Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

N’cifukwa ciyani amuna amene sanali Aisiraeli anatumikila m’gulu la asilikali a Mfumu Davide?

ASILIKALI a Davide omwe sanali Aisiraeli anaphatikizapo amuna monga Zeleki mbadwa ya Amoni, Uriya Muhiti, komanso Itima wa ku Mowabu. a (1 Mbiri 11:​39, 41, 46) M’gulu limenelo munalinso mtundu wa “Akereti,” “Apeleti,” komanso “Agiti.” (2 Sam. 15:18) Zioneka kuti Akereti na Apeleti anali pa ubale wapafupi na Afilisiti. (Ezek. 25:16) Naonso Agiti ayenela kuti anali ocokela mu mzinda wa Afilisiti wa Gati.—Yos. 13:​2, 3; 1 Sam. 6:​17, 18.

N’cifukwa ciyani Davide anaika anthu amenewa m’gulu la asilikali ake? Anali wotsimikiza kuti iwo anali okhulupilika kwa iye, komanso makamaka kwa Yehova. Mwa citsanzo, ponena za Akereti na Apeleti buku lina lochedwa The New Interpreter’s Dictionary of the Bible inati: “Iwo anakhalabe okhulupilika kwa Davide ngakhale pa nthawi zovuta za ulamulilo wake.” Motani? Pa nthawi ina, “anthu onse a Isiraeli anacoka kwa Mfumu Davide n’kuyamba kutsatila” munthu amene anayambitsa mpatuko dzina lake “Sheba mwana wa Bikiri.” Koma Akereti na Apeleti anakhalabe okhulupilika kwa Davide, ndipo anathandiza kuthetsa mpatuko umenewo. (2 Sam. 20:​1, 2, 7) Pa nthawi ina, mwana wa Mfumu Davide, Adoniya, anafuna kudzilonga yekha ufumu m’malo mwa Solomo. Komabe, Akereti na Apeleti anakhalabe okhulupilika kwa Davide. Anatelo mwa kuthandiza kuika Solomo pa ufumu, munthu yemwe Yehova anasankha kuti adzaloŵe Davide m’malo.—1 Maf. 1:​24-27, 38, 39.

Munthu wina amene anakhalabe wokhulupilika kwa Davide ngakhale kuti sanali Mwisiraeli anali Itai Mgiti. Iye na asilikali ake 600 anathandiza Mfumu Davide pomwe mwana wake, Abisalomu, anam’pandukila n’kucititsa mitima ya Aisiraeli kumugalukila. Poyamba, Davide anauza Itai kuti popeza sanali Mwisiraeli, nkhondoyo sinali kumukhudza ndipo anamuuza kuti abwelele. Koma Itai anayankha kuti: “Ndikulumbila m’dzina la Yehova Mulungu wamoyo komanso mbuyanga mfumu muli apa, kulikonse kumene inu mungapite, ine mtumiki wanu ndipitanso komweko, ndipo ndine wokonzeka ngakhale kufa nanu limodzi!”—2 Sam. 15:​6, 18-21.

Itai anali wokhulupilika kwa Davide, mfumu yodzozedwa ya Yehova

Ngakhale kuti Akereti, Apeleti, komanso Agiti sanali Aisiraeli, anali kuona Yehova kuti ni Mulungu woona, komanso Davide monga wodzozedwa wake. N’zosacita kufunsa kuti Davide anali woyamikila kukhala na amuna okhulupilika amenewa pambali pake!

a Lamulo la Mulungu lopezeka pa Deuteronomy 23:​3-6 inaletsa a Amoni komanso Amowabu kuloŵa mu mpingo wa Aisiraeli. Zioneka kuti lamulo limeneli linali kuwaletsa kukhala nzika za Isiraeli mwalamulo. Komabe, silinawaletse kugwilizana na anthu a Mulungu kapena kupezeka pakati pawo. Onani buku lakuti Insight on the Scriptures, Volume 1, tsamba 95.