Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tiziyamikila Kukoma Mtima Kwakukulu Kumene Tinalandila

Tiziyamikila Kukoma Mtima Kwakukulu Kumene Tinalandila

“Tonsefe tinalandila . . . kukoma mtima kwakukulu kosefukila.”—YOH. 1:16.

NYIMBO: 95, 13

1, 2. (a) Fotokozani fanizo la Yesu la mwini munda wa mpesa. (b) Kodi fanizoli liwonenetsa bwanji khalidwe la kuwolowa manja ndi kukoma mtima kwakukulu?

TSIKU lina, munthu wina amene anali ndi munda wa mpesa anacelela ku msika kukasakila anthu aganyu. Anawauza malipilo amene adzawapatsa ndipo anthuwo anavomela. Koma popeza kuti mwini munda wa mpesayo anali kufuna anchito ambili, anapitanso ku msika maulendo angapo kukasakila anchito ena. Iye analonjeza kuti anchito onse adzawapatsa malipilo oyenelela, ngakhale amene anagwila nchito kwa ola limodzi. Madzulo, mwini munda wa mpesa uja anaitanitsa anchitowo kuti awapatse malipilo. Iye anali woolowa manja ndipo anapeleka malipilo ofanana kwa anchito onse, kaya anaseŵenza tsiku lonse kapena ola limodzi cabe. Koma anchito amene anaseŵenza tsiku lonse anayamba kudandaula. Mwini munda wa mpesayo anawafunsa kuti: ‘Nakupatsani malipilo amene tinapangana, si conco? Kodi n’kosaloleka kupatsa anchito anga onse malipilo amene nifuna? Kapena mwacita nsanje cifukwa cakuti ndine woolowa manja?’—Mat. 20:1-15.

2 Fanizo la Yesu limatikumbutsa khalidwe la Yehova lochulidwa kambili m’Baibulo. Khalidwe limeneli ni “kukoma mtima kwakukulu.” [1] (Ŵelengani 2 Akorinto 6:1.) Ena angaganize kuti anchito amene anaseŵenza ola limodzi anafunika kulandila ndalama yocepa kuposa enawo. Koma mwini mundayo anaonetsa khalidwe la kukoma mtima kwakukulu kwa anchito amene anaseŵenza nthawi yocepa. Pokamba za liwu limene linamasulidwa kuti “kukoma mtima kwakukulu,” katswili wina anakamba kuti: “Mau amenewa makamaka amakamba za mphatso yaulele imene yapatsidwa kwa munthu amene sanaiseŵenzele, ndiponso amene si woyenelela kuilandila.”

MPHATSO YAMTENGO WAPATALI YA YEHOVA

3, 4. N’cifukwa ciani Yehova anaonetsa anthu onse kukoma mtima kwakukulu? Nanga anacita bwanji zimenezo?

3 Baibulo imakamba za “mphatso yaulele ya kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (Aef. 3:7) Kodi Yehova anapeleka bwanji “mphatso yaulele” imeneyi? Nanga n’cifukwa ciani? Sembe kuti timacita zonse zimene Yehova amafuna popanda kulakwitsa ciliconse, kukoma mtima kwake kukanatiyenelela. Koma timalephela kucita zimenezo. Ndiye cifukwa cake, Mfumu yanzelu Solomo inati: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amacita zabwino zokhazokha osacimwa.” (Mlal. 7: 20) Mtumwi Paulo nayenso anakamba kuti: “Onse ndi ocimwa ndipo ndi opeleŵela pa ulemelelo wa Mulungu.” Anakambanso kuti “malipilo a ucimo ndi imfa.” (Aroma 3:23; 6:23a) Conco, cilango ca imfa cinali cotiyenela.

4 Popeza kuti Yehova amakonda anthu kwambili, anatumiza “Mwana wake wobadwa yekha” kuti adzatifele. Iyi ni njila yaikulu koposa imene Mulungu anationetsela kukoma mtima kwake kwakukulu. (Yoh. 3:16) Paulo anakamba kuti Yesu ‘anamuveka ulemelelo ndi ulemu ngati cisoti cacifumu cifukwa cakuti anazunzika mpaka imfa. Zimenezi zinamucitikila kuti mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, alaŵe imfa m’malo mwa munthu aliyense.’ (Aheb. 2:9) Zoona, “mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 6:23b.

5, 6. N’ciani cimacitika ngati tilamulidwa ndi (a) ucimo? (b) kukoma mtima kwakukulu?

