Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi
Tingaonetse bwanji kuti timaganizila abale ndi alongo amene amadwala akamva fungo la pelefyumu?
Anthu amene amadwala akamva fungo la pelefyumu amavutika kwambili. Zimakhala zovuta kwa io kupewelatu fungo la pelefyumu cifukwa amakumana ndi anthu osiyanasiyana tsiku ndi tsiku. Conco, ena afunsapo ngati n’zotheka kupempha abale ndi alongo kuleka kugwilitsila nchito pelefyumu ndi mafuta ena onunkhila akamabwela ku misonkhano yampingo, yadela, ndi yacigawo.
Palibe Mkristu amene mwadala angafune kuti mnzake azilephela kupezeka pa misonkhano yacikristu. Tonse timasangalala kulandila cilimbikitso pa misonkhano yathu. (Aheb. 10:24, 25) Conco, aliyense amene amadwala cifukwa ca fungo la pelefyumu moti amalephela kufika pa misonkhano angakambilane ndi akulu za nkhaniyo. Ngakhale kuti si ca m’Malemba ndipo sicoyenela kuti akulu azipanga malamulo okhudza kagwilitsidwe nchito ka pelefyumu pobwela ku misonkhano, io angadziŵitse mpingo za mavuto amene ena akukumana nao cifukwa ca pelefyumu. Akulu angakonze zakuti pakhale nkhani ya zosoŵa za pampingo pa Msonkhano wa Nchito pogwilitsila nchito nkhani imene inatulukapo malinga ndi zosoŵa za pamalopo. Angapelekenso cilengezo cokhudza nkhaniyo mwa njila yosakhumudwitsa ena. * Koma n’zosatheka kuti akulu azilengeza zimenezi nthawi zonse. Pa misonkhano yathu, nthawi zonse pamabwela anthu atsopano acidwi ndiponso alendo amene sadziŵa za vutolo, ndipo timafuna kuti io akhale omasuka. Amene amagwilitsila nchito pelefyumu mosapitilila malile sayenela kudziona kuti ndi olakwa.
Ngati pali ena amene ali ndi vutoli, bungwe la akulu lingakonze zakuti anthu amene amadwala cifukwa ca fungo la pelefyumu akhale paokha m’Nyumba ya Ufumu ngati n’zotheka. Mwacitsanzo, ngati m’Nyumba ya Ufumu muli cipinda cina mmene angathe kumvetsela misonkhano, io angakhale mmenemo. Ngati vutolo likupitililabe ndipo ena akuvutikabe ndi fungo la pelefyumu, mungakonze zowajambulila misonkhano kapena kuwalumikiza pafoni kuti azimvetsela misonkhanoyo ali kunyumba, monga mmene zimakhalila ndi anthu ena amene sakwanitsa kuyenda.
M’zaka zaposacedwapa, Utumiki Wathu wa Ufumu wakhala ukulimbikitsa abale ndi alongo kuti aziganizila ena pankhani yogwilitsila nchito pelefyumu akamabwela ku misonkhano yacigawo. Timalimbikitsidwa kuganizila ena makamaka pa misonkhano yacigawo, cifukwa cakuti n’zosatheka kukhala ndi malo apadela a anthu amene amadwala cifukwa ca fungo la pelefyumu. Komabe, colinga copelekela malangizo amenewa si cakuti likhale lamulo limene mipingo iyenela kutsatila.
Popeza tikukhala m’dongosolo lino la zinthu, tonse timavutika cifukwa ca kupanda ungwilo. Koma timayamikila kwambili zimene ena amacita potithandiza kucepetsa mavuto athu. N’kovuta kuti ena apewe kugwilitsila nchito pelefyumu kapena mafuta ena onunkhilitsa kuti amene amadwala cifukwa ca fungo la zinthu zimenezi asalephele kupezeka pa misonkhano yacikristu. Koma cikondi cidzatisonkhezela kucita zimenezo.
Kodi mabuku ena a ku dziko amavomeleza kuti panali munthu wochedwa Pontiyo Pilato?
Anthu amene amaŵelenga Baibulo amam’dziŵa Pontiyo Pilato cifukwa ca zimene anacita pamene Yesu anali kuimbidwa mlandu mpaka kuphedwa. (Mat. 27:1, 2, 24-26) Komabe, dzina lake limapezekanso nthawi zambili m’mabuku ena a mbili zakale. Dikishonale ina inakamba kuti mafaelo ofotokoza za Pontiyo Pilato ndi “ambili ndipo amafotokoza zinthu zambili zokhudza iye kuposa za bwanamkubwa waciroma aliyense amene analamulilapo mu Yudeya.”—The Anchor Bible Dictionary.
Dzina la Pilato limapezeka nthawi zambili m’mabuku a wolemba mbili yakale waciyuda wochedwa Josephus. Iye analemba zocitika zitatu pofotokoza za mavuto amene Pilato anakumana nao polamulila Yudeya. Ndipo wolemba mbili yakale waciyuda wochedwa Philo, anaonjezela cocitika cacinai. Wolemba mbili waciroma wina wochedwa Tacitus, amene analemba za olamulila ufumu wa Roma, anatsimikizila kuti Pontiyo Pilato analamula kuti Yesu aphedwe panthawi imene Tiberiyo anali kulamulila.
Mu 1961, akatswili ofukula zinthu zakale anapeza mwala umene panali dzina la Pilato m’Cilatini pamene anali kufukula zinthu zakale m’bwalo la maseŵela la Aroma limene linali m’dela la Kaisareya, ku Israel. Mau amene ali pamwalawo sakuonekela bwinobwino, koma ayenela kuti anali kunena kuti: “Tiberieum (iyi) nyumba imene Pontiyo Pilato, Bwanamkubwa wa ku Yudeya, anapeleka kwa milungu yolemekezeka.” Nyumba imeneyo iyenela kuti inali kacisi amene anamangidwa pofuna kulemekeza Mfumu ya Roma yochedwa Tiberiyo.
Kodi mlongo ayenela kuvala cakumutu pamene akucititsa phunzilo la Baibulo limodzi ndi mwamuna wofalitsa?
Nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” ya mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002, inafotokoza kuti mlongo ayenela kuvala cakumutu ngati akucititsa phunzilo la Baibulo limodzi ndi mwamuna kaya ndi wobatizidwa kapena ai. Komabe, pakhalako masinthidwe ena okhudza nkhani imeneyi.
Ngati mlongo wapita ndi m’bale wobatizidwa kukacititsa phunzilo la Baibulo, mlongoyo ayenela kuvala cakumutu. Akacita zimenezi, amaonetsa kuti akulemekeza makonzedwe a Yehova okhudza umutu mumpingo wacikristu, cifukwa cakuti kuphunzitsa ndi udindo wa abale. (1 Akor. 11:
Komabe, ngati mlongo wapita ndi mwamuna wosabatizidwa kukacititsa phunzilo la Baibulo lokhazikika, ndipo mwamunayo si mwamuna wake, iye safunikila kuvala cakumutu monga mmene Malemba amakambila. Ngakhale zili conco, alongo ena cikumbumtima cao cingawalole kuvala cakumutu pazocitika ngati zimenezi.
^ par. 4 Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani yakuti “Kuthandiza Anthu Odwala MCS,” mu Galamukani! ya August 8, 2000, masamba 24-26.