Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mungakhale na Moyo Kwamuyaya Padziko Lapansi

Mungakhale na Moyo Kwamuyaya Padziko Lapansi

ICI NI CIYEMBEKEZO CABWINO MANINGI! Mlengi wathu anatilonjeza moyo wosatha, pano padziko lapansi. Koma ambili amavutika kukhulupilila zimenezi. Iwo amakamba kuti, ‘munthu aliyense amabadwa na kufa, ndiye mmene moyo ulili.’ Enanso amaona kuti kukhala na moyo kwamuyaya n’kotheka, koma osati pano padziko lapansi. Iwo amakamba kuti munthu amalandila moyo wosatha akafa na kuyenda kumwamba. Kodi imwe muganiza bwanji?

Mukalibe kuyankha, mungacite bwino kudziŵa mmene Baibo imayankhila mafunso atatu awa: Kodi mmene munthu anapangiwila zimaonetsa ciani ponena za kutalika kwa nthawi imene munthu afunikila kukhala na moyo? Kodi poyamba colinga ca Mulungu cokhudza dziko lapansi ndi anthu cinali ciani? Kodi cinacitika n’ciani kuti anthu ayambe kufa?

ANTHU ANALENGEWA MWAPADELA

Pa zamoyo zonse zimene Mulungu analenga padziko lapansi, anthu analengewa mwapadela kwambili. N’cifukwa ciani? Baibo imaonetsa kuti ni anthu cabe amene analengewa ‘‘m’cifanizilo’’ ca Mulungu komanso ‘mofanana’ naye. (Genesis 1:26, 27) Kodi zimenezi zitanthauza ciani? Izi zitanthauza kuti anthu analengewa na makhalidwe amene Mulungu ali nawo, monga cikondi na cilungamo.

Kuonjezela apo, anthu analengewa mwa njila yakuti azikwanitsa kuganiza mozama, na kukwanitsa kusiyanitsa cabwino na coipa, ndiponso ali na cikhumbo cofuna kudziŵa Mulungu na kukhala naye pa ubwenzi. N’cifukwa cake timasangalala na ukulu wa cilengedwe, zodabwitsa za m’cilengedwe, mapikica okopewa mwaluso, nyimbo, komanso ndakatulo. Koposa zonse, anthu amakwanitsa kupalana ubwenzi na Mlengi. Makhalidwe amenewa amasiyanitsa kwambili anthu na zamoyo zina zonse padziko lapansi.

Ndiyeno ganizilani izi: Kukanakhala kuti Mulungu anatilenga kuti tizikhala na moyo kwa zaka zocepa cabe, kodi akanalenga anthu na makhalidwe apadela monga amenewa, amene timafuna kukhala nawo na kuwakulitsa kwamuyaya? Zoona n’zakuti Mulungu analenga anthu na makhalidwe apadela amenewa kuti azisangalala na moyo kwamuyaya pano padziko lapansi.

COLINGA CA MULUNGU CA POYAMBA

Ena amakamba kuti Mulungu sanalenge anthu kuti azikhala padziko lapansi kwamuyaya. Iwo amakamba kuti dziko inapangiwa kuti ikhale malo oyembekezela cabe, podziŵila kuti ndani ali woyenelela kuyenda kumwamba kuti akakhale na moyo kwamuyaya na Mulungu. Ngati zimenezo zikanakhala zoona, kodi sizingatanthauze kuti Mulungu ndiye acititsa zoipa zonse zimene zili paliponse m’dzikoli? Zimenezo zikanakhala zosiyana na makhalidwe a Mulungu. Ponena za iye, Baibo imakamba kuti: “Njila zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupilika, amene sacita cosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”—Deuteronomo 32:4.

Baibo imafotokoza momveka bwino colinga ca Mulungu ca poyamba cokhudza dziko lapansi m’mau awa: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi analipeleka kwa ana a anthu.” (Salimo 115:16) Inde, Mulungu analenga dziko lapansi kuti likhale malo okongola, okhalapo anthu kwamuyaya. Ndipo anaikamo zonse zofunikila kuti tisangalale na moyo kwamuyaya.—Genesis 2:8, 9.

“Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi analipeleka kwa ana a anthu.”Salimo 115:16

Baibo imakambanso momveka bwino ponena za colinga ca Mulungu cokhudza anthu. Iye analamula Adamu na Hava kuti ‘adzaze dziko lapansi, ndipo aliyang’anile. . . . Ayang’anilenso colengedwa ciliconse cokwawa padziko lapansi.’ (Genesis 1:28) Anali na mwayi waukulu wosamalila na kukulitsa malile a Paradaiso zungulile dziko lonse! Zoonadi, ciyembekezo cimene Adamu na Hava komanso ana awo amene anali kudzabadwa cinali moyo wosatha padziko lapansi osati kumwamba.

N’CIFUKWA CIANI TIMAFA?

Nanga n’cifukwa ciani timafa? Baibo imafotokoza kuti mmodzi wa zolengedwa zauzimu za Mulungu amene pambuyo pake anakhala wopanduka, Satana Mdyelekezi, anayesa kulepheletsa colinga ca Mulungu mu Edeni. Motani?

Satana anakopa makolo athu oyamba Adamu na Hava, kuti akhale ku mbali yake popandukila Mulungu. Satana anakamba kuti Mulungu anali kuŵamana cinthu cina cabwino, cimene ni ufulu wodzisankhila cabwino na coipa. Iwo anasankha kukhala kumbali ya Satana na kupandukila Mulungu. Zotulukapo zake? M’kupita kwa nthawi iwo anafa, monga mmene Mulungu anawacenjezela. Anataya ciyembekezo cokhala na moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.—Genesis 2:17; 3:1-6; 5:5.

Kupanduka kwa Adamu na Hava kunakhudza anthu onse mpaka masiku ano. Mau a Mulungu amakamba kuti: ‘Ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse.’ (Aroma 5:12) Timafa cifukwa tinatengela ucimo kwa makolo athu oyambilila, osati cifukwa cakuti Mulungu anakonzelatu ‘mapulani’ ena osamvetsetseka.

MUNGAKHALE NA MOYO KWAMUYAYA PADZIKO LAPANSI

Kupanduka kwa mu Edeni sikunasinthe colinga ca Mulungu cimene anali naco poyamba cokhudza anthu na dziko lapansi. Cikondi cangwilo ca Mulungu na cilungamo cake, zinamusonkhezela kuti atimasule kuukapolo wa ucimo na imfa umene tinatengela. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Malipilo a ucimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Mwacikondi, Mulungu “anapeleka Mwana wake wobadwa yekha [Yesu Khristu], kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mwa kudzipeleka na mtima wonse kuti akhale nsembe ya dipo, Yesu anaombola zonse zimene Adamu anataya. a

Posacedwa, lonjezo la Mulungu la paradaiso padziko lapansi lidzakwanilitsidwa. Mungakhale na tsogolo labwino kwambili limeneli ngati mungacite zimene Yesu anakamba kuti: “Lowani pacipata copapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuciwonongeko, ndipo anthu ambili akuyenda mmenemo. Koma cipata colowela ku moyo n’copapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owelengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Inde, tsogolo lanu lidalila pa zosankha zimene mumapanga. Kodi imwe mudzacita ciani?

a Kuti mudziŵe zambili za mmene dipo ingakuthandizileni, onani nkhani 27 m’buku lakuti, Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! yopangiwa na Mboni za Yehova, limene mungacitile daunilodi pa webusaiti ya www.isa4310.com.