Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kusala Kudya?
Yankho la m’Baibulo
Kale, Mulungu ankalola kuti anthu azisala kudya pa zifukwa zomveka. Koma sankasangalala ngati munthu akusala kudya pa zifukwa zolakwika. Masiku ano, Baibulo silikakamiza kapena kuletsa anthu kuti azisala kudya.
Kodi anthu otchulidwa m’Baibulo ankasala kudya pa zifukwa ziti?
Akafuna kuti Mulungu awathandize komanso kuwatsogolera. Pa nthawi imene anthu ankapita ku Yerusalemu, anasala kudya posonyeza kupempha mochokera pansi pamtima kuti Mulungu awathandize. (Ezara 8:21-23) Komanso Paulo ndi Baranaba, ankasala kudya akafuna kusankha akulu mumpingo.—Machitidwe 14:23.
Akafuna kukwaniritsa cholinga cha Mulungu. Yesu atabatizidwa, anasala kudya kwa masiku 40, pokonzekera kuti adzathe kukwaniritsa cholinga cha Mulungu pa utumiki umene anali atatsala pang’ono kuuyamba.—Luka 4:1, 2.
Akafuna kusonyeza kulapa pa zomwe analakwitsa m’mbuyomo. Mulungu anauza mneneri Yoweli kuti auze Aisiraeli omwe anali osakhulupirika kuti: “Bwererani kwa ine ndi mtima wanu wonse. Salani kudya, lirani momvetsa chisoni ndiponso mokuwa.”—Yoweli 2:12-15.
Akafuna kuchita Mwambo Wophimba Machimo. Pa Chilamulo chomwe Mulungu anapereka kwa Aisiraeli, anaikaponso lamulo lakuti chaka chilichonse pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo a azisala kudya. (Levitiko 16:29-31) Pamwambowu zinali zomveka kuti Aisiraeli azisala kudya chifukwa zimenezi zinkawakumbutsa kuti anali ochimwa ndipo ankafunika kuti Mulungu aziwakhululukira.
Kodi anthu amasala kudya pa zifukwa zosayenera ziti?
Pofuna kusangalatsa anthu. Yesu anaphunzitsa kuti nkhani ya kusala kudya ndi yachinsinsi ndipo imakhala ya pakati pa munthu ndi Mulungu.—Mateyu 6:16-18.
Pofuna kudzionetsa ngati olungama. Kusala kudya sikuchititsa munthu kuti akhale wabwino kwambiri komanso kuti Mulungu azimukonda.—Luka 18:9-14.
Pofuna kufafaniza machimo omwe anachita mwadala. (Yesaya 58:3, 4) Mulungu ankasangalala ndi anthu omwe ankasala kudya posonyeza kuti ndi omvera komanso pofuna kusonyeza kulapa mochokera pansi pamtima pa zomwe analakwitsa.
Pongofuna kutsatira mwambo wachipembedzo. (Yesaya 58:5-7) Mulungu sasangalala ndi anthu amene amachita zimenezi. Tikutero chifukwa zili ngati mwana amene amalemekeza bambo ake mwamwambo chabe koma osati mochokera pansi pamtima.
Kodi Akhristu amayenera kusala kudya?
Ayi. Mulungu ankalola Aisiraeli kuti azisala kudya pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. Koma mwambowu unatha Yesu atapereka moyo wake ngati nsembe yophimba machimo a anthu olapa. (Aheberi 9:24-26; 1 Petulo 3:18) Akhristu satsatiranso Chilamulo cha Mose chomwe chinkanena kuti anthu azichita mwambo wophimba machimo. (Aroma 10:4; Akolose 2:13, 14) Choncho Mkhristu angasankhe yekha ngati angafune kusala kudya kapena ayi.—Aroma 14:1-4.
