Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi Yesu anatanthauza ciyani pokamba kuti: “Musaganize kuti ndinabweletsa mtendele”?

▪ Yesu anali kulalikila uthenga wamtendele. Ngakhale n’conco, iye pa nthawi ina anauza atumwi ake kuti: “Musaganize kuti ndinabweletsa mtendele padziko lapansi, sindinabweletse mtendele koma lupanga. Pakuti ndinabwela kudzagawanitsa anthu. Ndinabwela kudzacititsa munthu kutsutsana ndi bambo ake, mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake, ndiponso mtsikana wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi.” (Mat. 10:34, 35) Kodi apa anatanthauza ciyani?

Yesu sanali na colinga cofuna kugaŵanitsa mabanja ayi. Koma anadziŵa kuti ziphunzitso zake zidzagaŵanitsa mabanja ena. Conco, amene akufuna kukhala otsatila a Khristu na kubatizika, ayenela kudziŵa kuti adzakumana na mavuto pa cisankho cawo. Iwo angatsutsidwe na mnzawo wa m’cikwati wosakhulupilila kapena acibale ena. Zimenezo zingapangitse kuti cikhale cowavuta kutsatilabe ziphunzitso za Khristu.

Baibo imalimbikitsa Akhristu kuti azikhala “mwamtendele ndi anthu onse.” (Aroma 12:18) Koma ziphunzitso za Yesu zimakhala ngati “lupanga” ku mabanja ena. Izi zimacitika ngati wina m’banja wavomeleza ziphunzitso za Yesu koma ena akutsutsana nazo. Zikatelo, acibale kapena kuti a m’banja amenewo, amakhala “adani” a munthu amene akuphunzila coonadi.—Mat. 10:36.

Ophunzila a Khristu amene acibale awo amapita ku cipembedzo cina, nthawi zina amakumana na zocitika zimene zingaike cikondi cawo pa Yehova na Yesu pa mayeso. Mwacitsanzo, acibale osakhulupilila angawakakamize kuti akondwelele nawo holide ya cipembedzo. Zikakhala conco, ayenela kusankha amene adzakondweletsa. Yesu anati: “Amene amakonda kwambili bambo ake kapena mayi ake kuposa ine sali woyenela ine.” (Mat. 10:37) Yesu sanatanthauze kuti ophunzila ake acepetse cikondi cawo pa makolo awo. M’malo mwake, anali kuwaphunzitsa kuti ayenela kuika patsogolo zinthu zofunika kwambili pa umoyo wawo. Ngati acibale osakhulupilila safuna kuti tizilambila Yehova, sitileka kuwakonda, koma timadziŵa kuti kukonda Mulungu ndiko kofunika koposa.

Kukamba zoona, kutsutsidwa na acibale kungakhale koŵaŵa. Koma ophunzila a Yesu amakumbukilabe mawu ake akuti: “Aliyense wosalandila mtengo wake wozunzikilapo ndi kunditsatila sali woyenela ine.” (Mat. 10:38) M’mawu ena, Akhristu amaona kuti citsutso cocokela kwa acibale ni limodzi mwa mavuto amene ayenela kuwapilila. Panthawi imodzimodzi, amayembekezela kuti khalidwe lawo labwino lidzalimbikitsa acibale awo kusintha maganizo awo, na kuyamba kumvetsela uthenga wa m’Baibo.—1 Pet. 3:1, 2.