Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Napeza Cimwemwe Potumikila Yehova

Napeza Cimwemwe Potumikila Yehova

NCHITO yanga yoyamba pa Beteli ku Canada inali kupyela m’cipinda copulintila mabuku. Umu munali m’caka ca 1958, ndipo n’nali na zaka 18. Umoyo unali kuyenda bwino, ndipo posapita nthawi n’nayamba kuseŵenzela pa makina amene anali kudulila magazini m’mbali akacoka kowapulinta. N’nali wokondwela zedi kutumikila pa Beteli!

Caka cotsatila, analengeza ku banja la Beteli kuti pakufunika anchito odzifunila ku nthambi ya South Africa, cifukwa kunabwela makina atsopano opulintila. N’nalembetsa dzina langa, ndipo n’nakondwela kuti ananisankha kupita. Abale enanso atatu anasankhidwa—m’bale Dennis Leech, m’bale Bill McLellan, na m’bale Ken Nordin. Anatiuza kuti tidzakhala ku South Africa mpaka kale-kale!

N’natumila foni amayi na kuwauza kuti: “Amayi, pali zimene nifuna kukuuzani. Niyenda ku South Africa!” Amayi anga anali a phee, osakamba-kamba. Koma anali munthu wauzimu wa cikhulupililo colimba. Iwo sanakambe zambili, koma n’nadziŵa kuti agwilizana na cisankho canga. Olo kuti amayi na atate anakwinyilila kuti n’dzakhala nawo kutali, sanadandaule na cisankho cimene n’napanga.

ULENDO WA KU SOUTH AFRICA UNAPSA!

Mu 1959, nili pa ulendo wocokela ku Cape Town kupita ku Johannesburg pamodzi na m’bale Dennis Leech, m’bale Ken Nordin, komanso m’bale Bill McLellan

Mu 2019, tonse anayi titakumananso pa nthambi ya South Africa patapita zaka 60

Coyamba, ife abale anayi tinapita ku Beteli ya ku Brooklyn kukaphunzila kwa miyezi itatu moseŵenzetsela makina atsopano opulintila. Pambuyo pa maphunzilowo, tinakwela sitima ya pamadzi kupita ku Cape Town, South Africa, apo n’kuti nangokwanitsa zaka 20. Kenako m’madzulo tinayenda ulendo wautali pa sitima kucoka ku Cape Town kupita ku Johannesburg. M’maŵa mwake, tinakaima m’tauni inayake m’dela la Karoo. M’tauni imeneyi munali fumbi kwambili komanso kunali kotentha. Tonse anayi titasuzila pawindo, tinadabwa kuona malo otelo. Tinayamba kudela nkhawa mmene utumiki wathu watsopano udzakhalila. Patapita zaka, tinali kupitako ku matauni amenewa, ndipo tinaona kuti anali malo abwino komanso abata.

Kwa zaka zingapo, n’nali kuseŵenzela pa makina opulintila ochedwa Linotype, amene anali kupulinta magazini a Nsanja ya Mlonda na Galamuka! Ofesi ya nthambi inali kupulinta magazini amenewa m’zinenelo zoculuka za ku maiko ambili a kumpoto kwa Africa. Tinali okondwela kwambili kuona kuti makina opulintila amenewa anali kugwilitsidwa nchito mokwanila.

Patapita nthawi, n’nayamba kuseŵenzela mu ofesi ya fakitale imene inali kusamalila nchito zosiyana-siyana monga kupulinta, kutumiza mabuku, na kumasulila. N’nali na zocita zambili, ndipo umoyo wanga unali wokhutilitsa.

