilani anthu a m’gawo lanu ndiponso zimene mungakambe kuti akhale ndi cidwi. Mukamakonzekela utumiki mwa njila imeneyi, mudzakwanitsa kugwilitsila nchito Baibulo mwaluso kuti mulalikile mogwila mtima.—1 Akorinto 2:4.

Lolani kuti zimene mwaŵelenga zikukhudzeni mtima, ndipo yamikilani Yehova pa zinthu zabwino zimene wakuphunzitsani

10. Ndi zinthu zabwino ziti zimene mungasinkhesinkhe?

10 N’ciani cina cimene mungasinkhesinkhe? Mukalemba mfundo zofunika pa nkhani ya onse, pamisonkhano yapadela ndi yacigawo, muzipeza nthawi yobwelelamo. Pamene mucita izi dzifunseni kuti, ‘Ndaphunzila ciani m’Mau a Mulungu ndi gulu lake?’ Mungasinkhesinkhenso nkhani zimene zimapezeka mu Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani! ndiponso m’zofalitsa zimene zinatulutsidwa posacedwapa pamsonkhano wacigawo. Mukaŵelenga cocitika cina cake mu Buku Lapacaka, imani pang’ono ndi kuganizila zimene mwaŵelenga kuti zikukhudzeni mtima. Mukaŵelenga cofalitsa cathu, mungalembe mzele pa mfundo zothandiza kapena kulemba tumau tocepa m’mphepete mwa tsamba la cofalitsaco. Zimenezi zidzakuthandizani mukamakonzekela ulendo wobweleza, waubusa kapena nkhani. Koposa zonse, mukamaima pang’ono ndi kusinkhasinkha pa zimene mwaŵelenga, cofalitsaco cidzakukhuzani mtima. Ndipo mudzapeza nthawi yoyamikila Yehova pa zinthu zabwino zimene watiphunzitsa.

MUZISINKHASINKHA MAU A MULUNGU TSIKU LILILONSE

11. Ndi cofalitsa cofunika citi cimene tifunika kusinkhasinkha? Ndipo kucita zimenezi kudzatithandiza bwanji? (Onani mau a munsi.)

11 Baibulo ndiye buku lofunika kwambili kulisinkhasinkha. Nanga bwanji ngati tsiku lina mulibe mwai wokhala ndi Baibulo? * (Onani mau a munsi) Palibe angakulepheletseni kusinkhasinkha pa zinthu zimene munaloŵeza pamtima, zinthu monga malemba amene mumakonda, kapena nyimbo za Ufumu. (Machitidwe 16:25) Ndipo mzimu wa Mulungu udzakuthandizani kukumbukila zinthu zimene munaphunzila. Zimenezi zidzakuthandizani kukhalabe wokhulupilika.—Yohane 14:26.

12. Mungakonze bwanji ndandanda yoŵelenga Baibulo tsiku lililonse?

12 Mungakonze bwanji ndandanda yoŵelenga Baibulo tsiku lililonse? Masiku ena mkati mwa mlungu, mwina mungaŵelenge ndi kusinkhasinkha mfundo za m’Baibulo malinga ndi ndandanda ya Sukulu ya Ulaliki. Masiku ena mungaŵelenge mabuku a Uthenga Wabwino wa Mateyu, Maliko, Luka, ndi Yohane. Ndipo mungasinkhesinkhe zimene Yesu anakamba ndi kucita. (Aroma 10:17; Aheberi 12:2; 1 Petulo 2:21) Tilinso ndi cofalitsa cimene cimafotokoza zocitika pa umoyo wa Yesu motsatila nthawi imene zinacitika. Cofalitsa cimeneci cingakuthandizeni kuti mupindule kwambili mukamaŵelenga mabuku a Uthenga Wabwino.—Yohane 14:6.

N’CIFUKWA CIANI KUSINKHASINKHA N’KOFUNIKA KWAMBILI?

13, 14. N’cifukwa ciani kupitiliza kusinkhasinkha za Yehova ndi Yesu n’kofunika kwambili? Ndipo zimenezi zidzatilimbikitsa kucita ciani?

13 Kusinkhasinkha za Yehova ndi Yesu kungathandize Mkristu kukhala wokhwima kuuzimu ndi kukhalabe ndi cikhulupililo colimba. (Aheberi 5:14; 6:1) Munthu amene amakhala ndi nthawi yocepa yosinkhasinkha za Mulungu, pang’nopang’ono angayambe kutaya ubwenzi wake ndi Yehova kapena angafike pomusiilatu. (Aheberi 2:1; 3:12) Yesu anaticenjeza kuti ngati sitimvela kapena kulandila Mau a Mulungu ndi “mtima woona komanso wabwino,” ‘sitingawagwilitsitse.’ M’malo mwake, zingakhale zosavuta ‘kutengeka ndi nkhawa, cuma ndi zosangalatsa za moyo uno.’—Luka 8:14, 15.

