Kodi Yesu Anakwatira? Kodi Anali ndi Abale Ake?
Yankho la m’Baibulo
Baibulo limasonyeza mooneka bwino kuti Yesu sanakwatire ngakhale kuti silitchula mwachindunji nkhani imeneyi. a Ganizirani mfundo izi:
Nthawi zambiri Baibulo limatchula za achibale ake a Yesu, azimayi amene ankayenda naye pa utumiki wake, komanso azimayi amene anaima pafupi ndi malo amene Yesuyo anapachikidwira. Koma Baibulo silitchulapo zoti Yesu anali ndi mkazi. (Mateyu 12:46, 47; Maliko 3:31, 32; 15:40; Luka 8:2, 3, 19, 20; Yohane 19:25) Chifukwa chomveka bwino chimene Baibulo silitchulira nkhaniyi n’chakuti iye sanakwatire.
Pofotokoza za anthu amene anasankha kusakwatira kuti atumikire Mulungu momasuka, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Amene angathe kuchita zimenezi [kusakwatira] achite.” (Mateyu 19:10-12) Popeza Yesu sanakwatire, anapereka chitsanzo kwa anthu amene asankha kusakwatira n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Mulungu.—Yohane 13:15; 1 Akorinto 7:32-38.
Yesu atatsala pang’ono kuti amwalire, anakonza zoti munthu wina azisamalira mayi ake. (Yohane 19:25-27) Iye akanakhala kuti anali ndi mkazi komanso ana, n’zosakayikitsa kuti akanaonetsetsa kuti nawonso azisamaliridwa.
Baibulo limauza amuna kuti azichita umutu wawo motsanzira Yesu, koma silisonyeza kuti Yesu anali ndi mkazi weniweni. M’malomwake, limafotokoza kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu monga mmene Khristu anakondera mpingo n’kudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” (Aefeso 5:25) Zikanakhala kuti Yesu anakwatira pa nthawi imene anali padziko lapansi, ndiye kuti vesili silikanatchula za mpingo koma likanatchula za mkazi wake.
Kodi Yesu anali ndi abale ake?
Inde, Yesu anali ndi abale ake osachepera 6. Ena mwa abale akewo anali Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi, komanso anali ndi azichemwali ake osachepera awiri. (Mateyu 13:54-56; Maliko 6:3) Abale akewa anali ana enieni a Mariya ndi Yosefe, omwe anali makolo ake a Yesu. (Mateyu 1:25) Baibulo limatchula Yesu kuti “mwana woyamba” wa Mariya, zimene zikusonyeza kuti Mariyayo analinso ndi ana ena.—Luka 2:7.
Maganizo olakwika amene anthu ena ali nawo okhudza abale ake a Yesu
Pofuna kulimbikitsa maganizo akuti Mariya anakhala namwali moyo wake wonse, anthu ena asintha tanthauzo la mawu akuti “abale.” Mwachitsanzo, anthu ena amanena kuti abale ake a Yesu anali ana a Yosefe amene anabereka ndi mkazi wake wina asanakwatire Mariya. Koma Baibulo limasonyeza kuti mwalamulo, Yesu ndi amene anali woyenerera kulowa ufumu umene unalonjezedwa kwa Davide. (2 Samueli 7:12, 13; Luka 1:32) Zikanakhala kuti Yosefe anali ndi ana akuluakulu kuposa Yesu, mosakayikira amenewa ndi amene akanakhala oyenerera mwalamulo kulowa ufumu.
Kodi mwina mawu akuti “abale” akutanthauza ophunzira a Yesu, kapena abale ake auzimu? Ayi, chifukwa zimenezo zikutsutsana ndi zomwe Baibulo limanena. Baibulo limanena kuti nthawi ina yake “abale akewo [a Yesu] sanali kumukhulupirira.” (Yohane 7:5) Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti pali kusiyana pakati pa abale a Yesu ndi ophunzira ake.—Yohane 2:12.
Enanso amanena kuti anthu amene amatchedwa abale ake a Yesu anali asuweni ake. Koma Malemba Achigiriki amagwiritsa ntchito mawu osiyana ponena za “m’bale” “wachibale” ndi “msuweni.” (Luka 21:16; Akolose 4:10) Akatswiri amaphunziro a Baibulo amavomereza kuti abale ake a Yesu analidi azichimwene komanso azichemwali ake enieni. Mwachitsanzo, buku lina limanena kuti: “Njira yosavuta yotithandiza kumvetsa mawu akuti ‘abale’ . . . ndiyakuti mawuwa amanena za ana amuna a Mariya ndi Yosefe. Choncho iwo anali abale ake a Yesu chifukwa nayenso Yesuyo mayi ake anali Mariya.” b—The Expositor’s Bible Commentary.
a Baibulo limatchula Khristu kuti mkwati, koma limasonyeza mosapita m’mbali kuti mawuwa ndi ophiphiritsa.—Yohane 3:28, 29; 2 Akorinto 11:2.
b Kuti mumvetse nkhaniyi, mukhozanso kuwerenga buku lakuti, The Gospel According to St. Mark, Second Edition, lolembedwa ndi Vincent Taylor, tsamba 249, ndiponso buku lakuti A Marginal Jew—Rethinking the Historical Jesus, lolembedwa ndi John P. Meier, Volume 1, tsamba 331 ndi 332.