Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muzicilikiza Ulamulilo wa Yehova

Muzicilikiza Ulamulilo wa Yehova

“Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu, cifukwa munalenga zinthu zonse.”—CHIV. 4:11.

NYIMBO: 112, 133

1, 2. Kodi aliyense payekha afunika kutsimikizila za ciani? (Onani pikica pamwambapa.)

MALINGA n’zimene tinakambilana m’nkhani yapita, Mdyelekezi amakamba kuti Yehova si wolamulila wabwino. Amakambanso kuti anthu angakhale na umoyo wabwino ngati adzilamulila okha. Kodi zimenezi n’zoona? Tiyelekezele kuti anthu amene asankha kudzilamulila alinso na moyo wosatha. Kodi angakhale na umoyo wabwino popanda ulamulilo wa Mulungu? Mukanakhala kuti mudzilamulila mwekha ndipo muli na moyo wosatha, kodi muganiza kuti mukanakhala na umoyo wacimwemwe?

2 Palibe munthu amene angakuyankhileni mafunso amenewa. Aliyense payekha afunika kuiganizila nkhaniyi. Ndipo inu pamwekha mufunika kutsimikiza kuti Mulungu ndiye woyeneladi kulamulila, ndi kuti ulamulilo wake ndiwo wabwino ngako. Komanso tifunika kuucilikiza na mtima wonse. Baibo imapeleka zifukwa zotithandiza kukhulupilila kuti Yehova ali na ufulu wolamulila cilengedwe conse. Tiyeni tikambilane zina mwa zifukwa zimenezi.

YEHOVA NDIYE WOYENELA KULAMULILA

3. N’cifukwa ciani Yehova yekha ndiye woyenela kulamulila cilengedwe conse?

3 Yehova ndiye woyenela kulamulila cilengedwe conse cifukwa ni Mulungu wamphamvuyonse ndiponso ni Mlengi. (1 Mbiri 29:11; Mac. 4:24) Pa Chivumbulutso 4:11, a 144,000 amene adzalamulila pamodzi na Khristu kumwamba anaonekela m’masomphenya akukamba kuti: “Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu, cifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” Inde, popeza kuti Yehova analenga zinthu zonse, iye ali na ufulu wonse wolamulila anthu kuphatikizapo zolengedwa zauzimu.

4. N’cifukwa ciani kutsutsa ulamulilo wa Mulungu n’kusaseŵenzetsa bwino ufulu wosankha?

4 Satana sanalengeko cinthu ciliconse. N’cifukwa cake iye alibe ufulu wolamulila cilengedwe. Pamene Satana ndi anthu aŵili oyambilila anapandukila ulamulilo wa Yehova, iwo anacita zinthu modzikuza. (Yer. 10:23) N’zoona kuti analengedwa na ufulu wodzisankhila zocita, ndipo palibe cikanawaletsa kusankha kudzilamulila okha popanda Mulungu. Koma kodi cinali coyenela iwo kucita zimenezi? Iyayi. Kukhala na ufulu wosankha kumathandiza anthu kusankha zocita mwanzelu tsiku lililonse. Koma ufuluwo supatsa anthu mphamvu yopandukila Mlengi wawo amene anawapatsa moyo. Kunena zoona, kupandukila Yehova n’kusaseŵenzetsa bwino ufulu wathu wodzisankhila zocita. Anthufe tifunika kugonjela ulamulilo wolungama wa Yehova.

5. N’cifukwa ciani ndise otsimikiza kuti zigamulo za Yehova n’zolungama?

5 Palinso cifukwa cina cimene cipangitsa Yehova kukhala woyenela kulamulila. Iye amalamulila mwacilungamo. Mulungu anati: “Ine ndine Yehova, amene ndimasonyeza kukoma mtima kosatha, ndimapeleka ziweluzo ndi kucita cilungamo padziko lapansi. Pakuti zinthu zimenezi zimandisangalatsa.” (Yer. 9:24) Mulungu sadalila buku lililonse la malamulo opangidwa ndi anthu opanda ungwilo kuti adziŵe cimene cili colungama ndi coyenela. Cilungamo ni mbali ya umunthu wake, ndipo malamulo amene iye anapatsa anthu ni ogwilizana ndi cilungamo cakeco. Wamasalimo anati: “Cilungamo ndi ciweluzo ndizo maziko a mpando [wake] wacifumu.” Conco, tili na cikhulupililo cakuti malamulo ake, mfundo zake, ndi zigamulo zake, zonse n’zolungama. (Sal. 89:14; 119:128) Ngakhale kuti Satana amakamba kuti ulamulilo wa Yehova ni wolephela, iye wakangiwa kukonza zinthu padziko kuti pakhale cilungamo.