14 Conco, tiyeni tipitilize kusinkhasinkha Malemba kuti timudziŵe bwino Yehova. Kucita zimenezi kudzatilimbikitsa kutengela kwambili makhalidwe ake. (2 Akorinto 3:18) Tidzapitilizabe kuphunzila zambili zokhudza Atate wathu wakumwamba ndi kumutsanzila kwamuyaya. Umenewu ndi mwai wamtengo wapatali kwambili.—Mlaliki 3:11.

Kusinkhasinkha za Yehova ndi Yesu kudzakuthandizani kukhalabe wacangu potumikila Mulungu

15, 16. (a) Kodi kusinkhasinkha za Yehova ndi Yesu kwakupindulitsani bwanji? (b) N’cifukwa ciani nthawi zina kusinkhasinkha n’kovuta? Koma n’cifukwa ciani tifunika kuyesayesa kucita zimenezo?

15 Kusinkhasinkha za Yehova ndi Yesu kudzakuthandizani kukhalabe wacangu potumikila Mulungu. Cangu canu cidzalimbikitsa abale anu ndiponso anthu amene mumalalikila. Ngati musinkhasinkha zimene Yehova anakucitilani mwa kukupatsani nsembe ya dipo ya Yesu, mudzapitiliza kuyamikila ubwenzi wanu ndi Mulungu. (Aroma 3:24; Yakobo 4:8) Mark, m’bale wa ku South Africa amene anakhala m’ndende kwa zaka zitatu cifukwa ca cikhulupililo cake, anakamba kuti: “Kusinkhasinkha kuli ngati kupita ku malo osangalatsa. Tikasinkhasinkha kwambili zinthu za kuuzimu, tidzaziŵanso zinthu zambili zatsopano zokhudza Mulungu wathu, Yehova. Nthawi zina ndikafooka kapena kudela nkhawa za tsogolo langa, ndimatenga Baibulo ndi kusinkhasinkha Malemba. Zimenezi zimandikhazika mtima pansi.”

16 Umoyo m’dziko lino ndi wodzala ndi zinthu zosokoneza cakuti zimakhala zovuta kupeza nthawi yosinkhasinkha Malemba. Patrick, m’bale wa ku Africa, anati: “Maganizo anga ali monga bokosi la mameseji lodzala ndi zinthu zambili, zoyenela ndi zosayenela. Ndipo ndimafunika kucotsamo zina tsiku lililonse. Ndikafufuza zimene zili m’maganizo mwanga, nthawi zambili ndimapezamo ‘maganizo olefula.’ Ndisanayambe kusinkhasinkha, ndimapemphela kwa Yehova kuti ndikhale ndi maganizo oyenela. Ngakhale kuti pamapita nthawi kuti ndiyambe kusinkhasinkha zinthu za kuuzimu, ndimamvela kuti ndili pafupi ndi Yehova. Zimenezi zimandicititsa kumvetsa bwino coonadi.” (Salimo 94:19) Kukamba zoona, timapindula m’njila zambili ngati tiŵelenga ndi kusinkhasinkha Malemba tsiku lililonse.—Machitidwe 17:11.

KODI MUMASINKHASINKHA NTHAWI ITI?

17. Kodi mumasinkhasinkha nthawi iti?

17 Ena amauka m’maŵa kuti aŵelenge, kusinkhasinkha, ndi kupemphela. Ena amacita izi pa nthawi yopumula masana. Mwina inu mumaona kuti nthawi yabwino yoŵelenga Baibulo ndi m’madzulo kapena usiku musanagone. Ena amakonda kuŵelenga Baibulo m’maŵa ndi m’madzulo asanapite kukagona. (Yoswa 1:8) Cofunika kwambili ndi ‘kugwilitsa nchito bwino nthawi yanu,’ kutanthauza kucepetsako nthawi yocita zinthu zina zosafunika kuti muzisinkhasinkha Mau a Mulungu tsiku lililonse.—Aefeso 5:15, 16.

18. N’ciani cimene Baibulo limalonjeza anthu amene amasinkhasinkha Mau a Mulungu tsiku lililonse ndi kucita zimene aphunzila?

18 Baibulo limalonjeza kuti Yehova adzadalitsa onse amene amasinkhasinkha Mau ake, ndi kuyesetsa kucita zimene aphunzila. (Ŵelengani Salimo 1:1-3.) Yesu anakamba kuti: “Odala ndi amene akumva mau a Mulungu ndi kuwasunga.” (Luka 11:28) Koma koposa zonse, kusinkhasinkha Mau a Yehova tsiku lilionse kudzatithandiza kucita zinthu zimene zimam’lemekeza. Tikatelo, Yehova adzatidalitsa, tidzakhala osangalala tsopano, ndipo tidzapeza moyo wosatha m’dziko lake latsopano.—Yakobo 1:25; Chivumbulutso 1:3.

^ par. 11 Onani nkhani yakuti “Tinayesetsa Kuti Tikhale Olimba Mwauzimu” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2006.