5 N’cifukwa ciani ndife ocimwa ndipo timafa? Baibulo imati: “Cifukwa ca ucimo wa munthu mmodziyo [Adamu] imfa inalamulila monga mfumu” kwa mbadwa za Adamu. (Aroma 5:12, 14, 17) Komabe, cokondweletsa n’cakuti tili ndi ufulu wokana kulamulidwa ndi ucimo. Tikakhulupilila nsembe ya dipo la Khiristu, ndiye kuti tasankha kuti tizilamulidwa ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Baibulo imati: “Pamene ucimo unawonjezeka, kukoma mtima kwakukulu kunasefukilanso. Cifukwa ciani? Kuti mmene ucimo unalamulila monga mfumu pamodzi ndi imfa, momwemonso kukoma mtima kwakukulu kulamulile monga mfumu kudzela m’cilungamo. Zimenezi zicitike kuti moyo wosatha ubwele kudzela mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.”—Aroma 5:20, 21.

6 Ngakhale kuti ndife ocimwa, sitiyenela kulola ucimo kutilamulila. Cotelo, ngati tacita chimo, tiyenela kupempha Yehova kuti atikhululukile. Paulo anaticenjeza kuti: “Ucimo usakhale mbuye kwa inu, cifukwa simuli pansi pa cilamulo koma pansi pa kukoma mtima kwakukulu.” (Aroma 6:14) Conco, tili pansi pa ulamulilo wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. Kodi zimenezi zimatipindulitsa bwanji? Paulo anakamba kuti: ‘Kukoma mtima kwakukulu [kwa Mulungu] . . . kwatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, acilungamo ndi odzipeleka kwa Mulungu m’nthawi ino.’—Tito 2:11, 12.

KUKOMA MTIMA KWAKUKULU “KUMENE WAKUSONYEZA M’NJILA ZOSIYANA-SIYANA”

7, 8. Kodi Malemba atanthauza ciani pamene akamba kuti Yehova wasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu “m’njila zosiyanasiyana?” (Onani zithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

7 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Molingana ndi mphatso imene aliyense walandila, igwilitseni nchito potumikilana monga oyang’anila abwino amene alandila kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kumene wakusonyeza m’njila zosiyanasiyana.” (1 Pet. 4:10) Kodi lembali litanthauza ciani? Litanthauza kuti pa mavuto alionse amene tingakumane nao, Yehova adzatipatsa mphamvu zofunikila kuti tikwanitse kupilila. (1 Pet. 1:6) Iye adzatipatsa ciliconse cofunikila n’colinga cakuti tisagonje tikakumana ndi ciyeso.

8 Kukamba zoona, Yehova wationetsa kukoma mtima kwake kwakukulu m’njila zosiyana-siyana. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Tonsefe tinalandila zinthu kucokela pa zoculuka zimene ali nazo. Tinalandila kukoma mtima kwakukulu kosefukila.” (Yoh. 1:16) Popeza kuti Yehova amaonetsa kukoma mtima kwake kwakukulu m’njila zosiyana-siyana, timalandila madalitso ambili. Kodi ena mwa madalitso amenewa ni ati?

9. Timapindula bwanji ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova? Nanga tingaonetse bwanji kuti timayamikila?

9 Mulungu amatikhululukila macimo. Cifukwa ca kukoma mtima kwake kwakukulu, Yehova amatikhululukila macimo. Koma amacita zimenezo ngati ndife olapa, ndipo tikuyesetsa kulimbana ndi zilakolako zoipa. (Ŵelengani 1 Yohane 1:8, 9.) Tiyenela kuyamikila Mulungu ndi kum’tamanda cifukwa ca cifundo cake. Paulo analembela Akhiristu anzake odzozedwa kuti: “[Yehova] anatilanditsa ku ulamulilo wa mdima, n’kutisamutsila mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Mwana wakeyo, tinamasulidwa ndi dipo, kutanthauza kuti macimo athu anakhululukidwa.” (Akol. 1:13, 14) Popeza kuti Mulungu amatikhululukila macimo, tilinso na mwayi wolandila madalitso ena ambili-mbili.

