PHUNZILO 2
Mmene Angakhalile Odzicepetsa
KODI KUDZICEPETSA N’CIANI?
Anthu odzicepetsa amakhala aulemu. Sacita zinthu modzitukumula, kapena kufuna kuti anthu ena aziwaona kuti ni apadela. M’malo mwake, munthu wodzicepetsa amakhala na cidwi mwa anthu ena, ndipo amafuna kuphunzila kwa ena.
Ena amaganiza kuti munthu akakhala wodzicepetsa ni wamantha. Koma m’ceni-ceni, kudzicepetsa kumathandiza anthu kudziŵa zimene amalakwitsa, komanso kuvomeleza zolephela zawo.
N’CIFUKWA CIANI KUDZICEPETSA N’KOFUNIKA?
-
Kudzicepetsa kumalimbitsa maubwenzi. Buku lochedwa The Narcissism Epidemic limati: “Anthu odzicepetsa nthawi zambili savutika kupeza mabwenzi.” Bukulo linakambanso kuti kwa anthu odzicepetsa cimakhala “cosavuta kukambilana komanso kuceza na anthu ena.”
-
Kudzicepetsa kudzam’thandiza mwana wanu kutsogolo. Kuphunzila kukhala wodzicepetsa kudzathandiza mwana wanu pali pano, komanso kutsogolo akadzakula. Mwacitsanzo, sangadzavutike kwambili kupeza nchito. Dr. Leonard Sax analemba kuti: “Acinyamata odzidalila kwambili, komanso osazindikila kuti pali zinthu zina zimene sadziŵa, nthawi zambili amalephela pa maintavyu a nchito. Koma acinyamata omvetsela modzicepetsa ku mafunso pa maintavyu, kaŵili-kaŵili amapeza mwayi wanchito.” *
MMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA KUDZICEPETSA
Thandizani mwana wanu kusadzikweza.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotelo, akudzinyenga.”—Agalatiya 6:3.
-
Pewani mawu otamanda koma osoceletsa. Mawu monga akuti “ungakwanilitse zolinga zako zonse,” kapena, “ungakwanitse kucita zilizonse zimene ufuna,” angamveke olimbikitsa, koma zimenezo si zoona kweni-kweni. Ana anu angakhale na umoyo wabwino, ngati akhala na zolinga zimene angazikwanitse zoona.
-
Muzimuyamikila pa zinthu zimene acitadi bwino. Kuuza mwana wanu mwacisawawa kuti “umacita bwino kwambili,” sikungam’thandize kukhala wodzicepetsa. Chulani mwacindunji zeni-zeni zimene wacita bwino.
-
Mulimbikitseni kucepetsa maceza a pa intaneti. Nthawi zambili, anthu pa malo amaceza a pa intaneti, amadzionetsela na zimene ali nazo. Iwo amalengeza maluso awo na zimene akwanilitsa mu umoyo wawo. Izi n’zosiyana kwambili na kudzicepetsa.
-
Phunzitsani mwana wanu kumapepesa mwamsanga. Mwana wanu akalakwa, m’thandizeni kumvetsa cimene walakwaco, na kuti acivomeleze.
M’phunzitseni kuyamikila.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Sonyezani kuti ndinu oyamikila.” —Akolose 3:15.
-
Kuyamikila zacilengedwe. Ana afunika kuyamikila zacilengedwe, na kudziŵa mmene zinthu zacilengedwe zimatithandizila kuti tikhale na moyo. Mwacitsanzo, timafunikila mpweya, madzi akumwa, na zakudya. Mungakambilane naye mbali zimenezi pom’thandiza kuyamikila zinthu zonse za m’cilengedwe.
-
Kuyamikila anthu. Thandizani mwana wanu kudziŵa kuti munthu aliyense amam’posa pa mbali zina. Ndipo m’malo mwakuti azicitila anthu ena nsanje cifukwa ca maluso awo, na zimene angakwanitse kucita, m’thandizeni kuona kuti angaphunzile zina kwa iwo.
-
Kukamba mawu oyamikila. Phunzitsani ana anu kukamba kuti zikomo. Koma afunika kumakamba mawu amenewa mocokela pansi pa mtima. Kuyamikila kumatithandiza kukhala odzicepetsa.
Phunzitsani ana anu kudziŵa kuti kuthandiza ena n’kofunika.
MFUNDO YA M’BAIBO: ‘Modzicepetsa ndi kuona ena kukhala okuposani, musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.’—Afilipi 2:3, 4.
-
Thandizani mwana wanu kugwila nchito za pakhomo. Ngati simulola mwana wanu kugwila nchito za pakhomo, angayambe kudziona kuti ni wapadela kwambili ndipo safunika kugwila nchitozo. Nchito za pakhomo zifunika kukhala patsogolo maseŵela pambuyo. M’thandizeni kuona kuti nchito za pakhomo zimene angacite, zimapindulitsa ena, ndipo amam’konda cifukwa cogwila nchitozo.
-
Gogomezani ubwino wothandiza ena. Kucitila ena zabwino kudzathandiza mwana wanu kukhwima m’maganizo. Conco, m’thandizeni kupeza anthu amene angafunikile thandizo. Ndiyeno kambilanani naye zimene angacite kuti awathandize. Pamene ayesa-yesa kuthandiza ena, muyamikileni na kum’cilikiza.
^ par. 8 Kucokela m’buku lakuti, The Collapse of Parenting.