Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Vesi la M’Baibulo la Tsiku Lililonse

Vesi la M’Baibulo la Tsiku Lililonse

Kabuku kakuti Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku kali ndi vesi la m’Baibulo la tsiku lililonse komanso ndemanga zofotokoza vesilo. Kabukuka kangakuthandizeni kuti muziyamba tsiku lililonse poganizira mfundo zolimbikitsa zochokera mu nkhani za m’Baibulo.

Mukhoza kuwerenga lemba la tsiku ndi ndemanga zake nthawi ina iliyonse, koma ambiri amaona kuti kuziwerenga m’mawa ndi kothandiza kwambiri. Akatero amathakuganizira zomwe aphunzirazo tsiku lonse. Ngati muli pa banja, zingakhalenso zothandiza kukambirana lemba la tsiku limodzi ndi banja lanu.

Mungawerenge lemba la tsiku pa LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower kapena mungapange dawunilodi PDF ya kabuku konse kokhala ndi mavesi a chaka chonse.