Pitilizani Kupemphela Kuti Mulungu Akuyanjeni
Mulungu anapatsa ife anthu mphatso yapadela yakuti tizikwanitsa kukambilana naye m’pemphelo, na kumuuza mmene timvelela. Mneneli Davide anapemphela kuti: “Inu Wakumva pemphelo, anthu a mitundu yonse adzabwela kwa inu.” (Salimo 65:2) Koma kodi tingapemphele bwanji kuti Mulungu atimvele na kutidalitsa?
PEMPHELANI MODZICEPETSA KOMANSO MOCOKELA PANSI PAMTIMA
Mapemphelo anu a panokha amakupatsani mwayi wokhuthulila Mulungu za mumtima mwanu, kuti mumuuze zokhudza mmene mumvelela. (Salimo 62:8) Mulungu Wamphamvuzonse amakonda mapemphelo ocokela pansi pamtima.
POKAMBA NA MULUNGU MUZISEŴENZETSA DZINA LAKE LENI-LENI
Ngakhale kuti Mulungu ali na maina audindo ambili, dzina lake leni-leni ni limodzi. Iye akuti, “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Yesaya 42:8) Dzina lakuti Yehova limapezeka maulendo opitilila 7,000 m’Malemba Oyela. Popemphela kwa Mulungu, aneneli ambili anali kuseŵenzetsa dzina lake leni-leni. Abulahamu anati: “Conde Yehova, . . . ndiloleni ndilankhulebe [nanu].” (Genesis 18:30) Nafenso tiyenela kuseŵenzetsa dzina la Mulungu lakuti Yehova popemphela.
PEMPHELANI M’CITUNDU CIMENE MUFUNA
Mulungu amamvetsetsa maganizo athu na mmene timvelela, mosasamala kanthu za citundu cimene timakamba. Mawu ake amatitsimikizila kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.”—Machitidwe 10:34, 35.
Koma kuwonjezela pa kupemphela, palinso zina zimene tifunika kucita kuti tidalitsidwe na Mulungu. M’nkhani zokonkhapo, tidzaona zimene tifunika kucita.