Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | KODI MUDZALANDILA MPHATSO YA MULUNGU YOPAMBANA ZONSE?

Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse N’cifukwa Ciani ni Yamtengo Wapatali?

Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse N’cifukwa Ciani ni Yamtengo Wapatali?

N’ciani cimacititsa mphatso kukhaladi yamtengo wapatali kwa imwe? Mwina cifukwa ca zinthu zinayi izi: (1) amene anakupatsani mphatsoyo, (2) cifukwa cimene anakupatsilani, (3) zimene anatailapo kuti akupatseni mphatsoyo, ndi (4) ngati mphatsoyo inakwanilitsa zosoŵa zanu. Kuganizila zinthu zimenezi kungatithandize kuyamikila kwambili dipo—mphatso ya Mulungu yopambana zonse.

AMENE ANAKUPATSANI MPHATSO

Mphatso zina ni za mtengo wapatali cifukwa amene anatipatsa ni munthu waudindo, kapena ni munthu amene timalemekeza kwambili. Koma mphatso zina, ngakhale kuti sizodula, timaziyamikila cifukwa zinacokela kwa wam’banja lathu amene timakonda, kapena mnzathu amene timadalila. Umu ndi mmene zinalili ndi mphatso imene a Russell, amene tawachula kuciyambi kwa nkhani yapita, anapatsa Jordan. Kodi izi zigwilizana bwanji ndi mphatso ya dipo?

Coyamba, Baibo imakamba kuti “Mulungu anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzela mwa iye.” (1 Yohane 4:9) Mfundo imeneyi ipangitsa dipo kukhala mphatso yamtengo wapatali. Palibe munthu amene ali na ulamulilo waukulu kupambana Mulungu. Pokamba za iye, wamasalimo waciheberi analemba kuti: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulila dziko lonse lapansi.” (Salimo 83:18) Sitikanalandila mphatso kucokela ku gwelo la ulamulilo.

Caciŵili, Mulungu ni “Atate wathu.” (Yesaya 63:16) Motani? Iye anatipatsa moyo. Kuwonjezela apo, amatisamalila mokhulupilika, monga mmene tate wacikondi amasamalila ana ake. Pochula ena mwa anthu ake akale kuti Efuraimu, Mulungu anafunsa kuti: “Kodi Efuraimu si mwana wanga wamtengo wapatali, kapena mwana wanga wokondedwa? . . . N’cifukwa cake m’mimba mwanga mukubwadamuka cifukwa ca iye. Mosalephela ndidzamumvela cisoni.” (Yeremiya 31:20) Mulungu amamvela cimodzi-modzi ndi alambili ake masiku ano. Si kuti iye ni Mlengi wamphamvuyonse cabe, koma alinso Atate wathu wokhulupilika ndi Mnzathu. Izi zikupangitsa kuti mphatso iliyonse yocokela kwa iye ikhale yamtengo wapatali.

CIFUKWA CIMENE ANAKUPATSILANI

Mphatso zina ni zamtengo wapatali cifukwa zimapelekewa kaamba ka cikondi cocokela pansi pamtima, osati cifukwa cakuti ni udindo wake kucita zimenezo. Munthu wopeleka mphatso moganizila ena sayembekezela kuti akamubwezele cifukwa ca kukoma mtima kwake.

Mulungu anatipatsa Mwana wake cifukwa amatikonda. Baibo imati ‘Mulungu anatisonyeza ife cikondi cake mwa kutumiza Mwana wake wobadwa yekha.’ Cifukwa ciani? “Kuti tipeze moyo kudzela mwa iye.” (1 Yohane 4:9) Kodi unali udindo wa Mulungu kucita zimenezi? Kutali-tali! “Dipo lolipilidwa ndi Khristu Yesu” limaonetsa ‘kukoma mtima kwakukulu’ kwa Mulungu.—Aroma 3:24.

N’cifukwa ciani mphatso ya Mulungu imaonetsa “kukoma mtima kwake kwakukulu”? Baibo imati: “Mulungu akuonetsa cikondi cake kwa ife, moti pamene tinali ocimwa, Khristu anatifela.” (Aroma 5:8) Cikondi copanda dyela cinacititsa Mulungu kuthandiza anthu ofooka, osoŵa thandizo, ndi ocimwa. Ife sitinali oyenelela kuonetsedwa cikondi cimeneco, komanso sitingakwanitse kumulipila. Dipo ndiye njila yaikulu imene Mulungu waonetsela cikondi cake m’mbili yonse ya anthu.

