NKHANI YOPHUNZILA 35
NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu
Mmene Akulu Angathandizile Amene Anacotsedwa Mumpingo
“Kumwamba kudzakhala cisangalalo coculuka cifukwa ca munthu mmodzi wocimwa amene walapa.”—LUKA 15:7.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Cifukwa cake anthu ena amacotsedwa mumpingo, komanso mmene akulu angathandizile anthu otelo kulapa na kuyandikilanso Yehova.
1-2. (a) Kodi Yehova amamva bwanji ngati anthu acita macimo mwadala? (b) Kodi Yehova amafuna kuti amene wacita colakwa cacikulu acite ciyani?
YEHOVA sakondwela na khalidwe lililonse loipa, ndipo amadana na ucimo. (Sal. 5:4-6) Iye amafuna tizitsatila miyeso yake yolungama yopezeka m’Mawu ake. Ngakhale n’telo, Yehova amadziŵa kuti ndife opanda ungwilo. Conco satiyembekezela kutsatila miyeso yake mmene munthu wangwilo angacitile. (Sal. 130:3, 4) Panthawi imodzimodziyo, iye sakondwela na anthu ‘osaopa Mulungu [amene] atenga kukoma mtima kwakukulu kwake kukhala cifukwa cocitila khalidwe lopanda manyazi.’ (Yuda 4) Ndipo Baibo imakamba za ‘kuwonongedwa [kwa] anthu osaopa Mulungu’ pa nkhondo ya Mulungu ya Aramagedo.—2 Pet. 3:7; Chiv. 16:16.
2 Ngakhale n’telo, Yehova safuna kuti munthu aliyense akawonongeke. Monga tinaphunzilila m’nkhani yaciŵili ya m’magazini ino, Baibo imaonetsa bwino kuti iye “akufuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Potengela citsanzo ca Yehova, akulu amakhala oleza mtima pamene akuyesetsa kuthandiza munthu amene anacita colakwa cacikulu kuti alape na kuyandikilanso Yehova. Komabe, nthawi zina munthu amene wacita colakwa sangafune kulapa. (Yes. 6:9) Ena amapitiliza kucita colakwa ngakhale kuti akulu ayesetsa mobweleza-bweleza kuwathandiza kuti alape. Kodi akulu ayenela kucita ciyani zikakhala conco?
“M’COTSENI MUNTHU WOIPAYO”
3. (a) Kodi Baibo imakamba kuti n’ciyani ciyenela kucitika kwa munthu wocimwa wosalapa? (b) Ngati munthu safuna kulapa, n’cifukwa ciyani tingakambe kuti iye wasankha yekha kucotsedwa mumpingo?
3 Ngati munthu wolakwayo saonetsa kulapa, akulu ayenela kutsatila malangizo ali pa 1 Akorinto 5:13 akuti: “M’cotseni munthu woipayo pakati panu.” Wolakwayo amadziŵa kuti ngati salapa, adzacotsedwa mumpingo. Conco zimakhala ngati wasankha yekha kucotsedwa mumpingo. Iye amakhala kuti akukolola zimene anafesa. (Agal. 6:7) N’cifukwa ciyani tikunena conco? Cifukwa cakuti munthuyo wakana kusintha njila zake, ngakhale kuti akulu ayesetsa mobweleza-bweleza kum’thandiza kuti alape. (2 Maf. 17:12-15) Zocita zake zimaonetsa kuti safuna kutsatila malamulo a Yehova.—Deut. 30:19, 20.
4. N’cifukwa ciyani cilengezo cimapelekedwa munthu wosalapa akacotsedwa mumpingo?
4 Munthu wosalapa akacotsedwa mumpingo, cilengezo cimapelekedwa podziŵitsa mpingo kuti munthuyo salinso wa Mboni za Yehova. Colinga copelekela cilengezo cimeneco sikucititsa manyazi wolakwayo ayi. M’malomwake, cilengezoco cimapelekedwa kuti mpingo utsatile lamulo la m’Malemba lakuti: “Musiye kugwilizana” naye “ngakhale kudya naye” munthuyo. (1 Akor. 5:9-11) Pali zifukwa zabwino zimene Yehova anapelekela lamulo limeneli. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zofufumitsa zazingo’no zimafufumitsa mtanda wonse wa ufa wokandakanda.” (1 Akor 5:6) Munthu wosalapa akapanda kucotsedwa mumpingo, anthu ena angaleke kulemekeza miyeso yolungama ya Yehova.—Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33.