10. Ni mwayi wabwanji umene tili nawo cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?

10 Timakhala pa unansi wabwino na Mulungu. Ife anthu timabadwa tili kale pa udani ndi Mulungu. Komabe, Paulo anati: “Pamene tinali adani, tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzela mu imfa ya Mwana wake.” (Aroma 5:10) Kuyanjanitsidwa kumeneko kunatithandiza kuti tikhale pamtendele ndi Yehova. Paulo anagwilizanitsa mwayi umenewu ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova pamene anauza odzozedwa anzake kuti: “Cotelo, popeza tsopano tayesedwa olungama cifukwa cokhala ndi cikhulupililo, tiyeni tikhale pa mtendele ndi Mulungu kudzela mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. Mwa ameneyunso, ndiponso cifukwa ca cikhulupililo, takhala ndi ufulu woloŵa m’kukoma mtima kwakukulu, mmene tilimo tsopano.” (Aroma 5:1, 2) Umenewu ni mwayi wa mtengo wapatali.

Mmene Mulungu waonetsela kukoma mtima kwake kwakukulu: Mwayi womvela uthenga wabwino (Onani ndime 11)

11. Kodi odzozedwa amathandiza bwanji a “nkhosa zina” kukhala olungama?

11 Timaonedwa olungama pamaso pa Mulungu. Ife tonse timabadwa osalungama. Mneneli Danieli analemba kuti m’nthawi ya mapeto, “anthu ozindikila,” kapena kuti odzozedwa, ‘adzathandiza anthu ambili kukhala olungama.’ (Ŵelengani Danieli 12:3.) Kodi odzozedwa amacita bwanji zimenezi? Amacita zimenezi mwa kulalikila uthenga wabwino ndi kuphunzitsa a “nkhosa zina” mamiliyoni ambili njila za Yehova. (Yoh. 10:16) Zimenezi zatheka cabe cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova. Paulo anafotokoza kuti: “Kuyesedwa olungama cifukwa ca kukoma mtima kwake kwakukulu kumene [Mulungu] wakusonyeza, powamasula ndi dipo lolipilidwa ndi Khristu Yesu, kuli ngati mphatso yaulele.”—Aroma 3:23, 24.

Mphatso ya pemphelo (Onani ndime 12)

12. Kodi pemphelo ligwilizana bwanji ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?

12 Tili na mwayi wopemphela kwa Mulungu. Cifukwa ca kukoma mtima kwake kwakukulu, Yehova anatipatsa mwayi wokamba naye m’pemphelo. Paulo anacha mpando wacifumu wa Yehova kuti “mpando wacifumu wa kukoma mtima kwakukulu,” ndipo anatilimbikitsa kuti tiyenela kupemphela kwa iye “ndi ufulu wa kulankhula.” (Aheb. 4:16a) Yehova anatipatsa mwayi wopemphela kwa iye kupitila mwa Mwana wake, amene “kudzela mwa iye, tili ndi ufulu wa kulankhula ndiponso njila yofikila Mulungu popanda kukayikila pokhala ndi cikhulupililo mwa Yesuyo.” (Aef. 3:12) Kukamba zoona, kupemphela kwa Yehova ni njila yaikulu kwambili imene waonetsela kukoma mtima kwakukulu.

Kulandila thandizo pa nthawi yoyenela (Onani ndime 13)

13. Tingapindule bwanji ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu “pa nthawi imene tikufunika thandizo”?

13 Timapeza thandizo pa nthawi yoyenela. Paulo anatilimbikitsa kupemphela kwa Yehova nthawi iliyonse imene tifuna, “kuti aticitile cifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:16b) Nthawi iliyonse tikakumana ndi ciyeso kapena mavuto ena, tingapemphe Yehova kuti atithandize. Ngakhale kuti ndife ocimwa, iye amayankha mapemphelo athu. Nthawi zambili amacita zimenezi kupitila mwa abale ndi alongo athu, kuti ‘tikhale olimba mtima ndithu ndi kukamba kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandicite ciani?’’—Aheb. 13:6.

14. Kodi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova kumatithandiza bwanji?

14 Timalimbikitsidwa. Mwayi wina waukulu umene timapeza cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova, ni cilimbikitso cimene amapeleka tikavutika maganizo. (Sal. 51:17) Pamene Akhiristu a ku Tesalonika anali kuzunzidwa, Paulo anawalembela kalata ndi kuwauza kuti: “Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyo, ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ndipo amatilimbikitsa m’njila yosalephela ndiponso anatipatsa ciyembekezo cabwino, mwa kukoma mtima kwakukulu, alimbikitse mitima yanu ndi kukulimbikitsani.” (2 Ates. 2:16, 17) N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti Yehova amatikonda ndi kutisamalila cifukwa ca kukoma mtima kwake.

