Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Kukhala Munthu Wauzimu N’kutani? Kodi Ndingakhale Munthu Wauzimu Popanda Kukhala M’chipembedzo Chilichonse?

Kodi Kukhala Munthu Wauzimu N’kutani? Kodi Ndingakhale Munthu Wauzimu Popanda Kukhala M’chipembedzo Chilichonse?

Yankho la m’Baibulo

 Mogwirizana ndi Baibulo, munthu wauzimu amafunitsitsa kusangalatsa Mulungu komanso kuphunzira kuti aziyendera maganizo a Mulungu. Iye amayesetsa kutsatira mfundo za Mulungu komanso kutsogoleredwa ndi mzimu wake woyera. aAroma 8:5.

 Pofuna kutithandiza kusiyanitsa munthu wauzimu ndi munthu amene si wauzimu, nthawi zambiri Baibulo limafotokoza zimene munthu amene si wauzimu amachita. Mwachitsanzo, mosiyana ndi munthu wauzimu, “munthu wokonda zinthu za m’dziko salandira zinthu za mzimu wa Mulungu,” kapena kuti zimene Mulungu amaphunzitsa. (1 Akorinto 2:14-16) Komanso mosiyana ndi anthu auzimu, anthu oganiza ngati anthu a m’dzikoli amakonda ‘kuchitirana nsanje ndi kukangana okhaokha,’ m’malo mokhala opatsa ndi amtendere. (1 Akorinto 3:1-3) Baibulo limanenanso kuti anthu amene amanenera anzawo zoipa komanso kugawanitsa anthu “amachita zauchinyama, ndipo alibe mzimu wa Mulungu.”—Yuda 19; Miyambo 16:28. b

Zimene zili munkhaniyi

 Kodi tingakwanitse bwanji kukhala anthu auzimu?

 Timatha kukhala anthu auzimu chifukwa choti tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Genesis 1:27) N’chifukwa chake anthu ambiri amafuna kudziwa za zinthu zomwe sitingazione ndi maso.

 Mwachibadwa, timathanso kukhala ndi makhalidwe ofanana ndi a Yehova c Mulungu, monga mtendere, chifundo komanso kupanda tsankho. (Yakobo 3:17) Mulungu amaperekanso mzimu wake kwa anthu amene amayesetsa kutsatira malamulo ake.—Machitidwe 5:32.

 Kodi kukhala munthu wauzimu ndi kofunika bwanji?

 Munthu wauzimu amapeza “moyo ndi mtendere.” (Aroma 8:6) Mphatso zimene Mulungu amaperekazi ndi zamtengo wapatali kwambiri.

  •   Moyo: Mulungu amalonjeza kuti adzapereka moyo wosatha kwa anthu auzimu.—Yohane 17:3; Agalatiya 6:8.

  •   Mtendere: Munthu wauzimu amakhala pa mtendere ndi Mulungu. Koma anthu amene amangoganizira zofuna za thupi lawo amakhala pa udani ndi Mulungu. (Aroma 8:7) Mulungu amapatsanso anthu auzimu “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afilipi 4:6, 7) Mtendere wamumtima umenewu umawathandiza kukhala osangalala.—Mateyu 5:3.

 Kodi ndingakhale bwanji munthu wauzimu?

  •   Muziphunzira malamulo a Mulungu ndi kuwatsatira. Mungachite zimenezi powerenga Baibulo chifukwa muli maganizo a Mulungu amene analembedwa ndi anthu omwe ‘anatsogoleredwa ndi mzimu woyera.’ (2 Petulo 1:21) Zimene mungaphunzire m’Baibulo zingakuthandizeni kulambira Mulungu “ndi mzimu ndi choonadi,” kapena kuti motsogoleredwa ndi mzimu woyera komanso mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna.—Yohane 4:24.

  •   Muzipempha Mulungu kuti azikuthandizani. (Luka 11:13) Mulungu adzakuthandizani kukhala ndi makhalidwe amene angakuthandizeni kukhala munthu wauzimu. (Agalatiya 5:22, 23) Adzakupatsaninso nzeru zokuthandizani kuthana ndi mavuto amene mungakumane nawo.—Yakobo 1:5.

  •   Muzigwirizana ndi anthu auzimu. Iwo adzakulimbikitsani kukhalanso munthu wauzimu. (Aroma 1:11, 12) Koma mosiyana ndi zimenezi, kugwirizana ndi anthu amene maganizo awo amasiyana ndi a Mulungu, kungakuchititseni kusiya kukhala munthu wauzimu.—Yakobo 4:4.