6. Chulani cifukwa cimodzi cimene Yehova alili woyenela kulamulila dziko.

6 Cina cimene cipangitsa Yehova kukhala woyenela kulamulila n’cakuti ali na cidziŵitso ndi nzelu zom’thandiza kusamalila bwino cilengedwe. Mwacitsanzo, ganizilani mmene Mulungu anathandizila mwana wake kupoletsa matenda amene madokota analephela kucilitsa. (Mat. 4:23, 24; Maliko 5:25-29) Yehova sanaone kuti zimene Yesu anacita n’zozizwitsa. Iye amadziŵa mmene thupi limagwilila nchito, ndipo ali na mphamvu zopoletsa matenda aliwonse. Alinso na mphamvu zoukitsa akufa ndi kuthetsa masoka a zacilengedwe.

7. Kodi nzelu za Yehova zimaposa bwanji nzelu za anthu a m’dziko lolamulidwa na Satana?

7 Anthu m’dziko lolamulidwa na Satana, alephela kupeza njila zothetsela nkhondo padziko. Ni Yehova cabe amene ali na nzelu zimene zingathandize kuti padziko pakhale mtendele. (Yes. 2:3, 4; 54:13) Tikaganizila cidziŵitso na nzelu zimene Mulungu ali nazo, timamvela monga mmene mtumwi Paulo anamvelela pamene analemba kuti: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapeleka ndi oculuka kwambili. Nzelu zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziŵa zinthu kwambili. Ziweluzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukile njila zake?”—Aroma 11:33.

ULAMULILO WA YEHOVA NDIWO WABWINO NGAKO

8. N’ciani cimakukondweletsani na kalamulidwe ka Yehova?

8 Baibo imapeleka zifukwa zomveka bwino zoonetsa kuti Yehova ni woyeneladi kulamulila. Komanso imafotokoza zinthu zimene zicititsa ulamulilo wake kukhala wabwino kuposa maulamulilo ena. Cimodzi n’cakuti iye amalamulila mwacikondi. Kukamba zoona, timacita cidwi na mmene Mulungu amalamulilila. Iye ni “wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi.” (Eks. 34:6) Mulungu amalemekeza atumiki ake. Amatisamalila kuposa mmene ise tingadzisamalile. Mosiyana ndi bodza limene Mdyelekezi anakamba, Yehova samana olambila ake okhulupilika zinthu zilizonse zabwino. Ndiye cifukwa cake anapeleka mwana wake wokondedwa kuti ise tikhale na ciyembekezo ca moyo wosatha.—Ŵelengani Masalimo 84:11; Aroma 8:32.

9. Tidziŵa bwanji kuti Mulungu amatikonda aliyense payekha?

9 Yehova amakonda anthu ake osati monga gulu cabe, koma amakondanso aliyense payekha. Mwacitsanzo, kwa zaka 300, Yehova anali kusankha oweluza ndi kuwapatsa mphamvu kuti apulumutse mtundu wa Isiraeli kwa anthu amene anali kuwazunza. Pa nthawi yovuta imeneyo, Mulungu sanalephele kukomela mtima Rute, amene sanali mwiisiraeli. Iye anadzimana zambili kuti akhale wolambila woona. Yehova anadalitsa Rute mwa kum’patsa mwamuna ndi mwana. Koma sizinathele pamenepo. Rute akadzaukitsidwa, adzakondwela kudziŵa kuti mwana wake anali mbali ya mnzele wobadwila wa Mesiya. Ganinilaninso cimwemwe cimene iye adzakhala naco, akadzadziŵa kuti mbili yake inalembedwa m’buku la m’Baibo lodziŵika na dzina lake.—Rute 4:13; Mat. 1:5, 16.

10. N’cifukwa ciani tingakambe kuti ulamulilo wa Yehova si wopondeleza?

10 Ulamulilo wa Yehova si wopondeleza koma ni wololela. Umalimbikitsa anthu kukhala na umoyo waufulu ndi wacimwemwe. (2  Akor. 3:17) Davide anakamba kuti: “Ulemu ndi ulemelelo zili pamaso pake [pa Mulungu], pokhala pake pali mphamvu ndi cimwemwe.” (1 Mbiri 16:7, 27) Komanso wamasalimo wina, dzina lake Etani, analemba kuti: “Odala ndi anthu amene amafuula mosangalala. Iwo amayendabe m’kuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova. Iwo amakondwela ndi dzina lanu tsiku lonse. Cilungamo canu cimawakweza.”—Sal. 89:15, 16.

