Kodi N’zotheka Kukhala m’Cikondi Ceniceni?
“Kuyaka [kwa cikondi] kuli ngati kuyaka kwa moto. Cikondico ndi lawi la Ya.”—NYIMBO 8:6.
1, 2. Ndani angapindule mwa kuphunzila mosamala Nyimbo ya Solomo? Nanga cifukwa ciani? (Onani cithunzi cili pamwamba.)
TAYELEKEZELANI kuti muli ku mwambo wa cikwati, ndipo okwatilanawo akuyang’anana ndi kumwetulilana monyadilana. N’zoonekelatu kwa onse opezeka ku mwambowo kuti aŵiliwo akukondana kwambili. M’bale amene wapeleka nkhani ya cikwati cao akuona okwatilanawo agwilana manja mwacikondi, ndipo akuganiza kuti, ‘Kodi cikondi ca aŵiliwa cidzapitiliza kukula pamene zaka zikupita? Kapena kodi cidzayamba kutha pang’onopang’ono?’ Ngati mwamuna ndi mkazi amakondanadi, cikwati cao cidzakhalabe colimba ngakhale atakumana ndi mavuto aakulu. Koma n’zomvetsa cisoni kuti okwatilana ambili amasiya kukondana ndipo amalekana. N’cifukwa cake mungafunse kuti: ‘Kodi cikondi cimakhalitsadi?
2 Cikondi ceniceni cinali cosoŵeka ngakhale m’nthawi ya Mfumu Solomo. Cifukwa ciani? Solomo anafotokoza kuti: “Pa anthu 1,000, ndapezapo mwamuna mmodzi yekha woongoka mtima, koma pa anthu onsewa sindinapezepo mkazi woongoka mtima. Zimene ndapeza n’zakuti, Mulungu woona anapanga anthu oongoka mtima, koma anthuwo asankha njila zina zambilimbili.” (Mlal. 7:26-29) Akazi acilendo aciwelewele amene anali kulambila Bala anali kukhala pakati pa Aisiraeli. Pa cifukwa cimeneci, amuna ndi akazi ambili aciisiraeli anakhalanso aciwelewele. * Koma zaka pafupifupi 20 m’mbuyomo, Mfumu Solomo analemba ndakatulo yokhudza mwamuna ndi mkazi amene analidi m’cikondi ceniceni. Kaya tili pa banja kapena ai, Nyimbo ya Solomo ingatithandize kudziŵa cikondi ceniceni ndi mmene tingacisonyezele.
N’ZOTHEKA KUKHALA M’CIKONDI CENICENI
3. N’cifukwa ciani n’zotheka kuti mwamuna ndi mkazi azisonyezana cikondi ceniceni?
3 Ŵelengani Nyimbo ya Solomo 8:6. Pa lembali, cikondi cikufotokozedwa kuti ndi “lawi la Ya.” N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti cikondi ndi khalidwe lalikulu la Yehova, ndipo anatilenga m’njila yakuti tizitha kutengela cikondi cake. (Gen. 1:26, 27) Pambuyo poti Yehova walenga munthu woyamba, Adamu, Iye anam’patsa mkazi wokongola. Pamene Adamu anaona Hava kwa nthawi yoyamba, iye anasangalala kwambili cakuti sanabise mmene anali kumvelela pamene ananena ndakatulo yake. Hava nayenso anakonda kwambili mwamuna wake. Ndipo mpake kuti anatelo cifukwa Yehova analenga Hava kucoka kwa Adamu. (Gen. 2:21-23) Popeza kuti Yehova analenga anthu m’njila yakuti azisonyeza cikondi, n’zotheka kuti mwamuna ndi mkazi azisonyezana cikondi ceniceni.
4, 5. Fotokozani mwacidule nkhani imene ili m’Nyimbo ya Solomo.
4 Nyimbo ya Solomo imafotokoza bwino kwambili za cikondi cimene cingakhale pakati pa mwamuna ndi mkazi. Nyimboyi ndi yokhudza cikondi ca pakati pa mtsikana wa ku mudzi wina wochedwa Sunemu, kapena kuti Sulemu, ndi m’busa wacinyamata. Nkhani yake ndi yakuti mtsikanayo anali kugwila nchito m’munda wa mpesa wa mlongosi wake. Mundawo unali pafupi ndi malo pamene Mfumu Solomo ndi asilikali ake anali kukhala. Mfumu Solomo anaona mtsikanayo ndipo analamula akapolo ake kumubweletsa kwa iye. Ndiyeno mfumuyo inauza mtsikanayo kuti anali wokongola kwambili, ndipo anam’lonjeza mphatso zambili. Koma mtsikanayo anali pa cisumbali ndi m’busa wacinyamata, ndipo anaumilila kunena kuti afunitsitsa kukhala ndi mnyamatayo. (Nyimbo 1:4-14) M’busayo anafunafuna kumene kunali mtsikanayo mpaka anam’peza. Atam’peza, anayamba kuonetsana ndi kuuzana mau acikondi.—Nyimbo 1:15-17.
