N’zotheka Kupeza Nzelu
“Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Pa vesiyi, mawu akuti “anauzilidwa” amatanthauza kuti Mulungu Wamphamvuzonse anaika maganizo ake m’mitima ya anthu amene analemba Baibo.
Mulungu Akukupemphani Kuti Mupindule na Nzelu Zake
“Ine Yehova . . . ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, . . . ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo. Zingakhale bwino kwambili mutamvela malamulo anga! Mukatelo mtendele wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo cilungamo canu cidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.”—YESAYA 48:17, 18.
Mawu a pa vesiyi atengeni monga ciitanilo canu cocokela kwa Mulungu. Iye amafuna kuti mukhale na mtendele wa maganizo komanso cimwemwe cokhalitsa, ndipo angakuthandizeni kuzipeza.
N’zotheka Imwe Kupeza Nzelu Zocokela kwa Mulungu
“M’mitundu yonse uthenga wabwino uyenela ulalikidwe.”—MALIKO 13:10.
“Uthenga wabwino” uphatikizapo malonjezo a Yehova akuti adzathetsa kuvutika, adzapanga dziko kukhala paradaiso, komanso adzaukitsa akufa. Mboni za Yehova zimalalikila uthenga wa m’Baibo umenewu padziko lonse.