11. Tingacite ciani kuti tizikhulupilila kwambili kuti ulamulilo wa Yehova ndiwo wabwino koposa?

11 Kuganizila mozama za ubwino wa Yehova nthawi zonse, kungatithandize kukhulupilila kwambili kuti ulamulilo wake ndiwo wabwino koposa. Timafika pomvela monga mmene wamasalimo wina anamvelela. Iye anati: “Kukhala tsiku limodzi m’mabwalo anu n’kwabwino kuposa kukhala masiku 1,000 kwina.” (Sal. 84:10) Izi n’zosadabwitsa cifukwa, monga Mlengi wathu wacikondi, Yehova amadziŵa bwino zimene timafunikila kuti tikhale na cimwemwe ceni-ceni, ndipo amatipatsa zonse zofunikila. Zilizonse zimene amatiuza kucita zimatipindulitsa ndi kutipatsa cimwemwe cosaneneka, ngakhale kuti nthawi zina tingafunike kudzimana zinthu zina.—Ŵelengani Yesaya 48:17.

12. Kodi cifukwa cikulu cimene tiyenela kucilikizila ulamulilo wa Yehova n’citi?

12 Baibo imaonetsa kuti pambuyo pa Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000, anthu ena adzapandukila ulamulilo wa Yehova. (Chiv. 20:7, 8) N’ciani cidzawasonkhezela kucita zimenezi? Mdyelekezi akadzamasulidwa m’ndende yake adzakhalanso na colinga cosoceletsa anthu. Mwacidziŵikile, iye adzakopa anthu mwa kuwalimbikitsa kukhala na mtima wadyela, ngati mmene wakhala akucitila nthawi yonseyi. Mwina adzayesa kucititsa anthu kukhulupilila kuti akhoza kukhala na moyo wosatha popanda kumvela Yehova. Koma limenelo lidzakhala bodza. Ngakhale n’conco, tingafunse kuti: ‘Kodi inu mudzakopeka na bodza limenelo?’ Ngati timakonda Yehova na kum’tumikila cifukwa cakuti ni wabwino ndipo ndiye woyenela kulamulila cilengedwe conse, sitidzakopeka ngakhale pang’ono na bodza la Satana. Tidzakhala ofunitsitsa kulamulidwa ndi Yehova, amene ndiye woyenela kulamulila ndipo amalamulila mwacikondi.

MUZICILIKIZA ULAMULILO WA MULUNGU MOKHULUPILIKA

13. Tingaonetse bwanji kuti tikucilikiza ulamulilo wa Mulungu?

13 Kukamba zoona, ulamulilo wa Yehova ni wofunika kuucilikiza na mtima wathu wonse. Monga taonela, iye ali na ufulu wolamulila, ndipo ulamulilo wake ndiwo wabwino koposa. Tingacilikize ulamulilo wa Yehova mwa kukhala na mtima wosagaŵanika ndi kum’tumikila mokhulupilika. Kodi n’ciani cina cimene tingacite pocilikiza ulamulilo wa Mulungu? Tifunika kucita zinthu mmene Yehova amafunila. Ngati titengela Yehova pocita zinthu, timaonetsa kuti tikucilikiza ulamulilo wake.—Ŵelengani Aefeso 5:1, 2.

14. Kodi akulu na mitu ya mabanja angatengele bwanji citsanzo ca Yehova?

14 M’Baibo, timaphunzila kuti Yehova amalamulila mwacikondi. Mofananamo, mitu ya mabanja ndi akulu amene amakonda ulamulilo wa Mulungu sacita kukakamiza anthu kuwamvela, monga kuti anakhazikitsa kaulamulilo kawo. M’malomwake, iwo amatengela citsanzo ca Yehova. Paulo anali citsanzo cabwino pa nkhani yotengela Mulungu ndi Mwana wake. (1 Akor. 11:1) Iye sanali kucititsa manyazi anthu ena kapena kuwakakamiza kucita zinthu zinazake. M’malomwake, anali kuwacondelela. (Aroma 12:1; Aef. 4:1; Filim. 8-10) Umu ni mmene Yehova amacitila zinthu. Conco, onse amene amakonda ndi kucilikiza ulamulilo wa Mulungu afunika kucita zimenezi.

15. Kodi kulemekeza dongosolo la umutu kumaonetsa bwanji kuti timakonda ulamulilo wa Yehova?

15 Kodi ise tifunika kucita ciani na makonzedwe a umutu amene Mulungu anakonza? Ngati ticita zinthu mogwilizana ndi amene akutitsogolela, timaonetsa kuti tikucilikiza ulamulilo wa Yehova. Ngakhale kuti zimene iwo asankha ise sitinazikonde, tifunikabe kucilikiza dongosolo la Mulungu. Izi n’zosiyana ndi zimene anthu a m’dzikoli amacita. Koma ndiye mmene tifunika kucitila ngati tifuna kucilikiza ulamulilo wa Yehova. (Aef. 5:22, 23; 6:1-3; Aheb. 13:17) Kucita zimenezi kudzatipindulitsa ngako cifukwa Mulungu amatifunila zabwino.

