KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?
Luso la Gulugufe Woyera Lotha Kuimitsa Mapiko Ake Ngati V
Gulugufe akafuna kuuluka amadalira dzuwa kuti minofu yake yomuthandiza kuuluka itenthe. Koma kukakhala mitambo gulugufe woyera ndi amene minofu yake imatentha mofulumira moti amayamba kuuluka mwamsanga kuposa agulugufe ena. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?
Taganizirani izi: Mitundu yambiri ya agulugufe isanayambe kuuluka imayamba yawothera kaye dzuwa mapiko ake ali otseka kapena otambasula. Koma gulugufe woyerayu akamaothera dzuwa, amaimitsa mapiko ake ngati chilembo cha V. Kafukufuku akusonyeza kuti gulugufeyu amaimika mapiko ake ngati V n’cholinga choti mphamvu ya dzuwa izitha kumufikira bwinobwino. Zimenezi zimathandiza kuti mphamvu ya kutentha kwa dzuwa izifika mosavuta m’minofu youlukira, yomwe imakhala pamimba ndi pamtima pake, popanda kutchingidwa ndi mapiko ndipo kutenthako kukangokwanira gulugufeyo amayamba kuuluka.
Akatswiri a kuyunivesite ya Exeter ku England, anachita kafukufuku kuti aone ngati angathe kupanga mapanelo a sola amphamvu okhala ngati V potengera mapiko a gulugufeyu. Atachita zimenezi, anapeza kuti mphamvu za magetsi zimene mapanelowo amatulutsa zinawonjezeka ndi maperesenti pafupifupi 50.
Akatswiriwo anapezanso kuti kunja kwa mapiko a gulugufeyu kumakhala kowala kwambiri. Potengera mmene mapiko a gulugufeyu amaimira komanso kuwala kwake, ochita kafukufukuwa anapanga mapanelo a sola opepuka koma amphamvu kwambiri. Pulofesa Richard ffrench-Constant, yemwe anagwira nawo ntchito yofufuzayi, ataona zimenezi ananena kuti gulugufeyu “ndi katswiri pokolola mphamvu ya dzuwa.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti gulugufeyu azitha kuimitsa mapiko ake ngati V? Kapena pali winawake amene anamupanga ndi luso limeneli?