Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi mudziŵa?

Kodi mudziŵa?

Sunagoge wa m’nthawi ya atumwi: Cithunzi ici cionetsa mmene sunagoge wakale anali kuonekela. Cinajambulidwa mogwilizana na mmene matongwe a sunagoge wa m’nthawi ya atumwi ku Gamla amaonekela. Matongwewo ali pa msenga wa makilomita pafupi-fupi 10 kumpoto kwa Nyanja ya Galileya.

Kodi masunagoge anayamba bwanji?

LIWU lakuti “sunagoge” linacokela ku liwu la Cigiliki limene limatanthauza “msonkhano” kapena “kukumana pamodzi.” Liwuli n’loyenelela cifukwa kucokela kale, Ayuda anali kusonkhana pamodzi m’masunagoge pofuna kulandila malangizo komanso kulambila. Malemba Aciheberi sachula mwacindunji liwu lakuti sunagoge. Koma Malemba Acigiliki Acikhristu amaonetsa kuti pofika m’nthawi ya atumwi, anthu anali atayamba kale kukumana m’masunagoge.

Akatswili ambili a Baibo, amakhulupilila kuti masunagoge anayamba pamene Ayuda anali ku ukapolo ku Babulo. Buku la Encyclopaedia Judaica limati: “Ku dziko laukapolo kumene Ayuda anali, kunalibe Kacisi. Conco, pofuna kutonthozana pa mavuto awo, nthawi na nthawi anali kukumana pa Sabata n’kumaŵelenga Malemba.” Ayuda atamasulidwa ku ukapolo, mwacionekele anapitiliza kukumana kuti azipemphela na kuŵelenga Malemba, ndipo anamanga masunagoge kulikonse kumene anakakhala.

Pofika m’nthawi ya atumwi, Ayuda okhala m’madela ozungulila nyanja ya Mediterranean, a m’cigawo conse ca Middle East, komanso a mu Israel, anali kukumana ku masunagoge kukalambila kapena kukacita zinthu zina. Pulofesa Lee Levine, wa pa yunivesite yochedwa Hebrew University of Jerusalem, anati: “[Ku sunagoge] anali kuphunzililako, kudyelako zakudya zopatulika, kuweluzilako milandu, kupelekelako zopeleka, komanso kucitilako misonkhano yandale ndi misonkhano ina.” Iye anakambanso kuti: “Koma colinga cacikulu cinali kupemphelelako.” Conco, n’zosadabwitsa kuti nthawi zambili Yesu anali kupita kukasonkhana ku masunagoge. (Maliko 1:21; 6:2; Luka 4:16) Kumeneko, anali kuphunzitsa anthu, kuwalangiza, na kuwalimbikitsa. Mpingo wacikhristu utakhazikitsidwa, mtumwi Paulo nayenso anali kulalikila kwambili m’masunagoge. Anthu a njala yauzimu anali kupita ku sunagoge. Ndiye cifukwa cake nthawi zambili Paulo akaloŵa mu mzinda, coyamba anali kupita ku sunagoge kukalalikila.—Mac. 17:1, 2; 18:4.