5 Pamene Solomo anali kubwelela ku Yerusalemu, iye anapitila limodzi ndi mtsikanayo, ndipo m’busa wacinyamata anatsatila mtsikanayo. (Nyimbo 4:1-5, 8, 9) Ngakhale kuti Solomo anayesa kukopa mtsikanayo mwa njila zosiyanasiyana, mtsikanayo anapitiliza kukonda m’busayo. (Nyimbo 6:4-7; 7:1-10) Kenako, Solomo analola mtsikanayo kubwelela kwao. Pomaliza pake, Msulami anaitana wacikondi wake kuti abwele mothamanga kwa iye “ngati insa.”—Nyimbo 8:14.
6. N’cifukwa ciani n’zovuta kudziŵa amene akulankhula m’Nyimbo ya Solomo?
6 Nyimbo ya Solomo imachedwa “nyimbo yokoma kwambili.” (Nyimbo 1:1) Koma m’nyimboyi, Solomo sanalembe maina a amene akulankhula. Sanafune kulemba zinthu zina zosafunika kwenikweni cifukwa cakuti anali kufuna kuonetsa kukoma kwa nyimbo yolembedwa mwa ndakatulo. Koma ngakhale kuti m’nyimboyo mulibe maina, n’zotheka kudziŵa amene akukamba mwakumva zimene akulankhula.
“CIKONDI CIMENE UMANDISONYEZA CIMAPOSA VINYO KUKOMA KWAKE”
7, 8. N’ciani cimene tinganene ponena za mau acikondi amene ali m’Nyimbo ya Solomo? Pelekani zitsanzo.
7 Mtsikana ndi m’busa wacinyamata anauzana zinthu zambili posonyezana cikondi. Izi zinacitika zaka zoposa 3,000 m’mbuyomu, ndipo kuonetsana cikondi mwa njila imeneyi kungaoneke kwacilendo kwa ife masiku ano. Ngakhale kuti cikhalidwe cao cinali cosiyana ndi cathu, tikhoza kuzindikila kuti aŵiliwa anali kukondana kwambili. Mwacitsanzo, mnyamata anakamba kuti maso a wokondedwa wake anali monga “maso a njiwa,” kusonyeza kuti anali kukonda maso a mtsikanayo. (Nyimbo 1:15) Mtsikanayo anayelekezela maso a wokondedwa wake ndi njiwa zenizeni osati maso a njiwazo. (Ŵelengani Nyimbo ya Solomo 5:12.) Iye anaona kuti mbali yakuda ya maso imene imazungulilidwa ndi mbali yoyela ya maso a bwenzi lakelo, ndi yokongola kwambili ngati njiwa zimene zikusamba mumkaka.
8 M’busayo ndi mtsikana wake, anayamikilanso zinthu zina kuonjezela pa maonekedwe ao. Mwacitsanzo, mbusayo anali kukonda mmene mtsikanayo anali kukambila ndi anthu ena. (Ŵelengani Nyimbo ya Solomo 4:7, 11.) Mbusayo anauza mtsikanayo kuti: “Milomo yako imangokhalila kukha uchi wapacisa.” N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti uci wapacisa umanzuna, ndipo umanunkhila kuposa uci umene wapitidwa mphepo. “Uci ndi mkaka zili kuseli kwa lilime [la mtsikanayo],” kutanthauza kuti mau ake ndi abwino ndiponso okoma ngati uci ndi mkaka. Mwacionekele, pamene mbusayo anauza mtsikanayo kuti “ndiwe wokongola paliponse, . . . ndipo mwa iwe mulibe cilema ciliconse,” sanali kutanthauza maonekedwe akunja cabe.
9. (a) Kodi cikondi ca anthu okwatilana cimaphatikizapo ciani? (b) N’cifukwa ciani okwatilana ayenela kuuzana mau acikondi?