CIKWATI NA UTUMIKI WATSOPANO

Ine na Laura tili apainiya apadela mu 1968

Mu 1968, n’nakwatila mlongo mpainiya dzina lake Laura Bowen, amene anali kukhala pafupi na Beteli. Iye anali kuthandizila pa nchito yotaipa m’dipatimenti yomasulila mabuku pa Beteli. Masiku amenewo, sanali kulola anthu okwatilana kutumikila pa Beteli, conco anatiuza kukacita upainiya wapadela. N’nali na nkhawa. N’nali n’tatumikila pa Beteli kwa zaka 10, ndipo nthawi yonseyi tinali kupatsidwa cakudya na malo ogona. Koma kodi tikanakwanitsa bwanji kupeza zofunikila pa umoyo na ndalama yocepa imene apainiya apadela anali kupatsidwa? Mwezi uliwonse, aliyense anali kupatsidwa ndalama zokwana 25 rand (imene panthawiyo anali madola 35 a ku America). Tinali kupatsidwa ndalamayi pokhapo ngati takwanitsa maola ofunikila, maulendo obwelelako, komanso kugaŵila zofalitsa. Pa ndalamayi, tinali kufunika kulipila lendi, kugulila cakudya, mayendedwe, cithandizo ca kucipatala, na zofunikila zina.

Tinatumizidwa kukacita upainiya wapadela kufupi na mzinda wa Durban, ku nyanja ya Indian Ocean. Kunali ciŵelengelo coculuka ca amwenye, amene ambili mwa iwo anali mbadwa za anthu ogwila nchito m’minda ya nzimbe m’ma 1875. Anthu amenewa anali kugwila nchito zosiyana-siyana. Ngakhale n’conco, iwo anasungabe cikhalidwe cawo, komanso zakudya za kwawo. Ndipo anali kukamba Cizungu, zimene zinakhala zosavuta kwa ife kuwalalikila.

Panthawiyo, apainiya apadela anali kufunika kukwanitsa maola 150 mwezi uliwonse. Conco, ine na mkazi wanga Laura tinakonza zakuti tsiku loyamba tilalikile kwa maola 6. Kunali kotentha kwambili. Tinalibe maulendo obwelelako na maphunzilo. Motelo, kwa maola 6 tinali kucita ulaliki wa nyumba na nyumba. Pambuyo pakuti talalikilako, n’nayang’ana pa nkoloko. N’nadabwa kuona kuti tangolalikilako kwa mphindi 40. Mu mtima n’nati, kodi tidzakwanitsa kucita upainiya wapadela?

Posakhalitsa, tinaika zinthu m’malo. Tsiku lililonse, tinali kunyamulako cakudya mu ulaliki. Tikafuna kupumula, tinali kuimika motoka yathu munsi mwa mtengo. Ndipo nthawi zina, ana acimwenye anali kutizungulila n’kumatiyang’ana mwacidwi. Patapita masiku angapo, tinaona kuti pambuyo polalikila kwa maola aŵili kapena atatu, tsiku linali kutha mofulumila.

Zinali zokondweletsa kwambili kuthandiza anthu oolowa manja m’gawo limeneli kuphunzila coonadi. Tinapeza kuti amwenye ni anthu aulemu, okoma mtima, komanso oopa Mulungu. Ahindu ambili anali kumvetsela uthenga wathu. Iwo anali kukonda kuphunzila za Yehova, Yesu, Baibo, dziko latsopano la mtendele, komanso za ciyembekezo ca kuuka kwa akufa. Patapita caka, tinakhala na maphunzilo a Baibo 20. Tsiku lililonse, tinali kudya cakudya pamodzi na banja limene tinali kuphunzila nalo. Tinali okondwela ngako.

Posapita nthawi, tinalandila utumiki wina. Tinapatsidwa nchito ya m’dela kufupi na gombe la nyanja ya Indian Ocean. Mlungu na mlungu, tinali kukhala alendo m’nyumba za abale pamene tinali kucezela mipingo kuti tiilimbikitse, na kuseŵenza na ofalitsa mu ulaliki. Tinali banja limodzi, ndipo tinali kusangalala kuseŵela na ana awo komanso agalu kapena acona. Pambuyo potumikila zaka ziŵili, mosayembekezela tinalandila foni kucokela ku ofesi ya nthambi. Anatiuza kuti, “Tifuna kuti mubwele kudzatumikilanso kuno ku Beteli.” N’nawayankha kuti, “Mudziŵa, tikusangalala na utumiki wathu kuno.” Koma zoona zake n’zakuti tinali okonzeka kupita kulikonse kumene angatitumize.

