Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 28

Muziyamikila pa Zimene Yehova na Yesu Anakucitilani

Muziyamikila pa Zimene Yehova na Yesu Anakucitilani

Kodi mungamve bwanji ngati mnzanu wakupatsani mphatso yabwino kwambili? Mwacidziŵikile mungakondwele ngako, ndipo mungamuyamikile cifukwa ca mphatso imeneyo. Yehova na Yesu anatipatsa dipo monga mphatso yopambana ina iliyonse. Kodi mphatso imeneyo ni ciyani? Ndipo tingacite ciyani poonetsa kuti timawayamikila cifukwa ca mphatso imeneyo?

1. Kodi njila imodzi yoyamikila zimene Mulungu na Khristu anaticitila ni iti?

Baibo imalonjeza kuti “aliyense wokhulupilila [Yesu]” angapeze moyo wosatha. (Yohane 3:16) Kodi mawu akuti ‘kukhulupilila’ atanthauza ciyani? Atanthauza kucita zambili kuposa kungokhulupilila cabe mwa Yesu. Timaonetsa cikhulupililo mwa zisankho zimene timapanga, komanso mwa zimene timacita. (Yakobo 2:17) Tikamaonetsa cikhulupililo cathu mwa zocita na zokamba zathu, timalimbitsa ubwenzi wathu na Yesu, komanso Atate wake Yehova.—Ŵelengani Yohane 14:21.

2. N’cocitika capadela citi cimene cimatipatsa mwayi woyamikila zimene Yehova na Yesu anaticitila?

Madzulo pa tsiku limene Yesu anaphedwa, iye anaonetsa otsatila ake njila ina yoyamikila nsembe yake. Anayambitsa mwambo wapadela umene Baibo imaucha “cakudya camadzulo ca Ambuye,” kapena kuti Mgonelo wa Ambuye, wodziŵikanso kuti Cikumbutso ca imfa ya Khristu. (1 Akorinto 11:20) Yesu anakhazikitsa mwambo umenewu na colinga cakuti atumwi ake, komanso Akhristu onse oona obwela pambuyo pawo, tizikumbukila kuti Yesu anapeleka moyo wake kaamba ka ife. Pa mwambo umenewu, Yesu analamulanso kuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.” (Luka 22:19) Mukapezeka pa Cikumbutso, mumaonetsa kuyamikila cikondi cacikulu cimene Yehova na Yesu anationetsa.

KUMBANI MOZAMILAPO

Pezani njila zina zoyamikila cikondi cacikulu cimene Yehova na Yesu anationetsa. Ganizilani za kufunika kwa Cikumbutso ca imfa ya Khristu.

3. Kuyamikila kumatilimbikitsa kucitapo kanthu

Yelekezani kuti munali kumila pamadzi, ndiye munthu wina wakupulumutsani. Kodi mudzangocokapo n’kuiŵalako zimene munthuyo wakucitilani? Kapena mungapeze njila zomuyamikila pa zimene iye wakucitilani?

Tidzapeza moyo wosatha cifukwa ca cisomo ca Yehova. Ŵelengani 1 Yohane 4:8-10, na kukambilana mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani nsembe ya Yesu ni mphatso yapadela kwambili?

  • Kodi mumamva bwanji pa zimene Yehova na Yesu anakucitilani?

Kodi tingayamikile motani zimene Yehova na Yesu anaticitila? Ŵelengani 2 Akorinto 5:15, komanso 1 Yohane 4:11; 5:3. Pambuyo poŵelenga iliyonse ya Malemba awiliwa, kambilanani funso ili:

  • Malinga na lembali, tiyenela kucita ciyani kuti tionetse kuyamikila kwathu?

4. Tengelani citsanzo ca Yesu

Njila ina imene tingaonetsele kuyamikila kwathu ni kutengela citsanzo ca Yesu. Ŵelengani 1 Petulo 2:21, na kukambilana funso ili:

  • Ni njila ziti zimene tingatsatilile mapazi a Yesu mosamalitsa?

5. Muzipezeka pa Cikumbutso ca imfa ya Khristu

Kuti muone mmene unacitikila Mgonelo woyamba wa Ambuye, ŵelengani Luka 22:14, 19, 20. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:

  • Kodi Mgonelo wa Ambuye unacitika motani?

  • Kodi mkate na vinyo ziimila ciyani?—Onani mavesi 19 na 20.

Yesu anafuna kuti otsatila ake azikumbukila imfa yake kamodzi pa caka, pa tsiku limene iye anaphedwa. Motelo, a Mboni za Yehova amasonkhana pamodzi caka ciliconse kuti akumbukile imfa ya Yesu m’njila imene iye analamula. Kuti mudziŵe zambili za msonkhano wofunika umenewu, Tambani VIDIYO. Ndiyeno kambilanani funso lotsatila.

  • Kodi n’ciyani cimacitika pa Cikumbutso?

Mkate na vinyo ni zophiphilitsa cabe. Mkate umaimila thupi la Yesu langwilo limene anapeleka kaamba ka ife. Vinyo amaimila magazi ake

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Ine n’namulandila kale Yesu monga mpulumutsi wanga, conco sinifunikilanso kucita ciliconse.”

  • Kodi mungaseŵenzetse bwanji Yohane 3:16 na Yakobo 2:17, poonetsa kuti palinso zina zofunikila kucita?

CIDULE CAKE

Timayamikila zimene Yesu anaticitila poonetsa cikhulupililo mwa iye, komanso kupezeka pa Cikumbutso ca imfa yake.

Mafunso Obweleza

  • Kodi kuonetsa cikhulupililo mwa Yesu kumatanthauza ciyani?

  • Kodi mungayamikile bwanji zimene Yehova na Yesu anakucitilani?

  • N’cifukwa ciyani ni cinthu cofunika kwambili kupezeka pa Cikumbutso ca imfa ya Khristu?

Colinga

FUFUZANI

Kodi imfa ya Khristu imatilimbikitsa kucita ciyani?

Anagwiritsa Ntchito Thupi Lake Polemekeza Yehova (9:28)

Dziŵani zambili zokhudza cikhulupililo na mmene tingacionetsele.

“Khalani na Cikhulupililo m’Malonjezo a Yehova” (Nsanja ya Mlonda, October 2016)

Mu nkhani yakuti “Nikuona Kuti Ndine Woyela Komanso Nili na Moyo Waphindu,” onani mmene mayi wina anapindulila pa umoyo wake atamvetsetsa za nsembe ya Khristu.

“Baibo Imasintha Anthu” (Nsanja ya Mlonda, August 1, 2011)

Onani cifukwa cake ni anthu ocepa cabe amene amadyako kapena kumwako ziphiphilitso pa Cikumbutso.

“N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Mumachita Mwambo wa Mgonero wa Ambuye Mosiyana ndi Zipembedzo Zina?” (Nkhani ya pawebusaiti)