Kodi Kukhala Munthu Wabwino Kungakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?
Kwa zaka mazana ambili, anthu akhala akukhulupilila kuti kukhala munthu wabwino n’kumene kungawathandize kukhala na tsogolo labwino. Mwacitsanzo, anthu ambili ku Asia amakhulupilila zimene anakamba mphunzitsi wochuka dzina lake Confucius (amene anakhalako pakati pa 551 na 479 B.C.E.) Iye anati: “Zimene simufuna kuti ena akucitileni, inunso musawacitile zimenezo.” *
ZIMENE AMBILI AMASANKHA KUCITA
Ambili amakhulupilila kuti kukhala na khalidwe labwino n’kumene kungawathandize kukhala na tsogolo labwino. Iwo amayesetsa kukhala aulemu, okoma mtima, kuzindikila udindo wawo, komanso kukhala na cikumbumtima cabwino. Mayi wina wa ku Vietnam, dzina lake Linh anati: “Nthawi zonse n’nali kukhulupilila kuti ngati nicita zinthu moona mtima, ndiye kuti nidzadalitsidwa.”
Anthu ena amayesetsa kucita zabwino cifukwa ca zimene amaphunzila ku cipembedzo cawo. Munthu wina dzina lake Hsu-Yun, amene amakhala ku Taiwan, anati: “N’naphunzitsidwa kuti ngati munthu acita zabwino, ndiye kuti adzakhala na umoyo wacimwemwe akadzamwalila. Koma ngati acita zoipa adzavutika.”
KODI ZOTULUKAPO ZAKE ZAKHALA ZOTANI?
N’zoona kuti tikamacitila ena zabwino, timapindula m’njila zambili. Komabe, anthu ambili amene amayesetsa kucitila ena zabwino, amaona kuti nthawi zina anthu ena sawacitila zabwino. Mayi wina wa ku Hong Kong, dzina lake Shiu Ping anati: “N’nadzionela nekha kuti anthu amene amacitila ena zabwino, nthawi zina sacitilidwa zabwino. N’nali kuyesetsa kusamalila banja langa na kucita zabwino. Koma ukwati wathu unavuta, ndipo mwamuna wanga anatithaŵa, ine na mwana wanga.”
Ambili amaona kuti anthu ena opembedza sakhala abwino. Mayi wina wa ku Japan, dzina lake Etsuko anati: “N’naloŵa cipembedzo cinacake, ndipo n’nakhala mtsogoleli wa kagulu ka acinyamata. N’nadabwa kuona kuti ena m’cipembedzo cathu anali na khalidwe la ciwelewele, anali kulimbilana maudindo, komanso anali osakhulupilika poseŵenzetsa ndalama za chalichi.”
“N’nali kuyesetsa kusamalila banja langa na kucita zabwino. Koma ukwati wathu unavuta, ndipo mwamuna wanga anatithaŵa, ine na mwana wanga.”—SHIU PING, HONG KONG
Anthu ena odzipeleka kwambili pa zacipembedzo komanso amene amayesetsa kucita zabwino, amakhumudwa akaona zinthu zoipa zimene zimawacitikila. Umu ni mmene mayi wina wa ku Vietnam dzina lake Van anamvelela. Iye anati: “Tsiku lililonse n’nali kugula zipatso, maluwa, na zakudya n’kukazipeleka pa guwa la nsembe la makolo anga akale amene anamwalila. N’nali kucita izi poganiza kuti kutsogolo nidzalandila madalitso. Ngakhale kuti kwa zaka zambili n’nali kucita zabwino na kutsatila miyambo ya cipembedzo cathu, mwamuna wanga anadwala matenda oopsa. Kenako mwana wanga anamwalila ali mtsikana, pamene anali kucita maphunzilo ku dziko lina.”
Ngati kukhala munthu wabwino pakokha sikungathandize munthu kukhala na tsogolo labwino, ndiye cingathandize n’ciani? Kuti funso limeneli liyankhidwe na ena amene tingakhale nawo, tifunikila gwelo la malangizo odalilika amene angatithandize kudziŵa zimene tingacite kuti tikhale na tsogolo labwino. Kodi malangizo amenewo tingawapeze kuti?
^ ndime 2 Kuti mudziŵe zambili za ciphunzitso ca Confucius, onani mutu 7, ndime 31-35, m’buku lakuti Mankind’s Search for God, lofalitsidwa na Mboni za Yehova, ndipo lilipo pa webusaiti yathu ya www.isa4310.com.