KUBWELELANSO KU BETELI

Pa Beteli n’nali kutumikila ku Service Department, ndipo n’nali na mwayi woseŵenza na abale ambili okhwima kuuzimu. Pa nthawiyo, mpingo uliwonse unali kulandila kalata kucokela ku nthambi yozikidwa pa lipoti limene wadela anali kutumiza pambuyo pocezela mpingo. Akalembela anali na nchito yaikulu yomasulila lipoti la wadela kucotsa m’cinenelo ca Xhosa, Cizulu, na zinenelo zina kupeleka m’Cizungu. Ndiyeno anali kumasulilanso kucotsa m’Cizungu kupeleka m’zinenelo zina za mu Africa. N’nali kuwayamikila kwambili omasulila akhama amenewo, cifukwa ananithandiza kudziŵa mavuto amene abale na alongo a ku Africa anali kukumana nawo.

Panthawiyo, boma la South Africa linali kulimbikitsa khalidwe la kusankhana mitundu. Anthu a mitundu yosiyana sanali kukhalila pamodzi, conco sanali kuyendelana. Abale athu akuda anali kukamba zinenelo zawo, kulalikila m’zinenelo zawo, komanso kusonkhana m’mipingo ya zinenelo zawo.

Sin’nali kudziŵana na abale ambili akuda, cifukwa n’nali kutumikila m’gawo la anthu okamba Cizungu. Koma zinthu zitasintha, n’nakhala na mwayi wophunzila cikhalidwe na miyambo ya anthu akuda. N’nadziŵa mavuto amene abale anali kukumana nawo, pokakamizidwa kucita miyambo yacikunja na zikhulupililo za cipembedzo. Iwo analimba mtima kwambili kuti awonjoke ku miyambo yosagwilizana na malemba. Analimbanso mtima pamene anali kutsutsidwa na a m’banja lawo na anthu a m’midzi cifukwa cokana kucita zamizimu. Ku madela a kumidzi, anthu anali osauka kwambili. Ambili anali osaphunzila, koma anali kulemekeza Baibo.

N’nali na mwayi wothandizila pankhani zina zokhudza ufulu wathu wa kulambila, komanso kusatengela mbali m’zandale. Cikhulupililo cathu cinalimba titaona kukhulupilika na kulimba mtima kwa Mboni zacicepele, zimene zinacotsedwa sukulu cifukwa cokana kucita nawo mapemphelo na kuimba nyimbo za fuko.

Abale athu anakumana na mavuto ena m’dziko la Swaziland. Pamene Mfumu Sobhuza Waciŵili anamwalila, nzika zonse zinayenela kucita mwambo wa malilo. Amuna anafunika kumeta mpala, ndipo akazi anafunika kuthepula tsitsi lawo. Abale na alongo ambili anazunzidwa cifukwa cokana kucita nawo mwambo umenewu wogwilizana na kulambila mizimu ya makolo. Kukhulupilika kwawo kwa Yehova kunatikondweletsa kwambili! Tinaphunzila zambili kwa abale athu akuda pa kukhulupilika na kuleza mtima kwawo, ndipo izi zinalimbitsa cikhulupililo cathu.

KUBWELELANSO KU NCHITO YOPULINTA

Mu 1981, n’nayambanso kugwila nchito yopulinta poseŵenzetsa makompyuta. Inali nthawi yokondweletsa ngako! Njila zopulintila zinali kusintha. Mwamuna wina woseŵenza pa kampani inayake anapatsa nthambi makina atsopano opulintila kuti tiwayese popanda kulipila ndalama iliyonse. Makina 9 akale a Linotype amene tinali kuseŵenzetsa analoŵedwa m’malo na makina 5 atsopano amene tinapatsidwa. Conco, tinayamba kupulinta mabuku ambili kuposa kale.

