Wolembedwa na Mateyo 21:1-46
21 Iwo atayandikila ku Yerusalemu, anafika ku Betefage pa Phili la Maolivi. Kenako Yesu anatuma ophunzila ake aŵili
2 n’kuwauza kuti: “Pitani m’mudzi uwo, ndipo mukakangoloŵamo, mukapeza bulu atam’mangilila pamodzi na mwana wake wamphongo. Mukawamasule, n’kuwabweletsa kwa ine.
3 Munthu aliyense akakakufunsani ciliconse, mukanene kuti, ‘Ambuye akuwafuna.’ Ndipo nthawi yomweyo akawatumiza.”
4 Zimenezi zinacitikadi kuti mawu amene ananenedwa kudzela mwa mneneli akwanilitsidwe, akuti:
5 “Uza mwana wamkazi wa Ziyoni kuti: ‘Taona! Mfumu yako ikubwela kwa iwe. Ni yofatsa, ndipo yakwela pa bulu, inde, mwana wamphongo wa bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.’”
6 Conco ophunzilawo anapita, ndipo anacita ndendende zimene Yesu anawauza.
7 Anabwela naye buluyo pamodzi na mwana wake. Kenako anayanzika zovala zawo pa abuluwo, ndipo Yesu anakwelapo.
8 Anthu ambili m’khamulo anayanzika zovala zawo zakunja mu msewu, ndipo ena anali kudula nthambi za mitengo n’kuziyala mu msewu.
9 Komanso khamu la anthu limene linali patsogolo na pambuyo pake linali kufuula kuti: “M’pulumutseni Mwana wa Davide! Wodalitsika ni iye wobwela m’dzina la Yehova! M’pulumutseni inu amene muli kumwambamwambako!”
10 Ndiyeno ataloŵa mu Yerusalemu, mumzinda wonsewo munakhala ciphokoso. Ena anali kufunsa kuti: “Ndani ameneyu?”
11 Khamulo linali kuyankha kuti: “Ameneyu ni mneneli Yesu, wocokela ku Nazareti, ku Galileya!”
12 Yesu analoŵa m’kacisi na kupitikitsila panja onse omwe anali kugulitsa na kugula zinthu m’kacisimo. Komanso anagudubula matebulo a osintha ndalama na mabenchi a ogulitsa nkhunda.
13 Ndipo anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphelelamo,’ koma inu mukuisandutsa phanga la acifwamba.”
14 Komanso anthu akhungu na olemala anabwela kwa iye m’kacisimo, ndipo anawacilitsa.
15 Ansembe aakulu na alembi ataona zinthu zodabwitsa zimene iye anacita, ndiponso ataona anyamata amene anali kufuula kuti, “M’pulumutseni Mwana wa Davide!” anakwiya kwambili,
16 ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ukumva zimene awa akukamba?” Yesu anawayankha kuti: “Inde. Kodi simunaŵelengepo mawu akuti, ‘Mwacititsa pakamwa pa ana na makanda kulankhula mawu acitamando?”
17 Ndiyeno anawasiya n’kutuluka mu mzindawo kupita ku Betaniya, ndipo anagona kumeneko.
18 Akubwelela ku mzinda wa Yerusalemu m’mamaŵa, anamva njala.
19 Ataona mtengo wa mkuyu m’mbali mwa msewu, anapita komweko, koma sanapezemo ciliconse. Anangopezamo masamba okha-okha. Conco anauza mtengowo kuti: “Kuyambila lelo sudzabalanso zipatso.” Ndipo mtengo wa mkuyuwo unafota nthawi yomweyo.
20 Ophunzilawo ataona zimenezi anadabwa kwambili, ndipo anati: “Zatheka bwanji kuti mtengo wa mkuyuwu ufote nthawi yomweyi?”
21 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Ndithu nikukuuzani kuti, ngati muli na cikhulupililo ndipo simukayika, mudzatha kucita zimene nacita ku mtengo wa mkuyuwu. Ndiponso kuposa pamenepa mudzatha kuuza phili ili kuti, ‘Nyamuka, ukadziponye m’nyanja,’ ndipo zidzacikadi.
22 Zilizonse zimene mudzapempha m’mapemphelo anu, mudzalandila ngati muli na cikhulupililo.”
23 Yesu ataloŵa m’kacisi, ansembe aakulu na akulu anabwela kwa iye pamene anali kuphunzitsa n’kumufunsa kuti: “Kodi ulamulilo wocita zimenezi munautenga kuti? Nanga ndani anakupatsani ulamulilo umenewu?”