16. Kodi anthu amene amacilikiza ulamulilo wa Mulungu amapanga bwanji zosankha?

16 Zosankha zathu zingaonetsenso kuti timacilikiza ulamulilo wa Mulungu. Yehova satipatsa malamulo acindunji pankhani zina. Iye potitsogolela amatiuza cabe maganizo ake. Mwacitsanzo, safotokoza mfundo zambili zokhudza zovala zimene Akhristu angavale. Iye amangotiuza kuti monga Akhristu, tifunika kuvala na kudzikongoletsa moyenelela. (1 Tim. 2:9,10) Mulungu amafunanso kuti tizipewa zosankha zimene zingakhumudwitse kapena kusokoneza ena. (1 Akor. 10:31-33) Sitiyenela kungotsatila zofuna zathu popanga zosankha. Koma tifunika kusankha mogwilizana ndi maganizo a Yehova ndi zofuna zake. Tikatelo, tidzaonetsa kuti timakonda ndi kucilikiza ulamulilo wake.

Muzicilikiza ulamulilo wa Mulungu popanga zosankha ndi pocita zinthu m’banja (Onani palagilafu 16-18)

17, 18. Ni njila zina ziti zimene anthu a m’cikwati angaonetsele kuti amacilikiza ulamulilo wa Yehova?

17 Ganizilani zimene Akhristu amene ali pabanja angacite kuti atengele citsanzo ca Yehova ndi kucilikiza ulamulilo wake. Kodi angacite ciani ngati akuona kuti umoyo wa m’cikwati ni wovuta kwambili kuposa mmene anali kuganizila? Nanga bwanji ngati akuona kuti agwilitsidwa mwala? Angacite bwino kuganizila mmene Yehova anali kucitila zinthu ndi Aisiraeli. Mulungu anakamba kuti anali monga mwamuna wa mtundu wakale umenewu. (Yes. 54:5; 62:4) Cimeneci ciyenela kuti cinali ‘cikwati’ covuta ngako. Olo kuti zinali conco, Yehova sanafulumile kuusiya mtundu umenewu. Anapitilizabe kuucitila cifundo, ndipo anakhalabe wokhulupilika pa pangano lake ndi iwo. (Ŵelengani Masalimo 106:43-45.) Kukamba zoona, kukoma mtima kosatha kwa Yehova kumaticititsa kukhala naye paubwenzi wolimba.

18 Nawonso anthu apabanja, amene amakonda ulamulilo wa Yehova angatengele citsanzo cake. Ngati iwo akumana ndi mavuto m’cikwati, safunika kufuna-funa njila zosakhala za m’Malemba zothetsela cikwati. Iwo amazindikila mfundo yakuti Yehova ndiye anawamanga pamodzi, ndipo afuna kuti iwo akhale ‘ophatikana’ kwa wina ndi mnzake. Maziko okha a m’Malemba amene amapatsa munthu ufulu wothetsa cikwati na kukwatilanso kapena kukwatiwanso, ndi cigololo cabe. (Mat. 19:5, 6, 9) Inde, anthu a m’cikwati angacilikize ulamulilo wolungama wa Yehova mwa kucita zonse zimene angathe kuti alimbitse cikwati cawo.

19. Kodi tiyenela kucita ciani ngati talakwitsa zinazake n’kulephela kucilikiza ulamulilo wa Mulungu?

19 Popeza ndise anthu opanda ungwilo, nthawi zina tingacite zinthu zokhumudwitsa Yehova. Iye amadziŵa zimenezi, ndipo cifukwa ca cikondi cake anatipatsa dipo kudzela mwa Khristu. Conco tikalakwitsa m’mbali zina, tizipempha Yehova kuti atikhululukile. (1 Yoh. 2:1, 2) M’malo mongokhalila kudziimba mlandu, tiziyesetsa kuphunzilapo kanthu pa zimene tinalakwitsa. Ngati tili paubwenzi wabwino na Yehova, iye adzatikhululukila, adzatithandiza kucila mwauzimu, ndi kutipatsa mphamvu kuti tisagonje ngati tayesedwanso kuti ticite chimo.—Sal. 103:3.

20. N’cifukwa ciani ino ndiyo nthawi yofunika kuonetsa kuti tikucilikiza ulamulilo wa Yehova?

20 M’dziko latsopano, anthu onse adzakhala pansi pa ulamulilo wa Yehova, ndipo adzaphunzila njila zake zolungama. (Yes. 11:9) Komabe, masiku ano timaphunzilanso zambili. Ndipo nkhani yokhudza ulamulilo wa Mulungu siinathe. Conco, ino ndiyo nthawi yofunika kucilikiza ulamulilo wa Mulungu. Tingaucilikize mwa kukhala wokhulupilika, kucita utumiki wathu ndi mtima wonse, ndi kucita zonse zotheka kuti titengele citsanzo ca Mulungu pa zilizonse zimene timacita paumoyo.