Kodi Akristu Ayenela Kupita ku Tuakacisi Topatulika Kukalambila?
CAKA ciliconse, anthu oposa 6 miliyoni amayenda ulendo wautali wopita ku thengo la cedar pacilumba cochedwa Shima ku Japan. Amapita ku kacisi wamkulu wochedwa Ise kumene amalambila mulungu wamkazi wa dzuŵa wochedwa Amaterasu Omikami. Iwo akhala akulambila mulungu ameneyu kwa zaka 2,000. Coyamba, anthu amadziyeletsa mwa kusamba m’manja ndiponso pakamwa. Ndiyeno, amaimilila patsogolo pa kacisi wolambilila ndi kutsatila miyambo yao yomwe ndi kuŵelama, kuomba m’manja, ndi kupemphela kwa mulungu wao wamkazi. * Anthu a m’cipembedzo ca Cishinto amaloledwa kusakaniza zikhulupililo. Abuda ndiponso anthu amene amakamba kuti ndi Akristu, kuphatikizapo ena, amaona kuti palibe colakwika kucitako miyambo ya Cishinto m’kacisi ameneyu.
Zipembedzo zambili padziko lapansi zili ndi akacisi opatulika, * ndipo anthu ambili amapita ku akacisi amenewo. M’maiko amene anthu amadzicha kuti ndi Akristu muli machalichi ndi tuakacisi twambili topelekedwa kwa Yesu, Mariya, ndi kwa anthu oyela mtima. Tuakacisi twina tunamangidwa pamalo amene panacitikila cinthu cina cochulidwa m’Baibulo, kapena pamalo amene akuganizila kuti panacitikila “zozizwitsa” zinazake posacedwapa. Ena amamangidwa pamalo amene pamasungidwila zinthu zopatulika zacipembedzo. Anthu ambili amapita ku tuakacisi topatulika cifukwa amakhulupilila kuti mapemphelo ao adzayankhidwa ngati apelekedwela pamalo amenewo. Ena amaona kuti akafika ku tuakacisi topatulika pambuyo poyenda ulendo wautali, mpamene amaonetsa kuti ndi odzipeleka pa kulambila kwao.
Kodi mapemphelo ndi mapembedzelo opelekedwela mu tuakacisi amayankhidwa? Kodi Mulungu amasangalala ndi anthu amene amapanga ulendo wautali wopita ku tuakacisi kukalambila? Nanga kodi Akristu ayenela kupita ku tuakacisi kukalambila? Mayankho a mafunso amenewo adzatithandiza kudziŵa mmene tiyenela kuonela kulambila mu tuakacisi. Adzatithandizanso kudziŵa kulambila kumene kumakondweletsa Mulungu.
LAMBILANI “MOTSOGOLELEDWA NDI MZIMU NDI COONADI”
Makambilano amene Yesu anali nao ndi mai wa ku Samariya, amaonetsa mmene Mulungu amaonela kulambila pamalo opatulika kapena mu tuakacisi. Pamene Yesu anali kupita ku Samariya, anaimilila pa citsime pafupi ndi mzinda wa Sukari kuti apumule. Iye anayamba kukambilana ndi mai wina amene anabwela kudzatunga madzi pa citsimepo. Pamene anali kukambilana, maiyo anakamba kuti panali kusiyana kwakukulu pakati pa Ayuda ndi Asamariya pankhani yacipembedzo. Maiyo anati: “Makolo athu anali kulambila m’phili ili, koma anthu inu mumanena Yohane 4:5-9, 20.
kuti Yerusalemu ndiwo malo kumene anthu ayenela kulambililako.”—Maiyo anali kukamba Phili la Gerizimu, limene linali pa mtunda wa makilomita 50 kumpoto kwa Yerusalemu. Kumeneko kunali kacisi amene Asamariya anali kucitilako zikondwelelo monga cikondwelelo ca Pasika. Komabe, Yesu sanaike maganizo ake pa kusiyana kumene kunalipo pakati pao. M’malomwake, anauza maiyo kuti: “Mai, ndithu nthawi idzafika pamene anthu inu simudzalambila Atate m’phili ili kapena ku Yerusalemu.” (Yohane 4:21) Mau amenewa ndi odabwitsa kwambili, makamaka cifukwa cakuti amene anawakamba anali Myuda. N’cifukwa ciani kulambila Mulungu ku kacisi wa ku Yerusalemu kunali kudzathetsedwa?
Yesu anapitiliza kuti: “Nthawi idzafika, ndipo ndi yomwe ino, pamene olambila oona adzalambila Atate motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi, pakuti Atate amafuna otelowo azimulambila.” (Yohane 4:23) Kwa zaka zambili, Ayuda anali kuona kuti kacisi wa ku Yerusalemu anali likulu la kulambila kwao. Iwo anali kupita ku kacisi katatu pa caka kukapeleka nsembe kwa Mulungu wao, Yehova. (Ekisodo 23:14-17) Koma Yesu anakamba kuti zonsezi zidzatha, ndipo “olambila oona” adzalambila Mulungu “motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi.”