ZIMENE ANATAILAPO

Mphatso zina ni za mtengo wapatali cifukwa ca zimene wopelekayo watailapo. Ngati munthu wina watipatsa cinthu ca mtengo wapatali, timaiyamikila ngako mphatso imeneyo cifukwa ca zimene anatailapo.

Mulungu “anapeleka Mwana wake wobadwa yekha.” (Yohane 3:16) Palibe wina wapamtima pake amene akanatipatsa kuposa Yesu. Mkati mwa zaka zosaŵelengeka zimene Mulungu anali kulenga cilengedwe conse, Yesu anali pambali pake kugwila naye nchito. Mulungu anali kukondwela kwambili ndi iye. (Miyambo 8:30) Yesu ndiye “Mwana wokondedwa” wa Mulungu, komanso ni “cifanizilo ca Mulungu wosaonekayo” (Akolose 1:13-15) Palibe amene anakhalapo pa mgwilizano wokondana kwambili monga wa Mulungu ndi Yesu.

Komabe, Mulungu ‘sanatimane Mwana wake wa iye yekha.’ (Aroma 8:32 Buku Lopatulika) Yehova anatipatsa amene amakonda kwambili. Palibe mphatso ina imene anatailapo zambili kuposa iyi.

KUKWANILITSA COSOŴA CACIKULU

Mphatso zina ni za mtengo wapatali cifukwa zimakwanilitsa zosoŵa zathu, ngakhale zofunika kwambili. Mwacitsanzo, ngati wina wadzipeleka kuti atilipilile cithandizo ca ku cipatala kuti apulumutse moyo wathu, cimene ife sitingakwanitse kulipila, timayamikila kwambili. Zoona, mphatso imeneyo ingakhale yamtengo wapatali, si conco?

Baibo imati: “Monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akorinto 15:22) Pokhala ana a Adamu, tonse ‘timafa.’ Sitingapewe matenda ndi imfa. Ndipo sitingakhalenso paubale ndi Mulungu mwa ife tekha, ndi kukhala wopanda mlandu kwa iye. Pokhala anthu wamba, sitingadzipulumutse tekha kapena kupulumutsa wina. Baibo imati: “Palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene angathe kuwombola m’bale wake, kapena kumupelekela dipo kwa Mulungu . . . Munthu sangathe kuwapeleka mpaka kale-kale.” (Salimo 49:7, 8) Tifunikiladi thandizo cifukwa sitingakwanitse kulipila mtengo wa dipo. Patokha, tikanasoŵa cocita.

Cifukwa ca cikondi cake cacikulu, Yehova mofunitsitsa anatilipilila cithandizo ca “mankhwala” cimene tinali kufunikila kuti tipulumuke. Anacita izi kuti kupitila mwa Yesu ‘onse akapatsidwe moyo.’ Kodi dipo limakwanilitsa bwanji zimenezi? “Magazi a Yesu Mwana wake akutiyeletsa ku ucimo wonse.” Zoonadi, kukhulupilila magazi okhetsedwa a Yesu kumatsegula khomo kuti macimo athu akhululukidwe, komanso kuti tikapeze moyo wosatha. (1 Yohane 1:7; 5:13) Nanga dipo lidzapindulitsa bwanji okondeka athu amene anamwalila? “Popeza imfa inafika kudzela mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzela mwa munthu mmodzi [Yesu].”—1 Akorinto 15:21. *

Palibe mphatso yocokela kwa munthu waudindo, kapena imene inapelekedwa cifukwa ca cikondi cacikulu imene ingapose nsembe ya Yesu. Palibe munthu amene anatailapo zambili potipatsa mphatso kuposa zimene Yehova Mulungu anatailapo. Ndipo palibe mphatso imene inakwanilitsapo cosoŵa cathu cacikulu kuposa nsembe imene inatimasula ku ucimo ndi imfa. Kukamba zoona, pa mphatso zonse, palibe imene tingaiyelekezele na mtengo wa dipo umene sitingakwanitse kuufotokoza.

 

^ par. 19 Kuti mudziŵe zambili zokhudza colinga ca Mulungu codzaukitsa akufa, onani Nkhani 7 m’buku yakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Buku imeneyi ipezekanso pa www.isa4310.com.