Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 3

NYIMBO 35 ‘Tsimikizilani Zinthu Zofunika Kwambili’

Pangani Zisankho Zokondweletsa Yehova

Pangani Zisankho Zokondweletsa Yehova

“Kuopa Yehova ndi ciyambi ca nzelu, ndipo ngati ungadziwe Mulungu, yemwe ndi Woyela Koposa, udzakhala womvetsa zinthu.”​—MIY. 9:10.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mmene tingagwilitsile nchito cidziwitso, kumvetsa zinthu, komanso kuzindikila kuti tipange zisankho zanzelu.

1. Ndi cinthu covuta citi cimene tonse tiyenela kucita pa umoyo wathu?

 TSIKU LILILONSE timafunikila kupanga zisankho. Zisankho zina monga kusankha cakudya cam’mawa kapena nthawi yopita kukagona ndi zosavuta kupanga. Koma zina zimakhala zovuta. Zisankhozo zingakhudze thanzi lathu, cimwemwe cathu, okondedwa athu kapena ubwenzi wathu ndi Yehova. Timafuna kuti zisankho zimene tapanga zitipindulile ife eni komanso a m’banja mwathu. Koma koposa zonse, timafuna kuti zisankho zathu zizikondweletsa Yehova.​—Aroma 12:​1, 2.

2. Ndi masitepe ati angakuthandizeni kupanga zisankho zanzelu?

2 Cimakhala cosavuta kupanga zisankho zanzelu ngati (1) mwadziwa zenizeni zokhudza cisankhoco, (2) mwaganizila mmene Yehova amaonela nkhaniyo, komanso (3) mwaika zisankho zanu pa sikelo. M’nkhani ino, tikambilane masitepe atatu amenewa, ndipo tione mmene tingaphunzitsile mphamvu zathu za kuzindikila.​—Miy. 2:11.

DZIWANI ZENIZENI ZOKHUDZA CISANKHO CIMENE MUFUNA KUPANGA

3. Pelekani citsanzo coonetsa cifukwa cake muyenela kupeza mfundo zonse musanapange cisankho.

3 Sitepe yoyamba imene munthu ayenela kutsatila kuti apange cisankho canzelu ndi kudziwa zoona zake zokhudza nkhaniyo. Zimenezi n’zofunika cifukwa ciyani? Tiyelekeze kuti munthu wapita kwa dokotala kukafunsa za matenda aakulu amene ali nawo. Kodi dokotala angapeleke mankhwala kwa munthuyo asanamupime kapena kumufunsako mafunso? Kutalitali! Mofanana ndi dokotala wabwino, inunso mungapange zisankho zanzelu ngati coyamba mumaganizila mfundo zonse zimene mwapeza zokhudzana ndi cisankho cimene mufuna kupanga. Mungacite bwanji zimenezi?

4. Malinga ndi Miyambo 18:​13, mungacite ciyani kuti mudziwe zoona zokhudza nkhani inayake? (Onaninso cithunzi.)

4 Nthawi zambili, mungadziwe zoona za nkhani inayake mwa kufunsa mafunso. Tinene kuti mwaitanidwa ku maceza enaake. Kodi muyenela kupita? Ngati simum’dziwa bwino munthu amene wakonza macezawo komanso zimene walinganiza, mungafunikile kumufunsa mafunso monga akuti: “Kodi macezawo adzacitikila kuti? Nanga adzacitika nthawi yanji? Kodi kudzakhala anthu oculuka motani? Ndani adzayang’anila macezawo? Ndani adzapezekako? Palinganizidwa zocitika zotani? Kodi kudzakhala mowa?” Mayankho a mafunso amenewa angakuthandizeni kupanga cisankho canzelu.​—Welengani Miyambo 18:13.

