Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yosamalira Makolo Achikulire?
Yankho la m’Baibulo
Ana akakula amakhala ndi udindo wosamalira makolo awo achikulire. Baibulo limanena kuti anawo amafunika “aphunzire kukhala odzipereka kwa Mulungu m’banja mwawo choyamba, mwa kubwezera kwa makolo . . . zowayenerera, pakuti zimenezi zimakondweretsa Mulungu.” (1 Timoteyo 5:4) Choncho ana akamayesetsa kusamalira makolo awo achikulire, amasonyeza kuti akumvera lamulo la m’Baibulo lakuti azilemekeza makolo awo.—Aefeso 6:2, 3.
Baibulo silipereka malangizo achindunji a zomwe muyenera kutsatira posamalira makolo achikulire. Koma limafotokoza zimene amuna ndi akazi ena anachita m’mbuyomo posamalira makolo awo. Ndipo lili ndi mfundo zomwe zingathandize anthu omwe akusamalira makolo achikulire.
Kodi atumiki ena akale ankasamalira bwanji makolo awo achikulire?
Panali njira zosiyanasiyana zosamalirira makolo achikulire potengera mmene zinthu zinalili. Mwachitsanzo:
Yosefe ankakhala kutali ndi kumene kunali bambo ake okalamba, a Yakobo. Zinthu zitayamba kumuyendera bwino, anakonza zoti bambo akewo abwere pafupi ndi komwe iyeyo ankakhala. Yosefe anawapatsa malo okhala, chakudya komanso ankawateteza.—Genesis 45:9-11; 47:11, 12.
Rute anachoka kwawo n’kupita kudziko la apongozi ake a akazi ndipo ankagwira ntchito mwakhama kuti aziwathandiza.—Rute 1:16; 2:2, 17, 18, 23.
Yesu atangotsala pang’ono kuphedwa, anasankhiratu munthu woti azidzasamalira mayi ake Mariya, yemwe ayenera kuti anali wamasiye.—Yohane 19:26, 27. a
Kodi ndi malangizo ati omwe Baibulo limapereka kwa anthu osamalira achikulire?
Baibulo lili ndi mfundo zomwe zingathandize anthu omwe akusamalira makolo achikulire kuti azithana ndi mavuto amene nthawi zina amakumana nawo powasamalira.
Muzilemekeza makolo.
Zimene Baibulo limanena: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.”—Ekisodo 20:12.
Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Muzilemekeza makolo anu powalola kuti azitha kudzisamalira okha mpaka pamene angathere. Ngati n’zotheka, muziwalola kusankha thandizo lomwe angafune. Mungasonyezenso kuti mumawalemekeza powapatsa thandizo lomwe mungakwanitse.
Muziwamvetsa komanso muziwakhululukira.
Zimene Baibulo limanena: “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.”—Miyambo 19:11.
Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Ngati makolo anu achikulire atalankhula mosakuganizirani kapena ngati sakusonyeza kuyamikira zomwe mumawachitira, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikanatani zikanakhala kuti ineyo ndiye wachikulireyo?’ Mukamvetsa mmene achikulire amachitira zinthu komanso mukamawakhululukira, mukhoza kupewa mavuto ambiri.
Muzipempha anthu ena kuti akuthandizeni.
Zimene Baibulo limanena: “Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima, koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.”—Miyambo 15:22.
Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Fufuzani zimene mungachite kuti muthandize makolo anu achikulire ngati amadwaladwala. Mungafufuze thandizo limene lilipo m’dera lanu lomwe mungawathandizire nalo. Muzifunsanso nzeru kwa anthu ena omwe anasamalirapo makolo achikulire. Ngati muli ndi achibale, mungakonze zoti mukambirane za thandizo lomwe makolo anu akufunikira, mmene mungawasamalire komanso zimene nonse mungachite pothandizana udindowo.
Muzidzichepetsa.
Zimene Baibulo limanena: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.”—Miyambo 11:2.
Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Muzidziwa malire anu. Mwachitsanzo, aliyense amakhala ndi malire akamagwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu. Malire ndi ofunikanso kuti muthe kudziwa zomwe mungakwanitsedi pothandiza makolo anu. Mukaona kuti mukupanikizika ndi udindowu, muzipempha achibale anu kapena anthu ena amene amasamaliranso achikulire kuti akuthandizeni.
Nanunso muzidzisamalira.
Zimene Baibulo limanena: “Palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.”—Aefeso 5:29.
Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Ngakhale kuti muli ndi udindo wosamalira makolo anu, nanunso muzidzisamalira. Ndipo ngati muli pabanja muzisamaliranso banja lanulo. Muzidya mokwanira. Muzipeza nthawi yopumula komanso muzigona mokwanira. (Mlaliki 4:6) Ngati n’zotheka musamadzipanikize mukamagwira ntchito. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzisangalala mukamasamalira makolo anu komanso kuti mukhale ndi thanzi labwino.
Kodi Baibulo limanena kuti makolo achikulire azisamaliridwa ali kuti?
Baibulo silimapereka malangizo achindunji okhudza malo amene ana angakasamalirireko makolo awo achikulire. Mabanja ena amasankha kuti azikhalabe ndi makolo awo achikulire. Nthawi zina amatha kuwapititsa kumalo omwe amasamalirako okalamba. Zikatere, achibale angakambirane zomwe aliyense angachite kuti azisamalira makolo achikulirewo.—Agalatiya 6:4, 5.
a Pa nkhaniyi, buku lina lofotokoza za Baibulo limanena kuti: “Zikuoneka kuti panali patapita nthawi kuchokera pamene Yosefe [mwamuna wake wa Mariya] anamwalira ndipo Yesu ndi amene ankasamalira Mariya. Koma popeza kuti Yesu anali atatsala pang’ono kuphedwa, n’kutheka kuti ankada nkhawa za amene adzasamalire mayi akewo. . . Apa Khristu anapereka chitsanzo chabwino kwa ana kuti azisamalira makolo awo achikulire.”—The NIV Matthew Henry Commentary in One Volume, pages 428-429.