Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

N’nalandila Coonadi Olo Kuti Nilibe Manja

N’nalandila Coonadi Olo Kuti Nilibe Manja

Anthu akafuna kugwa, amagwila cinacake. Koma ine sinikwanitsa cifukwa nilibe manja. Pamene n’nali na zaka 7, ananidula manja kucipatala kuti apulumutse moyo wanga.

Amayi anga anali na zaka 17 pamene n’nabadwa mu 1960. Atate anathaŵa panyumba nikalibe kubadwa. Ine na amayi tinali kukhala na ambuya ku Burg, tauni ing’ono m’dziko limene kale linali kuchedwa East Germany. Ndipo anthu ambili kumeneko, kuphatikizapo acibale anga, sanali kukhulupilila kuti Mulungu aliko. Mulungu tinalibe naye nchito.

Pamene n’nali kukula, n’nali kukonda kuseŵela na ambuya aamuna. Anali kukonda kunipatsa nchito zambili monga kukwela m’mitengo kuti nidule nthambi zake ndipo n’nali kusangalala pocita zimenezo. N’nalibe nkhawa pa umoyo wanga ndiponso n’nali kukhala wosangalala.

NGOZI INASINTHA UMOYO WANGA

Tsiku lina, nili na zaka 7, cina-cake coopsa cinanicitikila. N’nali nitangoyamba kumene giledi 2. Pobwelela kunyumba n’takomboka kusukulu, n’nakwela pho ya malaiti. N’nakwela mpaka kufika mamita 8. Nili pamwamba n’nadonsewa mwamphamvu na malaiti cakuti n’nakomoka. N’naukila ku cipatala, apo n’kuti nilibe manja. Manja anga anapsa kwambili pangozi imeneyo, ndipo zilonda zinali zikulu ngako cakuti ananidula manja kuti poizoni isafalikile thupi lonse. Amayi na ambuya anamva cisoni kwambili. Koma popeza n’nali mwana, sin’nali kudziŵa kuti kukhala nilibe manja kudzakhudza bwanji umoyo wanga.

N’tatulutsidwa m’cipatala, n’nayambanso kuyenda kusukulu. Anzanga anayamba kuniseka, kunizunza, ndi kunitema na zinthu cifukwa codziŵa kuti siningawabwezemo. Anali kunicitila nkhanza na kuninena, ndipo cinali kuniŵaŵa ngako. Ndiyeno, ananitumiza ku sukulu ya olemala yochedwa Birkenwerder, imene inali monga sukulu ya boding’i. Sukuluyi inali kutali kwambili na kwathu cakuti amayi na ambuya sanali kukwanitsa kukaniona. N’nali kuonana nawo m’maholide cabe. Conco, kwa zaka 10 n’nakulila kutali na amayi ndi ambuya.

UMOYO WOPANDA MANJA

N’naphunzila kuseŵenzetsa mendo pocita zinthu. Ganizilani cabe, n’nafunika kuseŵenzetsa mendo pogwila foloko na spuni kuti nidye. Pang’ono-pangono n’naphunzila kucita zimenezi. N’naphunzilanso kutsuka manu na kusakula tsitsi poseŵenzetsa mendo. Ndiponso n’nayamba kucita magesicha na mendo pokamba na anthu. Mendo ndi imene inakhala monga manja anga.

Pamene n’nali wacicepele, n’nali kukonda kuŵelenga nkhani zopeka za sayansi. Nthawi zina, n’nali kulaka-laka kukhala na manja opanga amene anganithandize kucita ciliconse cimene nafuna. Pamene n’nali na zaka 14, n’nayamba kupepa fwaka. Kucita zimenezo kunali kunicititsa kukhala na cidalilo na kudziona kuti ningathe kucita zinthu ngati anthu ena onse. Zinali monga nikamba kuti: ‘Naine ndine mkulu, ningapepe fwaka olo kuti nilibe manja.’