5. Kodi tiyenela kumuona motani munthu amene wacotsedwa mumpingo? Nanga cifukwa ciyani?
5 Conco ngati m’bale kapena mlongo wacotsedwa mumpingo, kodi tiyenela kumuona motani? Ngakhale kuti timaleka kuceza naye, tisaganize kuti munthuyo sangabwelele kwa Yehova. M’malomwake, tizimuona ngati nkhosa yosocela. Nkhosa yosocela cifukwa cakuti yapatuka pa gulu la zinzake imatha kubwelela. Kumbukilani kuti munthuyo anadzipatulila kwa Yehova. Koma zacisoni n’zakuti sakusungabe lonjezo lake la kudzipatulila kwake, ndipo izi zimaika pa ciopsezo ubwenzi wake na Yehova. (Ezek. 18:31) Komabe malinga ngati nthawi ikalipo, komanso Yehova ni wokonzeka kuonetsa cifundo, timakhala na ciyembekezo cakuti munthuyo angabwelele. Kodi akulu amaonetsa bwanji kuti ali na ciyembekezo cimeneci kwa munthu amene wacotsedwa mumpingo?
MMENE AKULU AMATHANDIZILA ANTHU OCOTSEDWA
6. N’ciyani cimene akulu amacita pofuna kuthandiza amene anacotsedwa mumpingo?
6 Munthu akacotsedwa mumpingo, kodi akulu amalekelatu kumuthandiza n’kumusiya kuti adzipezele yekha njila yobwelela kwa Yehova? Ndithudi ayi! Pouza munthu wolakwa kuti adzacotsedwa mumpingo, komiti ya akulu imamufotokozela zimene ayenela kucita kuti abwelele mumpingo. Koma akulu amacitanso zina kuwonjezela pamenepo. Nthawi zambili iwo adzauza wolakwayo kuti angakonde kudzaonananso naye pambuyo pa miyezi ingapo kuti aone ngati wasintha maganizo ake. Ngati pambuyo pa miyezi ingapo munthuyo wavomela kukumananso na akulu, iwo adzamulimbikitsa mwacikondi kuti alape na kubwelela mumpingo. Ngati munthuyo sanalape ngakhale atakumananso naye, akulu adzayesetsa kuti akakumanenso naye m’tsogolo na kumulimbikitsa kuti alape.
7. Kodi akulu amatengela bwanji khalidwe la Yehova la cifundo pamene akuthandiza munthu amene anacotsedwa mumpingo? (Yeremiya 3:12)
7 Akulu amayesetsa kutengela khalidwe la Yehova la cifundo pamene akucita naye munthu amene anacotsedwa mumpingo. Mwacitsanzo, Yehova sanayembekezele anthu ake Aisiraeli kuti alape asanacitepo kanthu kuti awathandize. M’malomwake, iye anawatumizila aneneli ngakhale pamene iwo anali asanaonetse mtima wofuna kulapa. Monga tinaphunzilila m’nkhani yaciŵili ya m’magazini ino, Yehova anauza Hoseya kuti akhululukile mkazi wake ngakhale kuti mkaziyo anali asanasiye kucita chimo lalikulu. Yehova anacita zimenezi pofuna kuphunzitsa anthu ake kuti iye ni wacifundo cacikulu. (Hos. 3:1; Mal. 3:7) Potengela citsanzo ca Yehova, akulu amafunitsitsa kuti munthu wolakwa alape na kubwelela mumpingo. Ndipo pocita zimenezi, iwo samamukhwimitsila zinthu munthuyo.—Ŵelengani Yeremiya 3:12.
8. Kodi fanizo limene Yesu anakamba la mwana woloŵelela, limatithandiza bwanji kumvetsa mozamilapo kuti Yehova ni wacifundo? (Luka 15:7)
8 Kumbukilani fanizo limene Yesu anafotokoza la mwana woloŵelela limene tinakambilana m’nkhani yaciŵili ya m’magazini ino. Bambo wa m’fanizo lija atangomuona mwana wake, “anamuthamangila n’kumukumbatila ndipo anamukisa mwacikondi.” (Luka 15:20) Bamboyu sanayembekezele kuti mwanayo apepese. M’malomwake, monga mmene tate wina aliyense wacikondi angacitile, bamboyu ndiye anayambilila kucitapo kanthu pothamangila mwana wake. Akulu amayesetsa kuonetsa khalidwe limeneli pothandiza anthu amene anasocela. Amafuna kuti nkhosa zosocela zimenezi zibwelele kwa Yehova. (Luka 15:22-24, 32) Kumwamba kumakhala cisangalalo munthu wocimwa akalapa na kubwelela, ndipo mpingo nawonso umasangalala!—Ŵelengani Luka 15:7.
