Nkhani 65
Ufumu Ugaŵanika
KODI udziŵa cifukwa cake munthu uyu ang’amba-ng’amba mkanjo wake? Yehova ndiye anamuuza kucita zimenezi. Munthu ameneyu ni mneneli wa Mulungu, Ahiya. Kodi umudziŵa mneneli? Mneneli ni munthu amene Mulungu amamuuza zinthu zimene zidzacitika mtsogolo.
Ahiya apa akamba ndi Yeroboamu. Yeroboamu ni munthu amene anaikidwa ndi Solomo kuti aziyang’anila nchito yake ya cimango. Pamene Ahiya akumana ndi Yeroboamu panjila monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa, Ahiya acita cinthu codabwitsa. Iye avula mkanjo wake watsopano ndi kuung’amba-ng’amba mu zidutswa 12. Kenako auza Yeroboamu kuti: ‘Tengapo zidutswa 10.’ Kodi udziŵa cifukwa cake Ahiya apatsa Yeroboamu zidutswa 10?
Ahiya afotokoza kuti Yehova adzalanda Solomo ufumu. Akamba kuti, Yehova adzapatsa Yeroboamu mafuko 10. Zimenezi zitanthauza kuti mwana wa Solomo, Rehoboamu adzalamulila mafuko aŵili cabe.
Pamene Solomo akumva zimene Ahiya anauza Yeroboamu, akalipa kwambili, cakuti afuna kupha Yeroboamu. Koma Yeroboamu athaŵila ku Iguputo. Patapita nthawi Solomo anafa. Iye anali mfumu kwa zaka 40, koma tsopano mwana wake Rehoboamu ndiye akhala mfumu. Pamene Yeroboamu ali ku Iguputo, amvela kuti Solomo wamwalila, conco abwelela ku Isiraeli.
Rehoboamu si mfumu yabwino. Iye amacita nkhanza kwambili kwa anthu kupambana ngakhale Solomo atate wake. Yeroboamu ndi anthu ena audindo apita kwa Rehoboamu kukam’pempha kuti azikhala wokoma mtima kwa anthu. Koma Rehoboamu sawamvela, ndipo ayamba kuwacitila nkhanza kwambili kuposa poyamba. Conco anthu aika Yeroboamu kukhala mfumu ya mafuko 10, koma fuko la Benjamini ndi la Yuda likhalabe ndi Rehoboamu monga mfumu yao.
Yeroboamu safuna kuti anthu ake aziyenda ku Yerusalemu kukalambila pa kacisi wa Yehova. Conco apanga ana ang’ombe aŵili kuti anthu a ufumu wa mafuko 10 aziwalambila. Posapita nthawi, dziko lonse lidzala ndi upandu ndi ciwawa.
Mu ufumu wa mafuko aŵili mulinso mavuto. Pasanapite zaka zisanu kucokela pamene Rehoboamu akhala mfumu, mfumu ya ku Iguputo inabwela kudzamenya nkhondo ndi Yerusalemu. Mfumuyi itenga zinthu zambili zamtengo wapatali mu kacisi wa Yehova. Conco, ulemelelo umene kacisi wa Yehova anali nao pamene anamangidwa sunakhale kwanthawi yaitali.
1 Mafumu 11:26-43; 12:1-33; 14:21-31.