N’cifukwa Ciani Mulungu Sayankha Mapemphelo Onse?
Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu, ni wokonzeka kumva mapemphelo athu ocokela pansi pa mtima ndipo amakondwela kutelo. Koma pali zinthu zina zimene zingapangitse kuti iye asamvetsele mapemphelo athu. Kodi zinthu zimenezo ni ziti? Nanga tiyenela kukumbukila ciani pamene tipemphela? Onani malangizo ena awa a m’Baibo.
“Iwe popemphela, usanene zinthu mobwelezabweleza.”—Mateyu 6:7.
Yehova safuna kuti tizipeleka mapemphelo oloŵeza pamtima kapena ocita kuwaŵelenga m’buku. Koma amafuna kuti tizikamba naye kucokela mumtima. Kodi mungamvele bwanji ngati mnzanu amabwela na kukuuzani mawu amodzi-modzi tsiku lililonse? Simungamvele bwino. Mabwenzi abwino amakambilana momasuka komanso moona mtima. Ngati tikamba mawu athu-athu popemphela kwa Atate wathu wakumwamba, zimaonetsa kuti timamuona kuti ni bwenzi lathu.
“Mumapempha koma simulandila, cifukwa mukupempha ndi colinga coipa.”—Yakobo 4:3.
Tidziŵa kuti Mulungu sangayankhe mapemphelo athu ngati tipempha zinthu zimene amaletsa. Mwacitsanzo, kodi Yehova angayankhe pemphelo la munthu wanjuga lopempha kuti awine njugayo pamene iye amaletselatu kucita zinthu mwadyela komanso kukhulupilila mulungu wamwayi? (Yesaya 65:11; Luka 12:15) Ndithudi, Yehova sangayankhe mapemphelo otelo! Conco, kuti Mulungu ayankhe mapemphelo athu, tifunika kuonetsetsa kuti zimene tipempha n’zogwilizana na zimene iye amatiuza m’Baibo.
Miyambo 28:9.
“Munthu amene amathaŵitsa khutu lake kuti asamve cilamulo, ngakhale pemphelo lake limakhala lonyansa.”—
M’nthawi yakale, Mulungu sanali kuyankha mapemphelo a anthu amene sanali kumvela malamulo ake olungama. (Yesaya 1:15, 16) Iye sanasinthe. (Malaki 3:6) Ngati tifuna kuti Mulungu azimvetsela mapemphelo athu, tiyenela kuyesetsa kumvela malamulo ake. Koma bwanji ngati tinacitapo zinthu zinazake zoipa m’mbuyomo? Kodi ndiye kuti basi Yehova sadzamvetselanso mapemphelo athu? Iyai! Iye adzatikhululukila ngati titembenuka na kuyesetsa kucita zinthu zomukondweletsa.—Machitidwe 3:19.