9. Kodi Yehova amawalimbikitsa bwanji anthu ocimwa?
9 Pofika pano taphunzila kuti Yehova sakondwela na munthu wocimwa amene safuna kulapa, ndipo samulola kuti akhalebe mumpingo. Ngakhale n’telo, iye saleka kuwathandiza. Amafuna kuti abwelele kwa iye. Pa Hoseya 14:4, Yehova anafotokoza mmene amamvela munthu wocimwa akalapa. Pa lembalo iye anakamba kuti: “Ndidzathetsa kusakhulupilika kwawo. Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga, cifukwa ndasiya kuwakwiyila.” Podziŵa mmene Yehova amamvela, akulu amaona masinthidwe alionse amene munthu wapanga poonetsa kuti wayamba kulapa. Ndipo mawu amenewa ayenela kutsimikizila amene anasiya Yehova kuti iye amawakonda, ndipo amafuna kuti abwelele kwa iye.
10-11. Kodi akulu angacite ciyani pothandiza anthu amene anacotsedwa mumpingo kumbuyoku?
10 Nanga bwanji za anthu amene anacotsedwa mumpingo kumbuyoku, mwina papita zaka zambili? N’kutheka anthu amenewo anasiya kucita zimene zinawacotsetsa mumpingo. N’kuthekanso kuti anthuwo sakumbukilanso cimene cinawacotsetsa mumpingo. Kaya papita nthawi yaitali motani pamene anthuwa anacotsedwa mumpingo, akulu adzayesetsa kufufuza kumene anthuwo ali na kukonza zakuti akakumane nawo. Pa maulendo amenewo, akulu adzapemphela nawo na kuwalimbikitsa mwacikondi kuti abwelele mumpingo. Ngati munthuyo wakhala kunja kwa mpingo kwa zaka zambili, mosakaikila angakhale kuti ni wofooka kwambili kuuzimu. Conco ngati munthuyo waonetsa kuti akufuna kubwelela mumpingo, akulu angalinganize zakuti munthu wina ayambe kuphunzila naye Baibo. Angacite izi ngakhale kuti munthuyo asanabwezeletsedwe mumpingo. Mulimonse mmene zingakhalile, akulu ndiwo ayenela kusankha m’bale kapena mlongo amene angayambe kuphunzila naye Baibo.
11 Akulu amayesetsa kutengela citsanzo ca Yehova mwa kucitila anthu cifundo. Conco iwo amafufuza anthu onse amene anasiya Yehova na kuwaonetsa kuti khomo n’lotseguka kuti iwo abwelele kwa iye. Munthu wocimwa akangoonetsa kuti walapa, ndipo wasiya zoipa zonse zimene anali kucita, angabwezeletsedwe mumpingo.—2 Akor. 2:6-8.
12. (a) Kodi akulu ayenela kukhala osamala kwambili pa nkhani ziti? (b) N’cifukwa ciyani sitiyenela kuganiza kuti n’zosatheka Yehova kucitila cifundo anthu amene anacita macimo ena ake? (Onaninso mawu a m’munsi)
12 Pa zocitika zina, akulu ayenela kukhala osamala kwambili asanabwezeletse munthu mumpingo. Mwacitsanzo, ngati munthu anacotsedwa cifukwa cocitila mwana nkhanza, kapena anali wampatuko, kapenanso anacita kukonza ciwembu kuti athetse ukwati wake, akulu ayenela kukhala otsimikiza kuti munthuyo ni wolapadi. (Mal. 2:14; 2 Tim. 3:6) Iwo ayenela kuteteza abale na alongo mumpingo. Koma panthawi imodzimodzi, tiyenela kudziŵa kuti Yehova amalandila munthu aliyense wocimwa amene walapadi na kusiya njila zake zoipa. Conco ngakhale kuti akulu ayenela kutsimikizila kuti munthu amene anacitila ena zacinyengo walapadi, sayenela kuganiza kuti n’zosatheka Yehova kumucitila cifundo munthu woteloyo. a—1 Pet. 2:10.