Dziwani zoona zake zokhudza nkhaniyo mwa kufunsa mafunso (Onani ndime 4) a


5. Kodi muyenela kucita ciyani mukamvetsa mfundo zonse?

5 Mukamvetsa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo, ganizilam’poni mosamala. Mwacitsanzo, bwanji ngati mwadziwa kuti anthu amene salemekeza mfundo za m’Baibulo adzapezeka ku macezawo, kapena ngati mowa udzagawilidwa mwacisawawa? Kodi n’kutheka macezawo angasinthe n’kukhala phwando la phokoso? (1 Pet. 4:3) Kumbali ina, bwanji ngati macezawo adzacitika pa nthawi imene mumapita kukasonkhana kapena pamene mumapita mu ulaliki? Mukamvetsa nkhani yonse, mudzakwanitsa kupanga cisankho canzelu. Koma pali sitepe ina imene muyenela kutsatila. Inuyo mwadziwa mmene mukuionela nkhaniyo, koma kodi Yehova akuiona bwanji?​—Miy. 2:6.

GANIZILANI MMENE YEHOVA AMAONELA NKHANIYO

6. Malinga ndi Yakobo 1:​5, n’cifukwa ciyani tiyenela kupemphela kwa Yehova kuti atithandize?

6 M’pempheni Yehova kuti akuthandizeni kudziwa mmene amaionela nkhaniyo. Yehova analonjeza kutipatsa nzelu zotithandiza kuzindikila ngati cisankho cinacake cingam’kondweletse kapena ayi. Iye amapeleka nzelu zimenezi “mowolowa manja kwa onse ndiponso amapeleka mosatonza.”​—Welengani Yakobo 1:5.

7. Mungadziwe bwanji kaganizidwe ka Yehova pa nkhani inayake? Pelekani citsanzo.

7 Mukapempha citsogozo kwa Yehova, khalani chelu kuti muone yankho limene wapeleka. Kuti timveketse bwino mfundoyi, tiyelekeze motele: Tinene kuti mwasocela, ndipo mwafunsa munthu wakumaloko kuti akuthandizeni kudziwa njila yotenga. Kodi mungacoke n’kumapita, munthuyo asanakuyankheni? Simungacite zimenezo! Musanacoke, mungafunike kumvetsela zimene akukuuzani. Mofananamo, mukapempha nzelu kwa Yehova, yesani kupeza yankho lake mwa kufufuza malamulo ndi mfundo za m’Baibulo zimene zigwilizana ndi nkhani yanu. Mwacitsanzo, pamene muganizila za cisankho copita kumaceza amene tawachula m’ndime 4, mungaganizile zimene Baibulo limakamba zokhudza maphwando aphokoso, mayanjano oipa, komanso za kufunika koika za Ufumu patsogolo pa zofuna zanu.​—Mat. 6:33; Aroma 13:13; 1 Akor. 15:33.

8. Mungacite ciyani mukafuna kupeza mfundo zokhudza cisankho cimene mufuna kupanga? (Onaninso cithunzi.)

8 Ngakhale n’telo, nthawi zina mungafunikile thandizo kuti mupeze mfundo zimene mukufuna. N’kutheka kuti mungapeze malangizo othandiza kwa m’bale kapena mlongo amene n’ciyambakale. Komabe, mungapindule kwambili ngati mungadzifufuzile nokha. M’zida zathu zofufuzila muli mfundo zambili zothandiza. Zida zimenezi ziphatikizapo zofalitsa monga Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova komanso lakuti Malemba Othandiza pa Moyo Wacikhristu. Muzikumbukila kuti colinga canu ndi kupanga cisankho cimene cidzakondweletsa Yehova.

Ganizilani mmene Yehova amaionela nkhaniyo (Onani ndime 8) b


9. Tingatsimikize bwanji kuti cisankho cimene tidzapanga cidzam’kondweletsa Yehova? (Aefeso 5:17)

9 Tingatsimikize bwanji kuti cisankho cimene tidzapanga cidzam’kondweletsa Yehova? Coyambilila, tiyenela kum’dziwa bwino Yehova. Baibulo limati: “Kudziwa Woyela Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.” (Miy. 9:10) Inde, kumvetsa zinthu kwenikweni kumabwela kaamba kodziwa makhalidwe a Yehova, colinga cake, komanso kudziwa zimene amakonda ndi zimene amadana nazo. Dzifunseni kuti, ‘Potengela zimene ndimadziwa zokhudza Yehova, ndi cisankho citi cimene ndingapange cimene cingam’kondweletse?’​—Welengani Aefeso 5:17.

