Zimene muyenela kucita kuti mupindule kwambili na maphunzilo a Baibo amenewa
Pezani wokuphunzitsani: Pemphani munthu amene anakupatsani kabuku kano kuti muziphunzila naye Baibo, kapena tumizani pempho lanu pa webusaiti yathu ya jw.org.
GAWO LOYAMBA
Ŵelengani ndime iliyonse, pamodzi na mafunso ali m’zilembo zacikasu (A) komanso malemba (B) otsindika mfundo zazikulu. Malemba ena ni olemba kuti “ŵelengani.”
GAWO LAPAKATI
Ciganizo coyamba (C) pansi pa kamutu kakuti Kumbani Mozamilapo cifotokoza zimene mudzakambilana. Tumitu tung’ono-tung’ono (D) tuonetsa mfundo zazikulu zokambilana. Ŵelengani malembawo, yankhani mafunso, ndipo tambani mavidiyo (E).
Onani zinthuzi na tumawu twake (F), ndiponso ganizilani mmene mungayankhile pambali yakuti Anthu Ena Amakamba Kuti (G).
GAWO LOTHELA
Cidule Cake na Mafunso Obweleza (H) ndizo mbali zomaliza phunzilo. Lembani deti imene mwatsiliza phunzilo. Pa mbali yakuti Zocita (I) pali zimene muyenela kucita. Ndipo pa mbali yakuti Fufuzani (J) pali zimene mungasankhe kuŵelenga kapena kutamba.
Mopezela mavesi m’Baibo
Malemba alembedwa motele; buku la m’Baibo (A), caputala (B), komanso vesi kapena mavesi (C). Mwacitsanzo, Yohane 17:3 itanthauza buku la Yohane, caputala 17, vesi 3.