N’nayamba kudzitangwanitsa mwa kucita zinthu zina. N’nakhala memba wa gulu landale la acicepele lochedwa Free German Youth limene linali kucilikizidwa na boma. N’nakhala kalembela wa gulu limenelo, ndipo umenewu unali udindo wapamwamba. N’naloŵanso kilabu ya zoyimba-yimba. N’nali kulemba ndakatulo na kucitako maseŵela a anthu olemala. Pambuyo pophunzilako nchito, n’nayamba kuseŵenza pa kampani inayake m’tauni yathu. N’nali kukonda kuvala manja a pulastiki kuti nizioneka kuti nili na manja.

KULANDILA COONADI CA M’BAIBO

Tsiku lina pamene n’nali kuyembekeza sitima kuti niyende ku nchito, munthu wina anabwela kwa ine. Iye ananifunsa ngati nidziŵa kuti Mulungu angacititse kuti nikhalenso na manja. N’nadabwa ngako! N’nali kulaka-laka kukhalanso na manja, koma n’nali kuona kuti zimene anakambazo ndi maloto cabe ndipo sizingatheke. Popeza n’nali kukhulupilila kuti kulibe Mulungu, n’nayamba kumupewa munthuyo.

Nthawi ina, mnzanga wa ku nchito ananiitana kunyumba kwake. Kumeneko, tinayamba kuceza na banja lake uku tikumwa khofi. Ndiyeno makolo ake anayamba kukamba za Mulungu—Yehova Mulungu. Aka kanali koyamba kumvela kuti Mulungu ali na dzina. (Salimo 83:18) Koma mumtima, n’nali kutsutsa kuti: ‘Bodza, kulibe Mulungu olo kuti am’patse dzina labwanji. Nidzaŵapatsa umboni woonetsa kuti zimene akamba n’zabodza.’ Nili na maganizo amenewo, n’navomela kuphunzila Baibo. Koma n’nadabwa cifukwa n’nakangiwa kupeleka umboni wakuti kulibe Mulungu.

Pamene tinali kuphunzila maulosi a m’Baibo, maganizo anga akuti kulibe Mulungu anayamba kusila. N’naona kuti zinthu zambili zimene Mulungu analosela, zinacitikadi ngakhale kuti anakamba kukali zaka zambili. Tsiku lina pokambilana za m’Baibo, tinayelekeza mmene dziko lilili masiku ano na maulosi ali pa Mateyu caputa 24, Luka caputa 21 na pa 2 Timoteyo caputa 3. Monga mmene zizindikilo zosiyana-siyana zimathandizila dokota kudziŵa matenda a wodwala, zizindikilo zochulidwa m’maulosi amenewo zinan’thandiza kudziŵa kuti tikukhaladi mu “masiku otsiliza” ochulidwa m’Baibo. * N’nasoŵa cokamba. N’naonadi kuti maulosi amenewa anali kukwanilitsika.

Sin’nakayikile kuti n’nali kuphunzila coonadi. N’nayamba kupemphela kwa Yehova Mulungu ndipo n’naleka kupepa fwaka. N’nakwanitsa kuleka ngakhale kuti n’nali n’tapepa kwa zaka zoposa 10. N’naphunzila Baibo pafupi-fupi kwa caka cimodzi. Pa 27 April, mu 1986, ananibatiza mwakabisila m’bafa yosambilamo, cifukwa panthawiyo Mboni zinali zoletsedwa ku East Germany.

KUPATSAKO ENA

Cifukwa cakuti Mboni zinali zoletsedwa m’dzikolo, tinali kusonkhana m’nyumba za abale m’tumagulu mwakabisila. Conco, sin’nali kudziŵa abale ambili. Mwamwayi wanji a boma ananilola kusamukila ku West Germany, kumene Mboni sizinali zoletsedwa. Ndipo kwa nthawi yoyamba mu umoyo wanga, n’nayamba kupezeka pa misonkhano ikulu-ikulu yophunzitsa Baibo. Pamisonkhanoyo n’naona abale na alongo anga ambili-mbili. Nthawi imeneyo inali yosangalatsa kwambili.