ZIMENE MPINGO UNGACITE
13. Kodi pali kusiyana kotani mmene timacitila naye munthu amene wadzudzulidwa, na uja wocotsedwa mumpingo?
13 Monga tinakambilana m’nkhani yapita, cilengezo cikapelekedwa cakuti munthu wina wake anadzudzulidwa, timapitiliza kugwilizana naye podziŵa kuti munthuyo analapa ndipo anasiya kucita zoipa. (1 Tim. 5:20) Munthuyo akali ciwalo ca mpingo, ndipo amafunika kulimbikitsidwa na Akhristu anzake poceza nawo. (Aheb. 10:24, 25) Komabe zinthu zimakhala zosiyanako na munthu amene wacotsedwa mumpingo. ‘Timasiya kugwilizana’ naye munthuyo “ngakhale kudya naye munthu” wotelo.—1 Akor. 5:11.
14. Kodi Mkhristu angaseŵenzetse bwanji cikumbumtima cake cophunzitsidwa Baibo pocita naye munthu amene anacotsedwa mumpingo? (Onaninso cithunzi.)
14 Kodi zimene takambilanazi zitanthauza kuti munthu akacotsedwa mumpingo, sitingamuitanile ku msonkhano kapena kum’patsa moni akabwela pa msonkhano? Osati kwenikweni. N’zoona kuti sitiyenela kuceza naye. Koma ngati munthuyo ni wacibale wathu kapena anali mnzathu wapamtima asanacotsedwe mumpingo, tingaseŵenzetse cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo, kusankha kuitanila munthuyo ku msonkhano wa mpingo. Ngati munthuyo wafika pa msonkhano, kodi tiyenela kucita naye bwanji? Kumbuyoku sitinali kupeleka moni kwa munthuyo. Koma pa mbali imeneyinso, Mkhristu aliyense ayenela kuseŵenzetsa cikumbumtima cake cophunzitsidwa Baibo. Ena angasankhe kum’patsa moni munthuyo kapena kumulandila pa msonkhano. Komabe sitiyenela kuceza naye munthuyo kapena kucita naye zinthu zina.
15. Kodi 2 Yohane 9-11 imakamba za anthu ati? (Onaninso mbali yakuti “ Kodi Yohane na Paulo Anali Kukamba za Chimo la Mtundu Umodzi?”)
15 Ena angafunse kuti, ‘Kodi Baibo siifotokoza kuti munthu amene wapatsa moni munthu wotelo akucita naye nchito zake zoipazo?’ (Ŵelengani 2 Yohane 9-11.) Nkhani yonse ya pa lembali ionetsa kuti malangizowa amakamba za ampatuko, komanso amene amalimbikitsa makhalidwe oipa. (Chiv. 2:20) Conco ngati munthu amalimbikitsa ziphunzitso za mpatuko kapena makhalidwe oipa, akulu sadzakonza zakuti akamuyendele. Komabe pali ciyembekezo cakuti anthu otelowa angasinthe. Mpaka pamene munthuyo adzasinthe, sitiyenela kum’patsa moni kapena kumuitanila ku msonkhano wa mpingo.
KUTENGELA KHALIDWE LA YEHOVA LA CIFUNDO
16-17. (a) Kodi Yehova amafuna kuti ocimwa acite ciyani? (Ezekieli 18:32) (b) Kodi akulu angaonetse bwanji kuti ni anchito anzake a Yehova pamene akuthandiza anthu amene anacimwa?
16 Taphunzila ciyani m’magazini ino? Yehova safuna kuti munthu aliyense akawonongeke! (Ŵelengani Ezekieli 18:32.) Iye amafuna kuti ocimwa agwilizanenso naye. (2 Akor. 5:20) Ndiye cifukwa cake Yehova wakhala akulimbikitsa atumiki ake amene anamusiya kuti alape na kubwelela kwa iye. Akulu mumpingo amagwila nchito pamodzi na Yehova pamene akuyesetsa kuthandiza anthu amene anacita macimo aakulu kuti alape.—Aroma 2:4; 1 Akor. 3:9.
17 Kumwamba kumakhala cimwemwe cacikulu munthu wocimwa akalapa! Atate wathu wa kumwamba, Yehova, amasangalala kwambili nthawi zonse nkhosa yosocela ikabwelela mumpingo. Cikondi cathu pa Yehova cimakulilako tikamaganizila cifundo cake komanso kukoma mtima kwake kwakukulu.—Luka 1:78.
NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe
a Malinga n’kunena kwa Baibo, pali chimo limene silingakhululukidwe. Chimo limenelo si mtundu wina wake wa chimo. Koma anthu amene amacita chimo limenelo ni aja amene amasankha kucita zinthu zotsutsana na Mulungu nthawi zonse. Komabe, ni Yehova yekha na Yesu amene amadziŵa kuti chimo limene munthu wacita ni losakhululukidwa.—Maliko 3:29; Aheb. 10:26, 27.