Kodi Baibulo Lingathandize pa Nkhani ya Mavuto Azachuma Ndiponso Ngongole?
Yankho la m’Baibulo
Inde. Mfundo za m’Baibulo zinayizi zingakuthandizeni pa mavuto azachuma kapena ngongole:
Muzipanga bajeti. “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miyambo 21:5) Musamangogula zinthu chifukwa chakuti zili pa selo. Muzipanga bajeti n’kumaitsatira.
Muzipewa ngongole. “Wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.” (Miyambo 22:7) Ngati panopa muli ndi ngongole ndipo ikukuvutani kubweza, mukambiranenso ndi okubwerekaniwo kabwezedwe kake. Muzitsatira zimene Baibulo limalangiza munthu amene analonjeza mosaganiza bwino kuti adzapereka ngongole ya mnzake iye akadzalephera kubweza. Limati: “Pita ukadzichepetse ndipo ukamuchonderere kwambiri mnzakoyo. Maso ako asapeze tulo, ndipo maso ako owala asagone.” (Miyambo 6:1-5) Muyenera kuchonderera kuti musinthe kabwezedwe. Akakana ulendo woyamba musasiyire pomwepo.
Muzipewa kukonda ndalama. “Munthu wanjiru amayesetsa kuti apeze zinthu zamtengo wapatali, koma sadziwa kuti umphawi udzamugwera.” (Miyambo 28:22) Nsanje ndi dyera zikhoza kuchititsa munthu kusauka komanso kulephera kutumikira Mulungu.
Musamafune zambiri. “Pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.” (1 Timoteyo 6:8) Ndalama sizingakuthandizeni kukhala wosangalala. M’dzikoli, anthu ena amene alibe ndalama zambiri ndi amene amakhala osangalala kwambiri. Zili choncho chifukwa chakuti amakhala pa ubwenzi wabwino ndi anthu am’banja lawo, anzawo ndiponso Mulungu.—Miyambo 15:17; 1 Petulo 5:6, 7.