15. Ni ciyembekezo ca bwanji cimene tili naco cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?

15 Tili na ciyembekezo ca moyo wosatha. Popeza ndife ocimwa, sitingakhale na ciyembekezo ciliconse. (Ŵelengani Salimo 49:7, 8.) Koma Yehova watipatsa ciyembekezo cosangalatsa. Yesu analonjeza otsatila ake kuti: “Cifunilo ca Atate wanga ndi cakuti, aliyense woona Mwana ndi kukhulupilila mwa iye akhale nawo moyo wosatha.” (Yoh. 6:40) Zoona, ciyembekezo ca moyo wosatha ni mphatso yoonetsa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. Paulo anayamikila mfundo imeneyi, ndipo anakamba kuti: “Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake kwakukulu kumene kumabweletsa cipulumutso kwa anthu, kaya akhale a mtundu wotani.”—Tito 2:11.

MUSATENGE KUKOMA MTIMA KWAKUKULU KWA MULUNGU KUKHALA CIFUKWA COCITILA MACIMO

16. Kodi Akhiristu ena akale ananyoza bwanji kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?

16 N’zoona kuti timalandila madalitso ambili cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova. Komabe, sitiyenela kuganiza kuti iye amalekelela makhalidwe oipa. Akhiristu ena akale ‘anatenga kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu . . . kukhala cifukwa cocitila khalidwe lotayilila.’ (Yuda 4) Akhiristu osakhulupilika amenewa anali kuganiza kuti angacimwe mmene afunila, ndipo Yehova adzapitiliza kuwakhululukila. Coipa kwambili n’cakuti iwo anayamba kukopa Akhiristu anzawo kuti nawonso azicita zimenezo. Ngakhale masiku ano, aliyense wocita zimenezi ‘amanyoza mzimu wa Mulungu, yemwe amasonyeza kukoma mtima kwakukulu.’—Aheb. 10:29.

17. Ni malangizo a mphamvu ati amene Petulo anapeleka?

17 Masiku ano, Satana wapangitsa Akhiristu ena kuganiza kuti angacimwe mmene afunila ndipo Yehova adzapitiliza kuwakhululukila. N’zoona kuti Yehova amakhululukila ocimwa amene alapa, koma amafuna kuti tiziyesetsa kulimbana ndi zilakolako zathu za ucimo. Ndiye cifukwa cake anauzila Petulo kulemba kuti: “Inu okondedwa, popeza mukudziŵilatu zimenezi, cenjelani kuti musasocele pokopeka ndi zolakwa za anthu ophwanya malamulowo, kuopela kuti mungalephele kukhala olimba ndipo mungagwe. Ndithu musatelo ayi, koma pitilizani kulandila kukoma mtima kwakukulu ndi kumudziŵa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khiristu.”—2 Pet. 3:17, 18.

KUKOMA MTIMA KWAKUKULU KUMABWELETSA UDINDO

18. Ni udindo wa bwanji umene tili nawo cifukwa ca kukoma mtima kwa Yehova?

18 Timayamikila kwambili Yehova kaamba ka kukoma mtima kwake kwakukulu. Motelo, tiyenela kuseŵenzetsa mphamvu zathu pomutamanda ndi kuthandiza ena. Nanga tingacite bwanji zimenezi? Paulo anakamba kuti: “Cotelo, popeza kuti tili ndi mphatso zosiyana-siyana mogwilizana ndi kukoma mtima kwakukulu kumene tinapatsidwa, . . . ngati tili ndi mphatso ya utumiki, tiyeni ticitebe utumikiwo. Amene akuphunzitsa, aziphunzitsa ndithu. Wocenjeza, aike mtima wake pa kucenjeza. . . . Wotsogolela, atsogolele mwakhama. Ndipo wosonyeza cifundo, acite zimenezo mokondwa.” (Aroma 12:6-8) Popeza kuti Yehova wationetsa kukoma mtima kwakukulu, tili ndi udindo wogwila nchito mwakhama mu ulaliki, wophunzitsa ena Baibulo, wolimbikitsa abale ndi alongo athu, ndi kukhululukila aliyense amene watilakwila.

19. Kodi m’nkhani yotsatila tidzakambilana za udindo uti?

19 Popeza kuti Yehova wationetsa kukoma mtima kwake kwakukulu, tiyeni tizicita zilizonse zimene tingathe kuti ‘ticitile umboni mokwanila za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.’ (Mac. 20:24) M’nkhani yotsatila, tidzakambilana za udindo wathu umenewu.

^ [1] (ndime 2) Onani mau akuti “Kukoma mtima kwakukulu” pa cigawo cakuti “Matanthauzo a Mau Ena” mu Baibulo la Dziko Latsopano.