Pambuyo pakuti cipupa ca Berlin cagwetsedwa, Mboni za Yehova zinapatsidwa ufulu wolambila. Panthawiyo tinayambanso kulambila Yehova Mulungu momasuka. N’nafuna kuyamba kulalikila kwambili. Komabe, n’nali kuopa kukamba na anthu amene siniŵadziŵa. N’nali kudziona wacabe-cabe cifukwa colemala komanso cifukwa cokulila m’nyumba ya olemala. Koma mu 1992, n’nayesako kulalikila kwa maola 60 kwa mwezi umodzi. Ulaliki unayenda bwino ndipo n’napeza cimwemwe coculuka. Conco, n’naganiza zakuti mwezi uliwonse nizicita zimenezo ndipo n’napitiliza mpaka zaka pafupi-fupi zitatu.

Nthawi zonse nimakumbukila mau a m’Baibo akuti: “Ndani ali wofooka, ine osakhalanso wofooka?” (2 Akorinto 11:29) Ngakhale kuti nilibe manja, nimaganiza na kukamba. Conco nimacita zimene ningakwanitse kuti nithandize ena. Popeza nidziŵa bwino mmene cimvekela kukhala wolemala, nimatha kutonthoza ena amene sakwanitsa kucita zambili. Nidziŵa mmene cimvekela ngati ufuna kucita cinthu koma sukwanitsa kucicita cifukwa colemala. Nimayesa kulimbikitsako ena amene amamvela conco. Kupatsa ena mwa njila imeneyo kumanibweletsela cimwemwe.

Kuuzako ena uthenga wabwino kumanipatsa cimwemwe

YEHOVA AMANITHANDIZA TSIKU LILILONSE

Kukamba zoona, nthawi zina nimavutika maganizo. Naine nimafuna kukhala na ziwalo zonse. Nimakwanitsa kucita zonse zofunikila tsiku lililonse, koma zimatenga nthawi yaitali, ndipo zimafuna khama ndi mphamvu zambili kuposa mmene munthu ali na manja amacitila. Mfundo imene imanithandiza tsiku lililonse ni yakuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Tsiku lililonse, Yehova amanipatsa mphamvu zofunikila kuti nicite zinthu “zofunika.” Kukamba zoona, Yehova sananisiyepo. Ndiye cifukwa cake naine sinidzamusiya.

Si zokhazo, Yehova wanidalitsa mwa kunipatsa banja—cinthu cimene n’nasoŵeka pamene n’nali kukula. Nili na mkazi wabwino, Elke, mkazi wacikondi ndiponso wacifundo. Kuwonjezela apo, Mboni za Yehova mamiliyoni ambili pa dziko lonse zakhala abale na alongo anga auzimu.

Ine na mkazi wanga wokondedwa, Elke

Nimatonthozedwa na lonjezo la Mulungu lakuti adzabweletsa Paradaiso mmene zinthu zonse zidzakhala “zatsopano” kuphatikizapo manja anga. (Chivumbulutso 21:5) Nimatsimikizila kuti lonjezo limeneli lidzakwanilitsika nikaganizila zimene Yesu anacita pamene anali pano padziko. M’nthawi yocepa cabe, anacilitsa munthu wopuwala dzanja ndi kubwezeletsa khutu la mwamuna wina limene linadulidwa. (Mateyu 12:13; Luka 22:50, 51) Malonjezo a Yehova na zozizwitsa zimene Yesu anacita zimanicititsa kukhala wotsimikiza kuti posacedwa nidzakhala na ziwalo zonse.

Komabe, dalitso likulu pa zonse, ni mwayi wodziŵa Yehova Mulungu. Iye ni atate wanga, bwenzi langa, wonitonthoza, ndi mphamvu yanga. Nimvela mmene Mfumu Davide anamvelela. Iye analemba kuti: “Yehova ndiye mphamvu yanga . . .Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwela.” (Salimo 28:7) Ndipo coonadi camtengo wapatali cimeneci nidzacisunga kwa moyo wanga wonse. Nimacigwila na manja aŵili olo kuti nilibe manja.

^ par. 17 Kuti mudziŵe zambili pankhani ya zizindikilo za masiku otsiliza, ŵelengani nkhani 9 yakuti; “Kodi Tili mu ‘Masiku Otsiliza’?” m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa na Mboni za Yehova, ndipo lilipo pa webusaiti yathu ya www.isa4310.com.