Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kukwiya?

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kukwiya?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo limanena kuti kukwiya kwambiri n’koopsa ndipo kumabweretsa mavuto kwa munthuyo komanso kwa amene wawakwiyira. (Miyambo 29:22) Ngakhale kuti nthawi zina munthu akhoza kukwiya pa zifukwa zomveka, Baibulo limanena kuti anthu amene amakonda “kupsa mtima” sadzapulumuka. (Agalatiya 5:19-21) Baibulo lili ndi mfundo zimene zingathandize munthu kuti azitha kuugwira mtima akakwiya.

 Kodi nthawi zonse kukwiya n’kolakwika?

 Ayi. Nthawi zina munthu angakwiye pa zifukwa zomveka. Mwachitsanzo, nthawi ina Nehemiya yemwe anali wokhulupirika ‘anakwiya kwambiri’ atamva kuti atumiki anzake akuponderezedwa.​—Nehemiya 5:6.

 Mulungu nayenso amatha kukwiya nthawi zina. Mwachitsanzo, Aisiraeli ataphwanya pangano loti azilambira Mulungu yekha n’kuyamba kulambira milungu ina yonyenga, ‘mkwiyo wa Yehova unawayakira.’ (Oweruza 2:13, 14) Komabe zimenezi sizikusonyeza kuti kukwiya ndi khalidwe lalikulu la Yehova Mulungu. Tikutero chifukwa chakuti amakwiya pa zifukwa zomveka ndipo amatha kubweza mkwiyo wake.—Ekisodo 34:6; Yesaya 48:9.

 Kodi ndi pa nthawi iti pamene kukwiya kumakhala kolakwika?

 Ngati munthu wina atakwiya mopitirira malire komanso popanda zifukwa zomveka, kukwiyako kungakhale kolakwika. Ndipotu zimenezi ndi zomwe anthu ochimwafe timakonda kuchita. Mwachitsanzo:

  •   Kaini “anapsa mtima kwambiri” chifukwa Mulungu sanalandire nsembe yake. Kaini anakwiya kwambiri mpaka kufika popha mbale wake.—Genesis 4:3-8.

  •   Mneneri Yona “anakwiya . . . koopsa” Mulungu atachitira chifundo anthu a ku Nineve. Choncho Mulungu anadzudzula Yona ndipo anamuuza kuti ‘panalibe chifukwa chilichonse choti akwiyire’ ndipo ankafunika kuchitira chifundo anthu a ku Nineve omwe analapa.—Yona 3:10–4:1, 4, 11. a

 Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti “mkwiyo wa munthu [wochimwa] subala chilungamo cha Mulungu.”—Yakobo 1:20.

 Kodi mungatani kuti muziugwira mtima mukakwiya?

  •   Muzidziwa mavuto amene mungakumane nawo ngati mutakwiya mopitirira malire. Anthu ena amaganiza kuti kupsa mtima kwambiri kumasonyeza kuti munthuyo ndi wolimba. Koma zoona zake n’zakuti kukwiya mowonjeza kumasonyeza kuti munthuyo ndi wofooka. Baibulo limanena kuti: “Munthu wosaugwira mtima ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa, n’kuusiya wopanda mpanda.” (Miyambo 25:28; 29:11) Apa zikusonyeza kuti tikamayesetsa kuugwira mtima, timasonyeza kuti ndife ozindikira komanso olimba. (Miyambo 14:29) Baibulo limanenanso kuti: “Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu.”—Miyambo 16:32.

  •   Muzidziwa mavuto amene mungakumane nawo chifukwa chokwiya. Lemba la Salimo 37:8 limati: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.” Ndipo limapitiriza kuti: “Usapse mtima kuti ungachite choipa.” Malembawa akusonyeza kuti tikakwiya timakhala ndi ufulu wosankha. Tikhoza kusankha kungoisiya nkhaniyo tisanachite “choipa.” Paja lemba la Aefeso 4:26 limanena kuti: “Kwiyani, koma musachimwe.”

  •   Ngati n’zotheka muzingochokapo mukaona kuti mkwiyo wanu wayamba kukula. Baibulo limanena kuti: “Chiyambi cha mkangano chili ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo.” Ndipo limapitiriza kuti: “Choncho mkangano usanabuke, chokapo.” (Miyambo 17:14) N’zoona kuti timafunika kuthetsa nkhani mofulumira tikasemphana maganizo ndi anzathu. Komabe pamafunika kuti inuyo ndi mnzanuyo mukhazikitse kaye mtima pansi kuti muthe kukambirana nkhaniyo mwamtendere.

  •    Muzimvetsa kaye nkhani yonse. Lemba la Miyambo 19:11 limanena kuti: “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake.” Choncho ndi bwino kuti tizimvetsa kaye nkhani yonse m’malo mofulumira kukwiya. Ngati titapeza umboni wa mbali zonse za nkhaniyo, sitingakwiye popanda zifukwa zomveka.​—Yakobo 1:19.

  •    Muzipempha Yehova kuti akupatseni mtendere wa mumtima. Pemphero lingakuthandizeni kupeza “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afilipi 4:7) Kupemphera ndi njira inanso yaikulu yomwe Mulungu amatipatsira mzimu wake woyera. Ndipotu mzimuwo ungatithandize kukhala ndi makhalidwe monga mtendere, kuleza mtima komanso kudziletsa.​—Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23.

  • Muzisankha bwino anthu ocheza nawo. Nthawi zambiri anthufe timatengera makhalidwe a anthu amene timacheza nawo. (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) N’chifukwa chake Baibulo limatichenjeza kuti: “Usamagwirizane ndi munthu aliyense wokonda kukwiya, ndipo usamayende ndi munthu waukali.” Baibulo limaperekanso chifukwa chake. Limati: “Kuti usazolowere njira zake ndi kuikira moyo wako msampha.”​—Miyambo 22:24, 25.

a Yona anamveradi malangizowo ndipo Mulungu anamugwiritsa ntchito kuti alembe buku la m’Baibulo lodziwika ndi dzina lake.