Makompyuta anathandizanso kupeza njila zatsopano zolinganizila mawu pa masamba mwa kuseŵenzetsa MEPS. Zipangizo zamakono zapita patsogolo kwambili kucokela nthawi imene tinabwela ku South Africa. (Yes. 60:17) Tonse anayi tinakwatila alongo abwino, amene anali apainiya okonda zinthu zauzimu. Ine na m’bale Bill tinali kutumikilabe pa Beteli. Koma m’bale Ken na Dennis anayamba kukhala na ŵana.

Nchito pa nthambi zinali kuwonjezeleka. Mabuku ophunzilila Baibo anali kuwamasulila na kuwapulinta m’zenenelo zambili. Kenako anali kuwatumiza ku nthambi zina. Conco panafunika kuwonjezela nyumba zina za Beteli. Abale anamanga nyumba ya Beteli kumadzulo kwa mzinda wa Johannesburg, ndipo anaipatulila mu 1987. Zinali zokondweletsa kwambili kwa ine kugwila nawo nchitoyo, komanso kutumikila m’Komiti ya Nthambi ku South Africa kwa zaka zambili.

UTUMIKI WINANSO WATSOPANO!

Mu 2001, sitinakhulupilile pamene ananiitana kuti nikatumikile m’Komiti ya Nthambi yokhazikitsidwa kumene ku United States. Olo kuti tinakwinyilila kusiya utumiki wathu na anzathu ku South Africa, tinakondwela zedi kuyamba umoyo watsopano monga ziwalo za banja la Beteli la United States.

Ngakhale n’conco, tinali na nkhawa kusiya amayi a mkazi wanga okalamba. Sitikanakwanitsa kuwasamalila mokwanila pamene tinali ku New York, koma azibale atatu a mkazi wanga anadzipeleka kuti adzayamba kuwapezela zofunikila pa umoyo. Iwo anati: “Tonse sitingakhale mu utumiki wa nthawi zonse, koma ngati ife kuno tisamalila amayi, zidzakuthandizani kupitiliza utumiki wanu.” Timawayamikila kwambili.

Panthawi imodzi-imodzi, mkulu wanga na mkazi wake, amene akhala ku Toronto, Canada, anali kusamalila amayi anga amasiye. Panthawiyo, anali atakhala nawo zaka zoposa 20. Timayamikila cikondi na cisamalilo cimene anali kuwapatsa mpaka imfa yawo, pasanapite nthawi yaitali kucokela pamene tinafika ku New York. Ni dalitso lalikulu kukhala na banja logwilizana limene n’lokonzeka kusintha zina na zina, kuti lisamalile makolo okalamba, kumene nthawi zina kumakhala kovuta.

Kwa zaka, n’natumikila m’dipatimenti yokonza mabuku, ndipo masiku ano nchitoyi yapepuka cifukwa ca kupita patsogolo kwa zipangizo zamakono. Caposacedwapa, nakhala nikutumikila m’Dipatimenti Yogula Zinthu. Kwa zaka 20 zapitazo, unali mwayi waukulu kwa ine kukhala m’banja lalikulu la Beteli, la anthu pafupifupi 5,000, komanso atumiki a pa Beteli oyendela pafupifupi 2,000.

Zaka 6 zapitazo, sin’naganizileko zakuti ningakhale kuno. Mkazi wanga Laura wakhala akunicilikiza na mtima wonse kwa zaka zonsezi. Nakhala na umoyo wabwino kwambili! Timayamikila mautumiki osiyana-siyana amene tinacitako, komanso abale na alongo amene taseŵenza nawo, kuphatikizapo awo amene tinadziŵana nawo poyendela nthambi zambili padziko lonse. Popeza lomba nili na zaka zoposa 80, nimaseŵenza nchito zocepa, cifukwa pali abale acinyamata amene amagwila nchito zimenezo.

Wamasalimo anati: “Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Sal. 33:12) Mawu amenewa ni oona. Niyamikila kwambili kutumikila Yehova pamodzi na anthu ake acimwemwe.