9 Okwatilana amene amatumikila Yehova, samaona cikwati kukhala mgwilizano wamba. Iwo amakondana kwambili ndipo amasonyezana cikondi. Koma ndi cikondi cotani cimene ayenela kusonyezana? Kodi ciyenela kukhala cikondi copanda dyela cimene Baibulo limatiphunzitsa kusonyeza anthu onse? (1 Yoh. 4:8) Kodi ndi cikondi cimene anthu a m’banja limodzi amasonyezana? Kodi ndi cikondi ca pakati pa mabwenzi apamtima? (Yoh. 11:3) Kapena kodi ndi cikondi ca pakati pa mwamuna ndi mkazi? (Miy. 5:15-20) Kunena zoona, okwatilana ayenela kusonyezana cikondi ca mitundu yonseyi. Iwo ayenela kupeza nthawi yotsimikizilana kuti amakondana mwa mau ndi zocita zao. Kucita zimenezi kudzathandiza kuti azisangalala mu cikwati cao. M’zikhalidwe zina, makolo ndi amene amasankhila mwana wao munthu wokwatilana naye, ndipo okwatilanawo samadziŵana mpaka pa tsiku la cikwati. Zikakhala conco, okwatilanawo ayenela kuzindikila kuti afunika kuuzana mau acikondi cifukwa zimenezi zidzathandiza kuti cikondi cao cilimbe, ndipo cikwati cao cidzakhala copambana.
10. Kodi kusonyezana cikondi kumalimbitsanso bwanji cikwati?
10 Okwatilana amalimbitsanso cikwati cao mwa njila ina akamauzana mau acikondi. Mfumu Solomo analonjeza Msulami kuti adzam’pangila ‘zokongoletsa zoti azivala kumutu. Zokongoletsazo zokhala zozungulila, zagolide, zokhala ndi mikanda yasiliva.’ Solomo anatama mtsikanayo kuti ndi “wokongola ngati mwezi wathunthu, wosadetsedwa ngati dzuwa lowala.” (Nyimbo 1:9-11; 6:10) Koma mtsikanayo anakhalabe wokhulupilika kwa m’busa wake wokondedwa. N’ciani cinam’thandiza kukhalabe wokhulupilika kwa m’busayo panthawi imene anali kukhala motalikilana? (Ŵelengani Nyimbo ya Solomo 1:2, 3.) Cimene cinam’thandiza ndi kukumbukila cikondi cimene wokondedwa wake anali kumuonetsa kuti “cimaposa vinyo kukoma kwake,” ndipo dzina lake linali “ngati mafuta othila pamutu.” (Sal. 23:5; 104:15) Inde, n’zofunika kuti okwatilana azisonyezana cikondi kaŵilikaŵili cifukwa zimenezo zimathandiza cikondi cao kukula. Kukumbukila mmene amasonyezelana cikondi kumathandiza cikwati cao kukhala colimba.
MUSAYESE KUDZUTSA CIKONDI “MPAKA PAMENE CIKONDICO CIFUNILE”
11. Kodi mau a Msulami kwa atsikana amene anali kukhala m’nyumba yacifumu ya Solomo amatiphunzitsa ciani?
11 Ngati mukufuna wokwatilana naye, n’ciani cimene mungaphunzile kucokela kwa Msulami? Iye sanali kukonda Mfumu Solomo, ndipo anauza atsikana amene anali kukhala m’Nyumba Yacifumu ya Solomo kuti: “Musayese kudzutsa cikondi mwa ine mpaka pamene cikondico cifunile.” (Nyimbo 2:7; 3:5) N’cifukwa ciani anatelo? Cifukwa cakuti munthu sayenela kukhala m’cikondi ndi wina aliyense amene angamfikile. Mkristu amene afuna kuloŵa m’banja ayenela kuleza mtima kuti apeze munthu amene adzam’konda ndi mtima wonse.
12. N’cifukwa ciani Msulami anakonda m’busa?
12 N’cifukwa ciani Msulami anakonda m’busa? N’zoona kuti m’busayo anali wokongola ngati “ mbawala,” zala zake zinali zolimba ngati “ zagolide,” miyendo yake inali yokongola ndi yolimba “ngati zipilala zamiyala ya mabo.” Koma sanali cabe wolimba ndi wokongola. Mtsikanayo anali kudziŵa kuti m’busayo anali kukonda Yehova komanso anali ndi makhalidwe abwino. Ndiye cifukwa cake anaona kuti wacikondi wake anali “monga mtengo wa maapozi pakati pa mitengo ya m’nkhalango, . . . pakati pa ana aamuna.”—Nyimbo 2:3, 9; 5:14, 15.
