Kodi Baibulo Limaphunzitsa Zotani Zokhudza Mariya Virigo?
Yankho la m’Baibulo
Baibulo limanena kuti Mariya adakali namwali, anapatsidwa mwayi wobereka Yesu. Baibulo linali litaneneratu za chozizwitsa chimenechi m’buku la Yesaya. Mabuku a Uthenga Wabwino a Mateyu ndi Luka amafotokoza mmene ulosi umenewo unakwaniritsidwira.
Polosera mmene zidzakhalire kuti Mesiya aonekere padzikoli, Yesaya analemba kuti: “Tamverani mtsikana adzatenga pakati ndipo adzabereka mwana wamwamuna.” (Yesaya 7:14) Mothandizidwa ndi mzimu woyera, Mateyu anafotokoza kuti ulosi wa Yesaya unkanena za Mariya amene anali ndi pakati pa Yesu. Mateyu atafotokoza kuti Mariya anali ndi pakati mothandizidwa ndi mzimu woyera, ananenanso kuti: “Zonsezi zinachitika kuti zimene Yehova ananena kudzera mwa mneneri wake zikwaniritsidwe. Iye anati: “Tamverani namwali a adzatenga pakati ndipo adzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli,” lotanthauza “Mulungu Ali Nafe,” likamasuliridwa.”—Mateyu 1:22, 23.
Luka amene nayenso analemba nawo uthenga wabwino, analembanso za pakati pozizwitsa pomwe Mariya anali napo. Iye analemba kuti Mulungu anatumiza mngelo Gabirieli “kwa namwali amene mwamuna wina wotchedwa Yosefe, wa m’nyumba ya Davide, anamulonjeza kuti adzamukwatira. Namwali ameneyu dzina lake anali Mariya.” (Luka 1:26, 27) Mariya mwiniwakeyo anatsimikiza zoti analidi namwali. Iye atauzidwa kuti adzakhala mayi wa Mesiya, anafunsa kuti: “Zimenezi zidzatheka bwanji, pakuti sindinagonepo ndi mwamuna?”—Luka 1:34.
Kodi zinatheka bwanji kuti munthu amene anali asanagonepo ndi mwamuna akhale ndi mwana?
Mariya anakhala ndi pakati mothandizidwa ndi mzimu woyera womwe ndi mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito. (Mateyu 1:18) Mariya anauzidwa kuti: “Mzimu woyera udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.” b (Luka 1:35) Choncho mozizwitsa, Mariya anakhala ndi pakati chifukwa Mulungu anasamutsa moyo wa Yesu n’kuuika m’mimba mwa Mariyayo.
N’chifukwa chiyani Mulungu anasankha zoti Yesu abadwe kwa namwali?
Mulungu anakonza zoti Yesu adzabadwe mwa namwali n’cholinga choti adzabadwe ndi thupi langwiro kuti adzathe kupulumutsa anthu ku uchimo ndi imfa. (Yohane 3:16; Aheberi 10:5) Mulungu anasamutsira moyo wa Yesu m’mimba mwa Mariya. N’zodziwikiratu kuti mzimu woyera wa Mulungu unateteza mwana amene anali m’mimbayo kuti asatengere uchimo wa mayi ake.—Luka 1:35.
Choncho Yesu anabadwa wangwiro ngati mmene analili Adamu asanachimwe. Baibulo limanena kuti Yesu “sanachite tchimo.” (1 Petulo 2:22) Chifukwa chakuti Yesu anabadwa wangwiro, zinali zotheka kuti apereke moyo wake ngati dipo kuti apulumutse anthu ku uchimo ndi imfa.—1 Akorinto 15:21, 22; 1 Timoteyo 2:5, 6.
Kodi Mariya anakhalabe namwali atabereka Yesu?
