Kodi Dzina la Buku la M’Baibulo, Lakuti Chivumbulutso, Limatanthauza Chiyani?
Yankho la m’Baibulo
Mawu achigiriki a buku la m’Baibulo la Chivumbulutso omwe ndi A·po·kaʹly·psis amatanthauza “kuvundukula” kapena “kuulula.” Dzinali limasonyeza tanthauzo labuku la m’Baibulo lakuti Chivumbulutso chifukwa chakuti limavundukula zinthu zimene zakhala zobisika komanso limaulula zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo. Maulosi ake ambiri sanakwaniritsidwebe.
Zimene zili m’buku la Chivumbulutso
Mawu oyamba.—Chivumbulutso 1:1-9.
Mauthenga ochokera kwa Yesu kupita ku mipingo 7.—Chivumbulutso 1:10–3:22.
Masomphenya osonyeza Mulungu atakhala pampando wake wachifumu kumwamba.—Chivumbulutso 4:1-11.
Masomphenya otsatizanatsatizana:
Zidindo 7 zomatira.—Chivumbulutso 5:1–8:6.
Malipenga 7. Malipenga atatu omaliza akubweretsa masoka atatu.—Chivumbulutso 8:7–14:20.
Mbale 7 ndipo m’mbale iliyonse muli chiweruzo cha Mulungu choti chithiridwe padziko lapansi.—Chivumbulutso 15:1–16:21.
Masomphenya osonyeza kuwonongedwa kwa adani a Mulungu.—Chivumbulutso 17:1–20:10.
Masomphenya osonyeza Mulungu akudalitsa kumwamba komanso dziko lapansi.—Chivumbulutso 20:11–22:5.
Mawu omaliza.—Chivumbulutso 22:6-21.
Zinthu zimene zingatithandize kumvetsa buku la Chivumbulutso
Tanthauzo la zinthu zimene zinafotokozedwa m’buku la Chivumbulutso ndi zokhudza zinthu zosangalatsa osati zochititsa mantha kapena zoopsa kwa anthu amene amatumikira Mulungu. Ngakhale kuti anthu ambiri akangomva mawu akuti “Chivumbulutso” amaganiza za tsoka lalikulu, buku la Chivumbulutso limayamba komanso kutha ndi mawu onena kuti anthu amene amawerenga komanso kugwiritsira ntchito uthenga wopezeka m’bukuli adzakhala osangalala.—Chivumbulutso 1:3; 22:7.
Buku la Chivumbulutso limafotokoza zinthu pogwiritsa ntchito zizindikiro kapena zithunzi zimene zingakhale zovuta kuzimvetsa ngati titaziganizira mmene zilili.—Chivumbulutso 1:1.
Mbali zikuluzikulu za m’buku la Chivumbulutso ndiponso zizindikiro, zimafotokozedwa m’mabuku enanso a m’Baibulo:
Yehova—“Mulungu woona wa kumwamba” ndiponso amene analenga zinthu zonse.—Deuteronomo 4:39; Salimo 103:19; Chivumbulutso 4:11; 15:3.
Yesu Khristu—“Mwanawankhosa wa Mulungu.”—Yohane 1:29; Chivumbulutso 5:6; 14:1.
Satana Mdyerekezi—mdani wa Mulungu.—Genesis 3:14, 15; Yohane 8:44; Chivumbulutso 12:9.
Babulo Wamkulu—mofanana ndi Babulo wakale kapena kuti Babele, iye ndi mdani wa Yehova Mulungu ndi anthu ake komanso ndi amene amayambitsa ziphunzitso zabodza zachipembedzo.—Genesis 11:2-9; Yesaya 13:1, 11; Chivumbulutso 17:4-6; 18:4, 20.
“Nyanja”—anthu oipa amene amatsutsa Mulungu.—Yesaya 57:20; Chivumbulutso 13:1; 21:1.
Zinthu zofanana ndi zimene zinkagwiritsidwa ntchito kulambira Mulungu pa chihema chopatulika—kuphatikizapo likasa la pangano, nyanja yoyera ngati galasi (beseni losambiramo), nyali, zofukiza ndi guwa lansembe.—Ekisodo 25:10, 17, 18; 40:24-32; Chivumbulutso 4:5, 6; 5:8; 8:3; 11:19.
Zilombo—kuimira maboma a anthu.—Danieli 7:1-8, 17-26; Chivumbulutso 13:2, 11; 17:3.
Manambala amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa.—Chivumbulutso 1:20; 8:13; 13:18; 21:16.
Masomphenya amenewa amakhudza “tsiku la Ambuye” limene linayamba pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa m’chaka cha 1914 ndipo Yesu anayamba kulamulira monga Mfumu. (Chivumbulutso 1:10) Zimenezi zikusonyeza kuti kukwaniritsidwa kwakukulu kwa masomphenyawa kukuchita masiku ano.
Kuti timvetse bwino zimene zili m’buku la Chivumbulutso tiyenera kugwiritsa ntchito zimene zimatithandiza kumvetsa Baibulo lonse. Zimenezi zikuphatikizaponso nzeru zochokera kwa Mulungu ndiponso anthu amene amalimvetsa bwino.—Machitidwe 8:26-39; Yakobo 1:5.