13. N’cifukwa ciani m’busa anakonda Msulami?
13 Nanga bwanji za Msulami? Ngakhale kuti anali wokongola kwambili cakuti anakopa mfumu imene panthawiyo inali ndi “mafumukazi 60, adzakazi 80 ndi atsikana osaŵelengeka,” Msulami anali kudziona ngati “duwa lonyozeka la m’cigwa ca m’mphepete mwa nyanja.” Mtsikanayu anali wodekha ndi wodzicepetsa kwambili. Ndiye cifukwa cake m’busayo anali kumuona kuti ndi wapadela “monga duwa pakati pa zitsamba zaminga.” Msulami anali wokhulupilika kwa Yehova.—Nyimbo 2:1, 2; 6:8.
14. N’ciani cimene tingaphunzile kwa m’busa ndi Msulami ngati tifuna kuloŵa m’banja?
14 Yehova amalamula atumiki ake kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Izi zitanthauza kuti Mkristu wosakwatiwa ayenela kupewa kuyamba cisumbali ndi munthu amene si Mboni ya Yehova yobatizidwa. Kodi zimenezi zingakhudze bwanji cikwati? Monga anthu okwatilana, io angadzakumane ndi mavuto pa umoyo wao. Koma ngati onse ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, cikwati cao cidzakhala camtendele ndi cacimwemwe. Motelo ngati mufuna kuloŵa m’banja tengelani citsanzo ca m’busa ndi Msulami. Muyenela kupeza munthu wa makhalidwe abwino komanso wokonda Yehova.
MKWATIBWI WANGA “ALI NGATI MUNDA WOCHINGIDWA NDI MPANDA”
15. N’ciani cimene Akristu amene ali pa cisumbali ayenela kuphunzila pa kukhulupilika kwa Msulami?
15 Ŵelengani Nyimbo ya Solomo 4:12. N’cifukwa ciani m’busa anakamba kuti wokondedwa wake anali “ngati munda wochingidwa ndi mpanda”? Munda wochingidwa sumakhala woonekela kwa anthu onse. Msulami anali ngati mundawo cifukwa anali kukonda cabe m’busa. Ngakhale kuti mfumu inali kumukopa, iye sanafune kusintha maganizo ake. Msulami anali kufuna kukwatiwa ndi m’busayo basi. Msulamiyo anali monga “khoma” osati monga “citseko” cimene cimatseguka mosavuta. (Nyimbo 8:8-10) Mofananamo, Akristu amene ali pa cisumbali ayenela kukhala okhulupilika kwa wina ndi mnzake. Iwo sayenela kukhala m’cikondi ndi munthu wina kusiyapo cisumbali cao.
16. Kodi Nyimbo ya Solomo imatiphunzitsa ciani pankhani ya cisumbali?
16 Pamene m’busa anauza Msulami kuti apite limodzi kokayenda, azilongosi ake anamuletsa. M’malo mwake, io anam’patsa nchito yolondela minda yampesa yao. Kodi sanali kum’khulupilila? Kodi anali kuganiza kuti Msulami anali kufuna kucita ciwelewele ndi m’busayo? Iyai. Azilongosi ake anali kum’teteza kuti asagwe m’ciyeso ndi kucita chimo. (Nyimbo 1:6; 2:10-15) Ngati muli pa cisumbali, n’ciani cimene muyenela kupewa kuti musacite ciwelewele? Muyenela kudziŵa pasadakhale zinthu zimene muyenela kupewa kuti cisumbali canu cikhalebe coyela. Muyenelanso kupewa kukhala aŵiliŵili pa malo obisika. Mungasonyezane cikondi, koma mwa njila yoyenela.
17, 18. Kodi mwapindula bwanji kuphunzila Nyimbo ya Solomo?
17 Yehova amafuna kuti cikwati cikhale cokhalitsa ndipo amafunanso kuti okwatilana azikondana. N’kosavuta kwa io kukondana akangoloŵa m’cikwati. Koma kuti cikwati cao cikhalitse, io ayenela kulimbitsa cikondi cao monga lawi la moto limene silizima.—Maliko 10:6-9.
18 Ngati mufuna kuloŵa mu cikwati, pezani munthu amene mudzakonda kwambili. Munthuyo mukamupeza, nonse aŵili muyenela kucita khama kuti cikondi canu cilimbe. Monga mmene taphunzilila m’Nyimbo ya Solomo, cikondi ceniceni ndi cotheka cifukwa ndi “lawi la Ya.”—Nyimbo 8:6.
^ par. 2 Onani Nsanja ya Olonda January 15, 2007, tsamba 31.