Kodi Mawu Oti Puligatoliyo Amapezeka M’Baibulo?
Zimene Baibulo limanena
Ayi. M’Baibulo simupezeka mawu akuti “puligatoliyo,” ndipo siliphunzitsa kuti mizimu ya anthu amene amwalira imakayeretsedwa ku puligatoliyo. a Taonani zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza uchimo ndi imfa zomwe ndi zotsutsana ndi chiphunzitso cha puligatoliyo.
Kukhulupirira magazi a Yesu ndi kumene kumayeretsa munthu ku uchimo, osati kupita ku puligatoliyo. Baibulo limanena kuti “magazi a Yesu Mwana [wa Mulungu] akutiyeretsa ku uchimo wonse” komanso limati “Yesu Khristu . . . anatimasula ku machimo athu ndi magazi ake.” (1 Yohane 1:7; Chivumbulutso 1:5) Yesu anapereka “moyo wake dipo la anthu ambiri” kuti awawombole ku uchimo.—Mateyu 20:28, Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu.
Anthu amene amwalira sadziwa chilichonse. “Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Munthu amene wamwalira sangamve china chilichonse, choncho sizingatheke kuti ayeretsedwe ndi moto wa ku puligatoliyo.
Munthu samalangidwa chifukwa cha machimo pambuyo poti wamwalira. Baibulo limanena kuti “malipiro a uchimo ndi imfa” komanso limati “munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” (Aroma 6:7, 23) Choncho, imfa ndi chilango chokwanira cha uchimo.
a Ponena za puligatoliyo, buku lina linati, “m’Mauthenga Abwino mulibe mawu amenewa.” (Orpheus: A General History of Religions) Buku linanso limati: “Tinganene kuti chiphunzitso cha Chikatolika cha puligatoliyo ndi chochokera ku miyambo, osati Malemba Oyera.”—New Catholic Encyclopedia Buku Lachiwiri, Volume 11, tsamba 825.
b Onani buku lakuti New Catholic Encyclopedia, Second Edition, Volume 11, tsamba 824.