NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA September 2014

Magazini ino ili ndi nkhani zophunzila za October 27 mpaka November 30, 2014.

Kodi Mukukalamila Udindo?

Kodi kukalamila koyenela ndi kuti?

Kodi Mumakhulupilila Kuti Muli ndi Coonadi? N’cifukwa Ciani?

Nkhani ino ifotokoza zifukwa zimene anthu ambili amakhulupilila kuti Mboni za Yehova zili ndi coonadi. Idzafotokozanso zifukwa zimene zimacititsa Mboni kukhulupilila kuti zili ndi coonadi.

Tumikilani Mulungu Mokhulupilika Panthawi ya “Masautso Ambili”

Tonse timakumana ndi mavuto cifukwa cokhala m’dziko la Satana. Ndi njila ziti zimene Satana amagwilitsila nchito poukila? Tingakonzekele bwanji masautso amenewo?

Makolo—Ŵetani Ana Anu

Makolo ali ndi udindo wolela ana ao “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aefeso 6:4) Nkhani ino ifotokoza mbali zitatu zimene makolo angacite poŵeta ana ao ndi kuwathandiza kukonda Yehova.

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Kodi zimene Baibulo limakamba pa Salimo 37:25 ndi pa Mateyu 6:33, zitanthauza kuti Yehova sadzalola Mkristu kusoŵa cakudya?

Imfa, Mdani Wotsilizila, Idzaonongedwa

Imfa ndi zonse zimene zimacititsa kuti tizifa zabweletsa mavuto aakulu. N’cifukwa ciani anthu amafa? Kodi imfa, mdani wotsilizila, idzaonongedwa motani? (1 Akorinto 15:26) Onani mmene mayankho akuunikila cilungamo ca Yehova, nzelu zake, ndi cikondi cake makamaka.

Muzikumbukila Amene Ali mu Utumiki Wanthawi Zonse

Olambila ambili a Yehova amagwila nchito mwakhama. Tingacitenji kuti tizikumbukila ‘nchito zao zacikhulupililo’ ndi ‘nchito zao zacikondi’?—1 Atesalonika 1:3.