Kodi Ndizipemphera Bwanji?—Kodi Ndizigwiritsa Ntchito Pemphero la Ambuye?
Yankho la m’Baibulo
Pemphero la Ambuye, limatithandiza kudziwa mmene tingamapempherere komanso kudziwa nkhani zomwe tingamatchule popemphera. Yesu anauza ophunzira ake pempheroli, chifukwa anamupempha kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera.” (Luka 11:1) Komabe, Pemphero la Ambuye kapena kuti Pemphero la Atate Wathu, si pemphero lokhalo lomwe Mulungu amamva. a Yesu ananena pempheroli ngati chitsanzo cha mmene tingamapempherere kuti Mulungu azitimvetsera.
Zimene zili munkhaniyi
Kodi Pemphero la Ambuye limanena za chiyani?
Pemphero la Ambuye lomwe limapezeka pa Mateyu 6:9-13, limamveka mosiyanasiyana m’Mabaibulo ena. Mwachitsanzo, taonani zitsanzo ziwirizi.
Baibulo la Dziko Latsopano limati: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Mutikhululukire zolakwa zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira. Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.”
Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu limati: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu. Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” b
Kodi Pemphero la Ambuye limatanthauza chiyani?
Zimene Yesu anaphunzitsa zimagwirizana ndi mfundo za m’Malemba osiyanasiyana. Choncho kuona zomwe mavesi ena a m’Baibulo amanena, kungatithandize kumvetsa zomwe Pemphero la Ambuye limatanthauza.
“Atate wathu wakumwamba”
Ndi zoyenera kutchula Mulungu kuti “Atate wathu,” chifukwa iye ndi amene anatilenga komanso kutipatsa moyo.—Yesaya 64:8.
“Dzina lanu liyeretsedwe”
Dzina la Mulungu lakuti Yehova, liyenera kulemekezedwa komanso kuonedwa kuti ndi loyera kapena kuti lopatulika. Anthu tingathe kuthandiza kuyeretsa dzina la Mulungu tikamalankhula zokhudza makhalidwe ake komanso tikamauza anthu ena za cholinga chake.—Salimo 83:18; Yesaya 6:3.
“Ufumu wanu ubwere”
Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba ndipo Yesu ndiye Mfumu ya Ufumuwo. Yesu anatiuza kuti tizipempherera kuti boma limeneli lidzalamulire dziko lonse lapansi.—Danieli 2:44; Chivumbulutso 11:15.
“Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano”
Monga mmene zilili kuti kumwamba kulibe zinthu zoipa komanso imfa, chifuniro cha Mulungu chokhudza dziko lapansili n’chakuti anthu azikhalapo kwamuyaya komanso mwabata ndi mtendere.—Salimo 37:11, 29.
“Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero”
M’nthawi ya Yesu, anthu ankadya buledi ngati chakudya chawo cha tsiku ndi tsiku. Tizikumbukira kuti anthufe timadalira Mlengi wathu kuti atipatse zinthu zofunikira zomwe zingatithandize kukhala ndi moyo.—Machitidwe 17:24, 25.
“Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu”
Munkhaniyi mawu akuti “mangawa,” akutanthauza machimo. (Luka 11:4) Anthu tonse timachimwa ndipo timafunika kukhululukidwa. Koma kuti Mulungu atikhululukire, timafunikanso kukhala okonzeka kukhululukira anzathu pa zomwe amatilakwira.—Mateyu 6:14, 15.
“Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo”
Yehova Mulungu satiyesa kuti tichite zoipa. (Yakobo 1:13) Koma timayesedwa ndi “woipayo” amene ndi Satana Mdyerekezi amene amadziwikanso kuti “Woyesayo.” (1 Yohane 5:19; Mateyu 4:1-4) Choncho timapempha Yehova kuti asalole kuti tigonje tikamayesedwa kuti tichite zinthu zoipa.
Kodi ndiyenera kuloweza Pemphero la Ambuye zivute zitani kuti ndiziligwiritsa ntchito ndikafuna kupemphera?
Yesu anaphunzitsa Pemphero la Ambuye kuti likhale chitsanzo. Si kuti ankafuna kuti tiloweze mawu aliwonse a m’pempheroli. Asanaphunzitse za pempheroli, Yesu anali atachenjeza kuti: “Popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza.” (Mateyu 6:7) Nthawi ina akuphunzitsanso ophunzira ake pemphero lachitsanzo, anagwiritsa ntchito mawu osiyana ndi a m’pempheroli.—Luka 11:2-4.
Njira yabwino kwambiri popemphera, ndikulankhula zomwe zili mumtima mwathu.—Salimo 62:8.
Kodi tizipemphera bwanji?
Pemphero la Ambuye limatipatsa chitsanzo chabwino cha mmene tingapempherere kuti Mulungu amve pemphero lathu. Taonani zimene mavesi ena a m’Baibulo amanena pa nkhani imeneyi.
Muzipemphera kwa Mulungu yekha
Lemba: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.
Tanthauzo lake: Mapemphero athu ayenera kupita kwa Mulungu yekha, osati kwa Yesu, Mariya kapenanso kwa oyera mtima. Mawu oyambira a mu Pemphero la Ambuye akuti “Atate wathu,” amatiphunzitsa kuti tizipemphera kwa Yehova Mulungu yekha basi.
Mapemphero anu azikhala ogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu
Lemba: “Chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”—1 Yohane 5:14.
Tanthauzo lake: Tikhoza kupempherera chilichonse kapena nkhani iliyonse yogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Yesu anasonyeza kuti chifuniro cha Mulungu ndi chofunika kwambiri moti mpaka mu Pemphero la Ambuye ananena kuti: “Chifuniro chanu chichitike.” Tikamaphunzira Baibulo, timaphunzira za chifuniro kapena kuti cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansili.
Muzipempherera zinthu zomwe zikukukhudzani pa moyo wanu
Lemba: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.”—Salimo 55:22.
Tanthauzo lake: Mulungu amakhudzidwa ndi mmene zinthu zikuyendera pa moyo wathu. Monga mmene Yesu anatchulira zinthu zina zomwe timafunikira pa moyo mu Pemphero la Ambuye, tikhozanso kupempha Mulungu kuti atithandize kupeza zinthu zofunika za tsiku ndi tsiku, kuti atitsogolere pamene tikufuna kusankha zoyenera kuchita pa nkhani zofunika kwambiri, kuti atithandize pamene tikukumana ndi mavuto komanso tikafuna kuti atikhululukire machimo athu. c
a Mwachitsanzo, Yesu ndi ophunzira ake anapereka mapemphero ena omwe anali ndi mawu osiyana ndi a m’pemphero lachitsanzo.—Luka 23:34; Afilipi 1:9.
b Baibulo la King James, limamaliza Pemphero la Ambuye ndi mawu akuti: ‘Kwa inu kukhale ufumu, ndi mphamvu, ndiponso ulemerero mpaka muyaya. Ame.’ Mawu amenewa amapezekanso m’Mabaibulo ena. Komabe, buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo linanena kuti: ‘Mawu amenewa . . . . sapezeka m’mipukutu yodalirika yakale ya Baibulo.’—The Jerome Biblical Commentary.
c Nthawi zina anthu ena omwe achita tchimo ndipo akufuna kuti Mulungu awakhululukire, amadziimba mlandu kwambiri moti amaona kuti sangakwanitse kupemphera. Koma Yehova amauza anthu omwe amamva mwanjira imeneyi kuti: “Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.” (Yesaya 1:18) Iye ndi wokonzeka kulandira aliyense amene akufunitsitsa kuti akhululukidwe.