24 Yesu anawayankha kuti: “Inenso nikufunsani cinthu cimodzi. Mukaniyankha, inenso nikuuzani kumene n’natenga ulamulilo wocita zimenezi:
25 Kodi ubatizo wa Yohane unacokela kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?” Koma iwo anayamba kukambilana, n’kumati: “Tikanena kuti, ‘Unacokela kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga n’cifukwa ciyani simunamukhulupilile?’
26 Komanso sitingakambe kuti, ‘Unacokela kwa anthu,’ cifukwa tikuopa khamu la anthuli popeza onse amakhulupilila kuti Yohane anali mneneli.”
27 Conco pomuyankha Yesu, iwo anati: “Sitidziŵa.” Yesu anati: “Inenso sinikuuzani kumene n’natenga ulamulilo wocita zimenezi.
28 “Muganiza bwanji? Munthu wina anali na ana aŵili. Ndipo anapita kwa mwana woyamba n’kumuuza kuti, ‘Mwanawe, lelo upite kukagwila nchito m’munda wa mpesa.’
29 Poyankha iye anati, ‘Sinipita,’ koma pambuyo pake anamva cisoni ndipo anapita.
30 Anapita kwa waciŵili n’kumuuzanso cimodzimodzi. Iye poyankha anati, ‘Nipita atate,’ koma sanapite.
31 Pa ana aŵiliwa, ndani anacita cifunilo ca atate ake?” Iwo anati: “Woyamba uja.” Ndiyeno Yesu anati: “Ndithu nikukuuzani kuti okhometsa misonkho na mahule akukusiyani m’mbuyo n’kukaloŵa mu Ufumu wa Mulungu.
32 Pakuti Yohane anabwela kwa inu n’kukuonetsani njila ya cilungamo, koma simunam’khulupilile. Komabe, okhometsa misonkho na mahule anam’khulupilila. Koma ngakhale kuti inu munaona zimenezi, simunamve cisoni pambuyo pake n’kusintha maganizo anu kuti mum’khulupilile.
33 “Mvelani fanizo lina: Panali munthu wina amene anali na munda. M’mundawo analimamo mphesa n’kumanga mpanda kuzungulila mundawo, komanso anakumbamo copondelamo mphesa na kumanga nsanja. Kenako anausiya m’manja mwa alimi n’kupita ku dziko lina.
34 Nyengo yokolola zipatso itafika, iye anatuma akapolo ake kwa alimi aja kuti akatengeko zipatso zake.
35 Koma alimiwo anagwila akapolo aja. Mmodzi anamumenya, wina anamupha, ndipo wina anamuponya miyala.
36 Anatumanso akapolo ena ambili kuposa gulu loyamba lija. Koma amenewanso anawacita cimodzimodzi.
37 Pamapeto pake anatuma mwana wake kwa iwo, n’kunena kuti, ‘Mwana wangayu akamulemekeza.’
38 Alimiwo ataona mwanayo anayamba kukambilana kuti, ‘Eya! Uyu ndiye wolandila coloŵa. Bwelani, tiyeni timuphe na kutenga coloŵa cake!’
39 Conco anamugwila na kumuponya kunja kwa munda wa mpesawo n’kumupha.
40 Ndiye kodi mwinimunda wa mpesa uja akadzabwela, adzacita nawo ciyani alimiwo?”
41 Iwo anayankha kuti: “Cifukwa cakuti ni oipa, adzawawononga koopsa ndipo adzapeleka munda wa mpesawo kwa alimi ena, amene angamupatse zipatso nthawi yokolola ikakwana.”
42 Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Kodi simunaŵelenge m’Malemba kuti, ‘Mwala umene omanga anaukana, wakhala mwala wapakona wofunika kwambili.* Umenewu wacokela kwa Yehova, ndipo ni wodabwitsa m’maso mwathu?
43 Ndiye cifukwa cake nikukuuzani kuti, Ufumu wa Mulungu udzacotsedwa kwa inu na kupelekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.
44 Komanso munthu wogwela pa mwala umenewu adzaphwanyika. Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwele, udzamupelelatu.”
45 Ansembe aakulu na Afalisi atamva mafanizo akewa, anadziŵa kuti anali kukamba za iwo.
46 Ngakhale kuti iwo anali kufuna kumugwila* anaopa khamu la anthu, cifukwa anthuwo anali kumuona kuti ni mneneli.
Mawu a m'Munsi
^ Mwala umenewu anali kuuika pa kona ya nyumba, pomwe zipupa ziŵili zimakumana.
^ Kapena kuti, “kumumanga.”