N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera M’dzina la Yesu?
Yankho la m’Baibulo
Mulungu anakonza zoti ngati tikufuna kuti iye amve mapemphero athu, tizipemphera m’dzina la Yesu basi. Yesu anati: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Iye anauzanso atumwi ake okhulupirika kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Ngati mupempha chilichonse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.”—Yohane 16:23.
Zifukwa zina zopempherera m’dzina la Yesu
Timasonyeza kuti timalemekeza Yesu ndiponso Atate wake Yehova Mulungu.—Afilipi 2:9-11.
Timasonyeza kuti timayamikira Mulungu chifukwa chakuti anatumiza Yesu kudzatifera kuti tipulumutsidwe.—Mateyu 20:28; Machitidwe 4:12.
Timasonyeza kuti tikudziwa zoti Yesu ndi mkhalapakati wa ife ndi Mulungu.—Aheberi 7:25.
Timasonyeza kuti tikulemekeza udindo wa Yesu monga Mkulu wa Ansembe amene angatithandize kuti tikhalenso paubwenzi wabwino ndi Mulungu.—Aheberi 4:14-16.