Kacisi wa Ayuda anali nyumba yeniyeni yomangidwa pamalo ena ake. Koma mzimu ndi coonadi si zooneka ndi maso, ndipo sizikhala pamalo ena ake. Apa Yesu anali kutanthauza kuti kulambila koona kwa Akristu sikudalila pa nyumba iliyonse kapena malo ena ake monga Phili la Gerizimu, kacisi wa ku Yerusalemu, kapena malo ena ake opatulika.
Pokambilana ndi mai wacisamariya, Yesu anakambanso kuti “nthawi” “idzafika” imene kulambila Mulungu mwa njila imeneyo kudzasintha. Kodi zimenezi zinali kudzacitika liti? Nthawi imeneyo inafika pamene Yesu anapeleka nsembe imene inathetsa njila imene Ayuda anali kulambilila yozikidwa pa Cilamulo ca Mose. (Aroma 10:4) Kenako, Yesu ananenanso kuti: “Nthawi . . . ndi yomwe ino.” N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti iye monga Mesiya, anali atayamba kale kusonkhanitsa ophunzila amene anali kudzamvela lamulo lotsatilali: “Mulungu ndiye Mzimu, ndipo onse omulambila ayenela kumulambila motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi.” (Yohane 4:24) Kodi kulambila motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi kumatanthauza ciani?
Pamene Yesu anakamba za kulambila motsogoleledwa ndi mzimu, iye anatanthauza kuti olambilawo adzatsogoleledwa ndi mzimu woyela wa Mulungu. Mzimu umenewu umatithandiza kucita zinthu zambili kuphatikizapo kumvetsetsa Malemba. (1 Akorinto 2:9-12) Ndipo coonadi cimene Yesu anakamba ndi ziphunzitso zolondola za m’Baibulo. Motelo, m’malo mokhala ndi malo ena ake apadela, kulambila kwathu kumakhala kovomelezeka kwa Mulungu ngati kumagwilizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, ndiponso ngati kumatsogoleledwa ndi mzimu woyela.
MMENE AKRISTU AYENELA KUONELA TUAKACISI
Kodi Akristu ayenela kuwaona bwanji maulendo opita kukalambila ku tuakacisi? Lamulo la Yesu lakuti olambila oona adzalambila Mulungu motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi, limaonetselatu kuti kulambila mu tuakacisi kapena pa malo opatulika sikukondweletsa Atate wathu wakumwamba. Kuonjezela apo, Baibulo limatiuza mmene Mulungu amaonela anthu amene amagwilitsila nchito mafano polambila. Limakamba kuti: “Thaŵani kupembedza mafano,” ndi kuti “pewani mafano.” (1 Akorinto 10:14; 1 Yohane 5:21) Conco, Akristu oona sayenela kulambila Mulungu pamalo amene anthu amaona kuti ndi opatulika kapena amene amalimbikitsa kupembedza mafano. Cifukwa ca mmene tuakacisito amatukonzela, Akristu oona amapewelatu kulambila pa malo amenewo.
Koma zimenezi sizitanthauza kuti Mau a Mulungu amaletsa kukhala ndi malo abwino kuti mupemphele, muphunzile, ndi kusinkhasinkha. Malo acete ndiponso oyenelela amathandiza anthu kuphunzila ndi kukambilana zinthu zakuuzimu bwinobwino. Ndipo sikulakwa kuika cipilala pa manda a munthu amene anafa. Kucita zimenezi kumangoonetsa kuti womwalilayo mumam’kumbukila ndi kuti mumam’konda kwambili. Koma kuona malo amenewo kukhala opatulika, kapena kulambila zithunzi komanso zinthu zakale zopatulika zacipembedzo pa malowo, sikugwilizana ndi zimene Yesu anakamba.
Cotelo, simufunika kucita kupita ku tuakacisi kukapemphela poganiza kuti m’pamene Mulungu adzayankha mapemphelo anu. Si kuti Mulungu adzakondwela nanu kapena kukudalitsani mwapadela cifukwa cakuti mwapanga ulendo wautali wopita ku tuakacisi. Baibulo limatiuza kuti Yehova Mulungu “sakhala mu akacisi opangidwa ndi manja. Iye ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.” Koma izi sizitanthauza kuti Mulungu ali kutali ndi ife. Tingapemphele kwa iye ndipo adzatimva kulikonse kumene tili cifukwa “iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”—Macitidwe 17:24-27.
^ par. 2 Miyambo imakhala yosiyana mu akacisi osiyanasiyana a Cishinto.
^ par. 3 Onani kabokosi kakuti “ Kodi Tuakacisi n’Ciani?”