10. N’cifukwa ciyani kutsatila mfundo za m’Baibulo n’kofunika kwambili kuposa kusangalatsa makolo kapena kutsatila cikhalidwe ca kumene timakhala?

10 Nthawi zina, kuti tikondweletse Yehova, timafunika kupanga cisankho cimene cingakhumudwitse anthu amene timakonda. Mwacitsanzo, makolo ena amene ali ndi zolinga zabwino angakakamize mwana wawo kukwatiliwa ndi munthu wacuma kapena amene angawapatse malowolo oculuka, ngakhale kuti mwamunayo si wolimba kuuzimu. N’zoona kuti iwo afuna kuti mwana wawo akasamalidwe bwino kuthupi, koma kodi ndani azikamuthandiza kupita patsogolo kuuzimu? Kodi Yehova amaiona bwanji nkhaniyo? Timapeza yankho pa Mateyo 6:33. Pa lembali, Akhristu amalimbikitsidwa “kupitiliza kufunafuna Ufumu coyamba.” Ngakhale kuti timawalemekeza makolo athu komanso anthu akudela limene timakhala, cofunika kwambili kwa ife ndi kukondweletsa Yehova.

IKANI ZOSANKHA ZANU PA SIKELO

11. Kodi ndi khalidwe liti lochulidwa pa Afilipi 1:​9, 10 limene lidzakuthandizani kuika zosankha zanu pa sikelo?

11 Mukapeza mfundo za m’Baibulo zogwilizana ndi cisankho cimene mufuna kupanga, santhulani mosamala zosankha zanu. (Welengani Afilipi 1:​9, 10.) Kuzindikila kudzakuthandizani kuona zotulukapo za cosankha ciliconse. Nthawi zina, n’cosavuta kupanga cisankho. Komabe si zisankho zonse zimene zimakhala zosavuta kupanga. Koma kuzindikila kudzakuthandizani kupanga zisankho zanzelu ngakhale pa nkhani zimene zingaoneke zovuta.

12-13. Kodi kuzindikila kudzakuthandizani bwanji kusankha nchito mwanzelu?

12 Yelekezani kuti mukufunafuna nchito imene ingakuthandizeni kusamalila banja lanu, ndipo mwapeza nchito ziwili. Kenako mukukhala pansi n’kuganizila zonse zolowetsedwamo monga mtundu wa nchitoyo, masiku ogwila nchitoyo, nthawi yopita komanso kubwelako, ndi zina zotelo. Mukuzindikilanso kuti nchito zonse ziwili siziwombana ndi mfundo za m’Baibulo. Ndiye tinene kuti pa nchito ziwilizo mwasankhapo imodzi cifukwa mwakonda mtundu wanchito, komanso malipilo ake ndi abwino ndithu. Koma pali zinthu zina zimene muyenela kuganizila musanapange cisankho.

13 Mwacitsanzo, kodi nchitoyi siziwombana ndi nthawi ya misonkhano? Kodi nchitoyi izikulepheletsani kukhala nthawi yaitali ndi banja lanu komanso kusamalila zosowa zawo zakuuzimu? Kudzifunsa mafunso ngati amenewa, kudzakuthandizani kuika “zinthu zimene ndi zofunikadi kwambili” patsogolo pa zinthu zakuthupi. Zinthu zofunikazo ndi kulambila kwanu komanso banja lanu. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kupanga cisankho cimene cingakondweletse Yehova.