Akhristu amadziwa kuti kusala kudya si nkhani yofunika kwambiri pa kulambira kwawo. Baibulo silinena kuti kusala kudya kumachititsa munthu kukhala wosangalala. Ndipo mosiyana ndi zimenezo, kulambira Mulungu movomerezeka ndi kumene kumachititsa munthu kukhala wosangalala ndipo zimenezi zimasonyeza khalidwe la Mulungu. Paja Baibulo limati iye ndi “Mulungu wachimwemwe.”—1 Timoteyo 1:11; Mlaliki 3:12, 13; Agalatiya 5:22.
Maganizo olakwika omwe anthu ena ali nawo
Maganizo olakwika: Mtumwi Paulo analimbikitsa anthu a pabanja kuti azisala kudya.—1 Akorinto 7:5, Baibulo la King James Version.
Zoona zake: M’Baibulo loyambirira pa 1 Akorinto 7:5, si pamanena za kusala kudya. b Ndipo pali umboni woti anthu ena amene ankakopera Baibulo, anawonjezera mavesi omwe amatchula za kusala kudya monga pa Mateyu 17:21; Maliko 9:29 komanso pa Machitidwe 10:30. Komabe omasulira Mabaibulo ambiri masiku ano amachotsa mavesiwa, chifukwa nkhani zomwe anaikamo zokhudza kusala kudya si zoona.
Maganizo olakwika: Akhristu ayenera kusala kudya pokumbukira masiku 40 omwe Yesu anasalanso kudya ali m’chipululu pambuyo pobatizidwa.
Zoona zake: Yesu sanalamule Akhristu kuti azisala kudya ngati mmene iyeyo anachitira. Komanso m’Baibulo palibe paliponse pamene pamasonyeza kuti Akhristu akale ankafunika kuchita mwambo wosala kudya. c
Maganizo olakwika: Akhristu amafunika kusala kudya pa nthawi yokumbukira imfa ya Yesu.
Zoona zake: Yesu sanalamule ophunzira ake kuti azisala kudya akamakumbukira imfa yake. (Luka 22:14-18) Ngakhale kuti Yesu ananena kuti ophunzira ake akhoza kudzasala kudya iyeyo atamwalira, sikuti anapereka lamulo loti adzasale kudya. Koma ankangosonyeza zimene zingadzachitike. (Mateyu 9:15) Ndipotu Baibulo linalimbikitsa Akhristu kuti azidyeratu kunyumba kwawo asanapite ku mwambo wokumbukira imfa ya Yesu.—1 Akorinto 11:33, 34.
a Pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, Mulungu anauza Aisiraeli kuti: “muzidzisautsa.” (Levitiko 16:29, 31) Mawu amenewa angatanthauzenso kusala kudya. (Yesaya 58:3) Baibulo lina linamasulira mawu akuti “kudzisautsa,” kuti “musadye chilichonse posonyeza kuti mukumva chisoni chifukwa cha zolakwa zanu.”—Contemporary English Version.
b Onani Baibulo lolembedwa ndi Bruce M. Metzger lakuti, A Textual Commentary on the Greek New Testament, Third Edition patsamba 554.
c Buku lina linafotokoza mmene anthu anayambira kusala kudya kwa masiku 40 pokonzekera isitala. Bukuli linati: “M’zaka za m’ma 300 C.E., anthu akamakonzekera phwando la pasika (Isitala) ankasala kudya kwa mlungu umodzi wokha, ndipo nthawi zinanso ankangosala kwa tsiku limodzi kapena awiri basi. Mawu onena za kusala kudya kwa masiku 40 amapezeka m’lamulo la nambala 5 lomwe linatuluka pamsonkhano wa akuluakulu achipembedzo wa ku Nicaea (mu 325 C.E) ngakhale kuti akatswiri ena amatsutsa zoti ankanena za kusala kudya kwa masiku 40 poyembekezera kuchita Isitala.”—New Catholic Encyclopedia, Second Edition, Volume 8, patsamba 468.