Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Onetsani Cifundo

Onetsani Cifundo

Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta

Ngati timakonda kuganizila mmene ena alili osiyana na ife, tingayambe kuwaona ngati ali na vuto. Ndiponso tingayambe kuona kuti anthu amene ni osiyana na ise ni otsalila. Tikakhala na maganizo aconco, cimakhala covuta kuwaonetsa cifundo anthu otelo. Kusoŵa cifundo kumeneko kungakhale cizindikilo cakuti tili na vuto lalikulu—tsankho.

Mfundo ya m’Baibo

“Sangalalani ndi anthu amene akusangalala. Lilani ndi anthu amene akulila.” —AROMA 12:15.

Kodi mfundo imeneyi itanthauza ciani? Mfundo imeneyi itiphunzitsa kuti tifunika kuonetsa cifundo kwa ena. Cifundo ni khalidwe lotha kuganizila mmene munthu wina amvelela, komanso mmene ife tikanamvelela sembe tinali munthu ameneyo.

Kodi Cifundo Cimathandiza Bwanji?

Tikamaonetsa cifundo kwa munthu, timayamba kuzindikila kuti ndife ofanana naye m’njila zambili. Tingazindikile kuti iye amamvela na kucita zinthu monga mmene ifenso timacitila. Cifundo cimatithandiza kuona kuti anthu onse, kaya ni a mtundu wotani, ni banja limodzi. Ngati tiganizila kwambili kufanana kumene kulipo pakati pa anthu ena na ife, timayamba kuwaona moyenela anthuwo.

Cifundo cimatithandizanso kuti tizilemekeza ena. Mwacitsanzo, ganizilani za Anne-Marie wa ku Senegal. M’dziko lawo muli mtundu wina wa anthu amene ambili amawaona kuti ni otsika. Nayenso Anne-Marie anali kuwaona kuti ni otsika anthu amenewo. Koma anafotokoza mmene cifundo cinam’thandizila kuthetsa vutoli. Anati: “Pamene n’naona mavuto amene anthu a mtundu umenewo anali kukumana nawo, n’nayamba kuganizila mmene ine nikanamvelela sembe n’nali wa mtundu umenewo. Izi zinanithandiza kuzindikila kuti sindine wapamwamba kuposa iwo, komanso kuti palibe ciliconse cimene n’nacita conipangitsa kukhala wapamwamba kuposa iwo.” Zoonadi, ngati tiyesetsa kumvetsetsa mavuto amene ena amakumana nawo, tidzawamvelela cifundo ndiponso tidzapewa kuwakambila zoipa.

Zimene Mungacite

Ngati anthu a mtundu winawake mumawaona molakwika, yesetsani kuganizila zinthu zimene imwe na iwo mumafanana. Mwacitsanzo, ganizilani mmene iwo amamvelela:

Cifundo cimatithandiza kuona kuti anthu onse ni banja limodzi

  • pamene akudya cakudya pamodzi na banja lawo

  • akakomboka kunchito pambuyo pogwila nchito yolemetsa

  • pamene aceza na anzawo

  • pamene amvetsela nyimbo zimene amakonda

Ndiyeno, yesetsani kuganizila mmene mukanamvelela sembe munali iwo. Dzifunseni kuti:

  • ‘Kodi ningamvele bwanji ngati wina wakamba mawu kapena kucita zinthu zonipangitsa kudziona wosafunika?’

  • ‘Ningamvele bwanji ngati ena aninena kuti ndine woipa pamene akalibe kunidziŵa bwino?’

  • ‘Kodi nikanakhala mmodzi wa iwo, sembe nifuna kuti anthu ena azicita nane zinthu motani?’