14. Kodi kukhala wozindikila komanso wacikondi kudzatithandiza bwanji kupewa kukhumudwitsa ena?

14 Kuzindikila kumatisonkhezelanso kuganizila mmene cisankho cathu cingakhudzile anthu ena kuti tipewe ‘kuwakhumudwitsa.’ (Afil. 1:10) Mfundoyi ndi yofunika kumaiganizila makamaka popanga zisankho zokhudza munthu mwini monga pa nkhani ya kuvala ndi kudzikongoletsa. Mwacitsanzo, tingakonde sitayelo inayake ya kavalidwe kapena ya kudzikongoletsa. Koma bwanji ngati abale ndi alongo athu kapena anthu ena amene sitilambila nawo angakhumudwe nazo? Kuzindikila kudzatithandiza kuganizila mmene zingawakhudzile. Ngati timawakonda, tidzaika zofuna zawo patsogolo ndipo tidzakhala odzicepetsa. (1 Akor. 10:​23, 24, 32; 1 Tim. 2:​9, 10) Kucita zimenezi kudzatisonkhezela kupanga cisankho cimene cidzaonetsa kuti timawakonda anthuwo komanso kuti timawalemekeza.

15. Kodi munthu afunika kucita ciyani asanapange cisankho cacikulu?

15 Ngati mufuna kupanga cisankho cacikulu, welengelani zonse zolowetsedwamo kuti mucikwanilitse. Yesu anatiphunzitsa kuti tiyenela ‘kuwelengela mtengo wake.’ (Luka 14:​28, Buku Lopatulika) Conco, ganizilani kuculuka kwa nthawi, cuma, komanso mphamvu zimene mufunikila kuti cisankhoco cikhale copambana. Pa zocitika zina, mungafunsile kwa a m’banja mwanu kuti muone zimene aliyense wa iwo angafunike kucita pokuthandizani kuti cisankhoco cikhale copambana. N’cifukwa ciyani kucita zimenezi n’kofunika? Kucita izi kungakuthandizeni kuona pamene mufunika kusintha. Mwina kungakuthandizeninso kuona kuti pali njila ina yabwino kwambili kuposa imene munaganizila poyamba. Mukafunsila kwa a m’banja mwanu, angakuthandizeni kuti cisankho canu cikhale copambana.​—Miy. 15:22.

PANGANI CISANKHO CANZELU

16. Ndi masitepe ati amene angakuthandizeni kupanga cisankho copambana? (Onaninso bokosi lakuti “ Mmene Tingapangile Zisankho Zanzelu.”)

16 Ngati mwatsatila masitepe amene tachulawa ndiye kuti ndinu wokonzeka kupanga cisankho canzelu. Mukafuna kupanga cisankho, muzifufuza mfundo zonse zokhudzana ndi cisankhoco, ndipo muzisanthula mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kupanga cisankho cokondweletsa Yehova. Kenako muzim’pempha Yehova kuti akuthandizeni kupanga cisankho copambana.

17. Kodi cofunika n’ciyani kuti munthu apange cisankho canzelu?

17 N’kutheka kuti kumbuyoku munapangapo zisankho zanzelu. Koma muzikumbukila mfundo yakuti, kuti mupange zisankho zanzelu, muyenela kupewa kudzidalila, kudalila nzelu zanu, kapena kudalila kumvetsa kwanu zinthu. M’malomwake, muyenela kudalila nzelu zocokela kwa Yehova. Iye yekha ndiye angakupatseni cidziwitso ceniceni, kumvetsa zinthu, komanso kuzindikila, zomwe ndi zofunika kuti mukhale wanzelu. (Miy. 2:​1-5) Angakuthandizeni kupanga zisankho zimene zingam’kondweletse.​—Sal. 23:​2, 3.

NYIMBO 28 Kukhala Bwenzi la Yehova

a MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Abale ndi alongo acinyamata akukambilana za ciitanilo copita ku phwando cimene analandila pa mafoni awo.

b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mmodzi wa abalewo akufufuza asanapange cisankho cakuti kaya apite ku phwandolo kapena ayi.