 Kodi ndimafunika kukhala m’chipembedzo chinachake kuti ndikhale wauzimu?

 Kungokhala m’chipembedzo sikumachititsa munthu kukhala wauzimu. Baibulo limati: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulira lilime lake, ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.”—Yakobo 1:26.

 Ngakhale zili choncho, Baibulo limasonyeza kuti anthu auzimu amalambira Mulungu m’njira imene iye amaivomereza. Iwo amavomereza kuti pali “mzimu umodzi,” womwe ndi mzimu woyera wa Mulungu. Mzimuwu umawalimbikitsa kulambira Mulungu monga “thupi limodzi,” kapena kuti gulu logwirizana lomwe ‘limasunga umodzi pokhala mwamtendere.’.—Aefeso 4:1-4.

 Maganizo olakwika okhudza munthu wauzimu

 Maganizo olakwika: Munthu wauzimu amachita chilichonse chimene chimamuthandiza kukhala wosangalala kapena chimene chimamuchititsa kumva kuti ndi munthu wabwino.

 Zoona zake: Baibulo limasonyeza kuti kukhala munthu wauzimu, ndi kukhala mogwirizana ndi maganizo a Mulungu. Kukhala munthu wauzimu sikulimbikitsa maganizo oyesetsa kukhala munthu wabwino pawekha popanda kudalira Mulungu. Anthu auzimu amakhala osangalala chifukwa chozindikira kuti Yehova ndi Mlengi wawo ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake.—Salimo 100:3.

 Maganizo olakwika: Munthu angakhale wauzimu akamadzimana zinthu kwambiri komanso akamadzizunza.

 Zoona zake: Kudzizunza thupi, ndi “kulambira kochita kudzipangira” ndipo kumachokera m’maganizo ochimwa. (Akolose 2:18, 23) Baibulo limasonyeza kuti munthu wauzimu amakhala moyo wosangalala osati wodzizunza.—Miyambo 10:22.

 Maganizo olakwika: Kuchita zinthu zokhudza kukhulupirira mizimu, kumalimbikitsa munthu kukhala wauzimu.

 Zoona zake: Mtundu wina wa kukhulupirira mizimu ndi kukhulupirira kuti mizimu ya anthu akufa ingalankhule ndi anthu amoyo. Koma Baibulo limaphunzitsa kuti anthu akufa sadziwa chilichonse. (Mlaliki 9:5) Zoona ndi zakuti, anthu okhulupirira mizimu amakhala akulankhula ndi mizimu yoipa imene Mulungu amadana nayo. Mulungu amadana ndi anthu amene amakhulupirira mizimu ndipo munthu wochita zimenezi sangakhale munthu wauzimu.—Levitiko 20:6; Deuteronomo 18:11, 12.

 Maganizo olakwika: Mwachibadwa, zamoyo zonse zimakhala zauzimu.

 Zoona zake: Zonse zimene Mulungu analenga zimamupatsa ulemerero. (Salimo 145:10; Aroma 1:20) Koma ndi angelo ndi anthu okha omwe angakhale auzimu. Mosiyana ndi zimenezi, zinyama zimangochita zinthu mwachibadwa ndipo sizingakhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Zimangochita zinthu pofuna kukhutiritsa zimene matupi awo akufuna. (2 Petulo 2:12) N’chifukwa chake Baibulo limasiyanitsa kukhala wauzimu ndi kukhala ndi maganizo ndi zochita zauchinyama.—Yakobo 3:15; Yuda 19.

a Mawu a m’chilankhulo choyambirira chimene Baibulo linalembedwa omwe amamasuliridwa kuti “mzimu,” kwenikweni amatanthauza “mpweya” womwe timapuma. Koma angatanthauzenso chinthu chosaoneka koma chokhala ndi mphamvu yogwira ntchito. Baibulo limafotokoza kuti Mulungu ndi Mzimu Wapamwamba Kwambiri. Munthu wauzimu amasankha kutsogoleredwa ndi zimene Mulungu amafuna komanso mzimu wake woyera.

b Baibulo likamanena za anthu amene ‘amakonda zinthu zam’dziko’ kapena omwe ‘amaganiza ngati anthu am’dzikoli,’ limanena za anthu amene amangotsatira zimene matupi awo akufuna popanda kuganizira mfundo za Mulungu.

c Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.—Salimo 83:18.