Baibulo silinena kuti Mariya anakhalabe namwali kwa moyo wake wonse. Koma limasonyeza kuti patapita nthawi anakhalanso ndi ana ena.—Mateyu 12:46; Maliko 6:3; Luka 2:7; Yohane 7:5.
Kodi Mariya analibe tchimo lililonse?
Ayi. Komabe buku lina pofotokoza za chiphunzitso choti Mariya anali munthu wopanda tchimo lililonse, linanena kuti: ‘Ngakhale kuti anthu onse anabadwa ndi uchimo. . . Mariya sanatengere uchimo wa Adamu ngakhale kungoyambira pomwe anabadwa. MWACHISOMO, iye anatetezedwa mwapadera kuti kuti asadzatengere uchimo wa Adamu.’—New Catholic Encyclopedia. c
Koma mosiyana ndi zimene bukuli linanena, palibe paliponse m’Baibulo pomwe pamanena kuti Mariya sanatengere uchimo wa Adamu. (Salimo 51:5; Aroma 5:12) Ndipotu Mariya mwiniwakeyo anapereka umboni wosonyeza kuti anali ndi uchimo. Atangokhala ndi mwana, anakapereka nsembe yochotsa machimo mogwirizana ndi zimene Chilamulo cha Mose chinkanena. (Levitiko 12:2-8; Luka 2:21-24) Buku lina linanena kuti: “Ndi zoona kuti Malemba safotokoza mwachindunji kuti Mariya sanabadwe ndi uchimo. . . Chimenechi ndi chiphunzitso cha Tchalitchi.”—New Catholic Encyclopedia.
Kodi ndi bwino kupereka ulemu wapadera kwa Mariya?
Mariya anasonyeza kuti anali, wodzichepetsa, womvera, komanso anali ndi chikhulupiriro ndipo ankakonda Mulungu. Iye ndi m’modzi wa anthu okhulupirika omwe tingawatsanzire.—Aheberi 6:12.
Ngakhale kuti Mariya anapatsidwa mwayi wokhala mayi wa Yesu, Baibulo silitiphunzitsa kuti tizimulambira kapenanso kupemphera kwa iye. Yesu sananenepo kuti mayi ake azipatsidwa ulemu wapadera ndipo sanaphunzitsepo ophunzira ake kuti azichita zimenezo. Kuwonjezera pamenepo, Mariya satchulidwa m’mabuku ena a Malemba a Chigiriki kupatulako m’mabuku a Uthenga Wabwino komanso pavesi limodzi lokha m’buku la Machitidwe.—Machitidwe 1:14.
Malemba sasonyeza kuti Mariya ankapatsidwa ulemu wapadera ngakhale ndi Akhristu oyambirira. Koma amaphunzitsa Akhristu kuti azilambira Mulungu yekha.—Mateyu 4:10.
a Mawu a Chiheberi akuti ʽal·mahʹ omwe anawamasulira kuti “namwali” mu ulosi wa Yesaya, akhoza kunena za mtsikana wamng’ono amene sanagonepo ndi mwamuna kapena za mzimayi wachitsikana. Koma mothandizidwa ndi mzimu woyera, Mateyu anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti par·theʹnos omwe amatanthauza mtsikana amene sanagonepo ndi mwamuna.
b Ena amapewa kutchula Yesu kuti “Mwana wa Mulungu” chifukwa amati mawuwa amasonyeza ngati kuti Mulungu anagonana ndi munthu wamkazi. Komatu zimenezo si zimene Malemba amatanthauza. Baibulo limanena kuti Yesu ndi “Mwana wa Mulungu” komanso “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse” chifukwa ndiye woyambirira kulengedwa. Komanso limamutchula choncho chifukwa chakuti Mulunguyo, anamulenga yekha mwachindunji. (Akolose 1:13-15) Komansotu Baibulo limanena kuti Adamu anali “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Izi zili choncho chifukwa Adamu nayenso anachita kulengedwa ndi Mulungu.
c Buku Lachiwiri, Volume 7, tsamba 331.